Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Abulahamu Anali Munthu Wachikhulupiriro

Abulahamu Anali Munthu Wachikhulupiriro

Abulahamu Anali Munthu Wachikhulupiriro

Tsiku lina Abulahamu anaima panja usiku kunja kuli zii. Iye anayang’ana kumwamba komwe kunkawala nyenyezi zambirimbiri ndipo anakumbukira lonjezo la Mulungu lakuti ana ake adzakhala ochuluka ngati nyenyezizo. (Genesis 15:5) Abulahamu ankati akaona nyenyezi, ankakumbukira zimene Yehova anamulonjeza. Kwa iye, nyenyezizo zinalinso umboni wakuti Mulungu adzakwaniritsadi lonjezo lake. Iye ankakhulupirira kuti popeza Yehova analenga chilengedwe chonsechi, sangalephere kuchititsa kuti iye ndi Sara akhale ndi mwana.

KODI CHIKHULUPIRIRO N’CHIYANI? M’Baibulo mawu akuti “chikhulupiriro” amatanthauza kutsimikizira ndi mtima wonse kuti chinachake chomwe sunachione, chilipo kapena chidzachitika. Munthu amatsimikizira zimenezi malinga ndi umboni umene ali nawo. Amene amakhulupirira Mulungu amaganizira kwambiri za malonjezo a Yehova ndipo amangoona ngati akwaniritsidwa kale.

KODI ABULAHAMU ANASONYEZA BWANJI KUTI ANALI NDI CHIKHULUPIRIRO? Abulahamu anasonyeza kuti ankakhulupirira malonjezo a Mulungu. Chifukwa cha chikhulupiriro, iye anachoka m’dziko lakwawo ndipo anali wotsimikiza kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezo Lake lomusonyeza dziko lina. Komanso chifukwa cha chikhulupiriro, Abulahamu anakhala monga mlendo m’dziko la Kanani koma ali ndi chikhulupiriro chakuti m’tsogolo, ana ake adzapatsidwa dzikolo kukhala lawolawo. Kuwonjezera pamenepo, Abulahamu anamvera pamene anauzidwa kuti apereke Isaki monga nsembe ndipo iye anamvera chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro choti Yehova adzaukitsa Isakiyo ngati patafunika kutero.​—Aheberi 11:8, 9, 17-19.

Abulahamu ankaganizira kwambiri zam’tsogolo, osati zinthu zimene anasiya. N’kutheka kuti Abulahamu ndi Sara ankakhala moyo wosangalala kwambiri ali ku Uri kusiyana ndi umene ankakhala ku Kanani. Komabe iwo ‘sankangokumbukira malo amene anachokera.’ (Aheberi 11:15) M’malomwake, ankaganizira kwambiri zoti Mulungu adzawadalitsa kwambiri komanso kuti adzadalitsa mbadwa zawo.​—Aheberi 11:16.

Kodi panali chifukwa chomveka chomwe chinachititsa kuti Abulahamu akhale ndi chikhulupiriro cholimba chonchi? N’zosachita kufunsa. Yehova anakwaniritsa malonjezo onse amene analonjeza Abulahamu ndipo patapita nthawi, mbadwa zake zinachuluka n’kukhala mtundu wa Isiraeli. Kenako Aisiraeli anayamba kukhala m’dziko la Kanani lomwe Yehova analonjeza Abulahamu.​—Yoswa 11:23.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Tiyenera kukhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake. Ngakhale ena mwa malonjezo amenewa ataoneka ngati osatheka, tiyenera kukumbukira kuti “zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”​—Mateyu 19:26.

Chitsanzo cha Abulahamu chikutiphunzitsanso kuti tisamangoganizira za mmene zinthu zinalili kale koma tiziganizira kwambiri za madalitso amene tidzapeze m’tsogolo. Izi ndi zimene munthu wina dzina lake Jason amachita. Iye ali ndi matenda oopsa amene anachititsa kuti afe ziwalo. Jason anati: “N’zoona kuti nthawi zina ndimaganizira za mmene moyo wanga unalili poyamba.” Iye ananenanso kuti: “Pali zinthu zina zing’onozing’ono zimene ndinkachita kale zomwe ndimalakalaka nditamachita monga, kukumbatira mkazi wanga, Amanda.”

Komabe Jason amakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake, kuphatikizapo lonjezo lakuti posachedwapa dziko lonseli lidzakhala paradaiso ndipo anthu okhulupirika adzakhala ndi moyo wosatha ali ndi thanzi labwino. * (Salimo 37:10, 11, 29; Yesaya 35:5, 6; Chivumbulutso 21:3, 4) Jason anati: “Ndimayesetsa kukumbukira kuti panopa n’zosatheka kukhala ndi moyo wabwino. Koma ndimadziwa kuti posachedwapa mavuto angawa adzatheratu. Sindidzakhalanso ndi nkhawa, sindidzakhumudwa komanso sindidzadziimba mlandu.” Pamenepatu Jason amasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro cholimba ngati cha Abulahamu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Kuti mudziwe zambiri zokhudza paradaiso wa m’tsogolo, onani mutu 3, 7 ndi 8 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.