Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Abulahamu Anali Munthu Wachikondi

Abulahamu Anali Munthu Wachikondi

Abulahamu Anali Munthu Wachikondi

Abulahamu anali ndi chisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya mkazi wake wokondedwa Sara ndipo pa nthawiyi n’kuti iye ali wokalamba. Pamene ankaika mkazi wakeyo m’manda, Abulahamu ankakumbukira zinthu zambiri zabwino zimene anachitira limodzi. Chisoni chitakula kwambiri, iye analira mpaka kugwetsa misozi. (Genesis 23:1, 2) Zimene Abulahamu anachitazi sizinali zochititsa manyazi koma zinasonyeza khalidwe lina labwino limene anali nalo. Khalidwe limeneli ndi chikondi.

KODI CHIKONDI N’CHIYANI? Chikondi chimatanthauza mmene munthu amamvera mumtima mwake chifukwa cha munthu amene amasangalatsidwa naye kwambiri. Munthu wachikondi amachita zinthu zosonyeza chikondi chakecho kwa anthu amene amawakonda ngakhale pamene kuchita zimenezi kungachititse kuti adzimane zinthu zina.

KODI ABULAHAMU ANASONYEZA BWANJI KUTI ANALI WACHIKONDI? Abulahamu anasonyeza kuti ankakonda kwambiri banja lake. N’zachidziwikire kuti iye anali munthu wotanganidwa kwambiri. Komabe ankapeza nthawi yocheza ndi banja lake komanso kulisamalira mwauzimu. Ndipotu, Yehova ankadziwa kuti Abulahamu ankatsogolera bwino banja lake pa zinthu zauzimu. (Genesis 18:19) Kuwonjezera pamenepo, Yehova ananena mawu osonyeza kuti Abulahamu anali munthu wachikondi. Pamene ankalankhula naye, Yehova ananena za Isaki kuti: “Mwana wako amene umamukonda kwambiriyo.”​—Genesis 22:2.

Timadziwanso kuti Abulahamu anali wachikondi tikaganizira zimene anachita mkazi wake atamwalira. Iye analira mokweza mawu. Ngakhale kuti anali wolimba mtima, sanachite manyazi kusonyeza chisoni chake. Pamenepatu Abulahamu anasonyeza kuti, ngakhale kuti anali wolimba mtima, analinso wachifundo.

Abulahamu anasonyeza kuti ankakonda Mulungu. Iye anachita zimenezi pa moyo wake wonse. Kodi iye anasonyeza bwanji kuti ankakonda Mulungu? Tiyenera kukumbukira kuti lemba la 1 Yohane 5:3, limanena kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.” Abulahamu anachita zimene lembali likunena, choncho ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yokonda Mulungu.

Nthawi zonse Yehova akamulamula kuti achite chinachake, Abulahamu ankamvera nthawi yomweyo. (Genesis 12:4; 17:22, 23; 21:12-14; 22:1-3) Iye ankachita zomwe wauzidwazo ngakhale zitakhala zovuta kutsatira. Ankachitanso zimene wauzidwa ngakhale asakudziwa chifukwa chake Yehova wamulamula kuchita zinthuzo. Kwa Abulahamu chofunika kwambiri chinali kuchita zimene Mulungu akufuna. Yehova akam’patsa malamulo, Abulahamu ankaona kuti ndi mwayi wake woti asonyeze kuti amakonda Yehova.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Tingatsanzire Abulahamu mwa kusonyeza chikondi kwa anthu ena, makamaka a m’banja lathu. Sitiyenera kutanganidwa ndi zochita za tsiku ndi tsiku mpaka kulephera kupeza nthawi yoti tichitire zabwino anthu amene timawakonda.

Tiyeneranso kuyesetsa kuti tizikonda kwambiri Yehova. Chikondi chimenechi chingachititse kuti tizichita zinthu zabwino pa moyo wathu. Mwachitsanzo, chingatipangitse kusintha mmene timaonera zinthu, mmene timalankhulira komanso khalidwe lathu n’cholinga choti tikondweretse Mulungu.​—1 Petulo 1:14-16.

N’zoona kuti si nthawi zonse pamene kumvera Yehova kumakhala kophweka. Komabe tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu, yemwe anathandiza Abulahamu komanso amene anamutcha kuti “bwenzi langa,” adzatithandizanso ifeyo. (Yesaya 41:8) Mawu ake, Baibulo, amatilonjeza kuti ‘adzatilimbitsa ndi kutipatsa mphamvu.’ (1 Petulo 5:10) Limenelitu ndi lonjezo lolimbikitsa kwambiri lochokera kwa Yehova, yemwe anali Bwenzi la Abulahamu.

[Bokosi patsamba 11]

Kodi N’zoona Kuti Mwamuna Salira?

Anthu ambiri angayankhe kuti n’zoona kuti mwamuna salira. Koma mwina angadabwe kumva kuti kuwonjezera pa Abulahamu, palinso amuna angapo amphamvu komanso achikhulupiriro amene Baibulo limafotokoza kuti pa nthawi ina analira. Ena mwa anthu amenewa ndi Yosefe, Davide, mtumwi Petulo, akulu a mumpingo wa ku Efeso ndiponso Yesu. (Genesis 50:1; 2 Samueli 18:33; Luka 22:61, 62; Yohane 11:35; Machitidwe 20:36-38) Ndiyetu apa n’zoonekeratu kuti Baibulo silimanena kuti mwamuna salira.