Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Baibulo Limalosera Zam’tsogolo?

Kodi Baibulo Limalosera Zam’tsogolo?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi maulosi a m’Baibulo amatchula zinthu ndendende mmene zidzachitikire?

Mulungu Wamphamvuyonse yekha ndi amene angathe kudziwiratu zinthu zam’tsogolo mwatsatanetsatane. (Amosi 3:7) Mwachitsanzo, iye analosera za kubwera kwa Mesiya kapena kuti Khristu ndipo anachita zimenezi kale kwambiri. Mesiya ameneyu anali woti adzakhala mbadwa ya Abulahamu yemwe anali munthu wokhulupirika. Iye analinso woti adzakhala mfumu imene idzathandize kuti anthu omvera adzapeze moyo wangwiro komanso wopanda matenda. (Genesis 22:18; Yesaya 53:4, 5) Kuwonjezera pamenepa, Wolonjezedwa ameneyu anali woti adzachokera ku Betelehemu.​—Werengani Mika 5:2.

Yesu ndi amene anali Mesiya wolonjezedwa ameneyu. Zaka zoposa 700 Yesu asanabadwe, Baibulo linalosera kuti Mesiya adzabadwa kuchokera kwa namwali ndipo adzanyozedwa. Linaloseranso kuti adzapereka moyo wake chifukwa cha machimo a anthu ambiri komanso adzaikidwa m’manda limodzi ndi anthu olemera. (Yesaya 7:14; 53:3, 9, 12) Komanso kudakali zaka zoposa 500, Baibulo linaneneratu kuti iye adzalowa mu Yerusalemu atakwera bulu komanso kuti adzaperekedwa ndi ndalama 30 zasiliva. Maulosi onsewa anakwaniritsidwa ndendende.​—Werengani Zekariya 9:9; 11:12.

2. Kodi Mulungu amaneneratu nthawi imene zinthu zidzachitike?

Kudakali zaka zoposa 500, Baibulo linalosera chaka chenicheni chimene Mesiya adzaonekere. Pa nthawi imeneyo, nthawi ankaiwerengetsera pogwiritsa ntchito milungu ndipo “mlungu” uliwonse unkakhala wautali zaka 7. Ulosi wonena za Mesiya unanena kuti iye adzaonekera patadutsa milungu 7 komanso milungu 62, yomwe tikaphatikiza ndi milungu 69 ya zaka. Choncho milungu 69 imeneyi, yomwe uliwonse ndi wautali zaka 7, ndi nthawi yotalika zaka 483. Kodi zaka 483 zimenezi zinayambira pati? Malinga ndi zimene Baibulo limanena, zaka zimenezi zinayamba pamene Nehemiya, mtumiki wa Mulungu anapita kukamanganso mzinda wa Yerusalemu. Mbiri yakale ya ku Perisiya imasonyeza kuti chimenechi chinali chaka cha 455 B.C.E. (Nehemiya 2:1-5) Patatha zaka ndendende 483, m’chaka cha 29 C.E., Yesu anabatizidwa n’kukhala Mesiya.​—Werengani Danieli 9:25.

3. Kodi maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa masiku ano?

Yesu analosera zinthu zikuluzikulu zimene zikuchitika masiku ano. Mu ulosi wake, iye anatchula za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu womwe udzabweretse madalitso padziko lonse kwa anthu okonda Mulungu. Ufumu umenewu udzathetsa zoipa zonse zimene zili m’dzikoli.​—Werengani Mateyu 24:14, 21, 22.

Maulosi a m’Baibulo anafotokoza mwatsatanetsatane zochitika za kumapeto a nthawi yathu ino. Baibulo linaneneratu kuti pa nthawi inoyo, imene anthu ambiri akuganiza kuti zinthu zikanakhala zikuyenda bwino, anthu adzawononga dzikoli. Linanenanso kuti zinthu monga nkhondo, kusowa kwa chakudya, zivomezi komanso miliri zidzawonjezeka. (Luka 21:11; Chivumbulutso 11:18) Baibulo linaneneratunso kuti anthu ambiri azidzakhala ndi makhalidwe oipa ndiponso pa nthawi yovuta imeneyi, otsatira a Yesu azidzalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa anthu a mitundu yonse.​—Werengani Mateyu 24:3, 7, 8; 2 Timoteyo 3:1-5.

4. Kodi anthu omvera ali ndi tsogolo lotani?

Mulungu Wamphamvuyonse wakonza zoti anthu omvera adzapeze madalitso ambiri. Yesu Khristu, yemwe ndi Mesiya, adzalamulira dziko lapansi ali kumwamba. Iye adzalamulira limodzi ndi anthu amene Mulungu anawasankha. Ufumu umenewu udzalamulira kwa zaka 1,000. Anthu amene anamwalira adzaukitsidwa ndipo adzapatsidwa mwayi wokhala ndi moyo kosatha. Komanso Ufumu umenewu udzachiritsa anthu onse odwala. Ndiyeno sikudzakhalanso matenda kapena imfa.​—Werengani Chivumbulutso 5:10; 20:6, 12; 21:4, 5.

Kuti mudziwe zambiri werengani tsamba 23 mpaka 25 komanso tsamba 197 mpaka 201 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?