Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena
Kodi N’chifukwa Chiyani Mulungu Ali Ndi Gulu Lake Limene Akulitsogolera?
Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.
1. N’chifukwa chiyani Mulungu anakonza zoti Aisiraeli akhale gulu la anthu ake?
Mulungu anakonza zoti mbadwa za Abulahamu zikhale gulu loti lizimulambira ndipo anazipatsa malamulo. Mulungu anatchula mtundu umenewu kuti Isiraeli ndipo anaupatsa udindo woteteza kulambira koona komanso Malemba Oyera omwe ndi Mawu ake. (Salimo 147:19, 20) Dongosolo limeneli lachititsa kuti anthu amitundu yonse apindule.—Werengani Genesis 22:18.
Mulungu anasankha Aisiraeli kuti akhale mboni zake. Aisiraeli akamamvera malamulo a Mulungu, zinthu zinkawayendera bwino. (Deuteronomo 4:6) Kuphunzira mbiri ya Aisiraeli kungatithandize kudziwa zambiri zokhudza Mulungu woona.—Werengani Yesaya 43:10, 12.
2. N’chifukwa chiyani pali gulu la Akhristu oona?
Patapita nthawi, mtundu wa Isiraeli unasiya kumvera Mulungu, choncho Yehova anakhazikitsa mpingo wachikhristu. (Mateyu 21:43; 23:37, 38) Poyamba Aisiraeli anali mboni za Mulungu. Koma masiku ano Akhristu oona ndi amene ali mboni za Yehova.—Werengani Machitidwe 15:14, 17.
Yesu anakonza zoti pakhale gulu la ophunzira ake n’cholinga chakuti lizilalikira za Yehova komanso liziphunzitsa anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mateyu 10:7, 11; 24:14; 28:19, 20) Panopa ntchito imeneyi yafika pachimake. Kwa nthawi yoyamba Yehova wasonkhanitsa anthu mamiliyoni ambiri ochokera m’mitundu yonse kuti azimulambira. (Chivumbulutso 7:9, 10) Yesu analangizanso Akhristu oona kuti azichita zinthu monga gulu n’cholinga choti azilimbikitsana komanso kuthandizana. Zimene iwo amaphunzira pa misonkhano yawo padziko lonse, zimakhala zofanana ndipo zimachokera m’Baibulo.—Werengani Aheberi 10:24, 25.
3. Kodi Mboni za Yehova za masiku ano zinayamba bwanji?
Mboni za Yehova za masiku ano zinayamba cha m’ma 1870. Kagulu ka anthu ophunzira Baibulo kanayamba kutulukiranso mfundo za choonadi cha m’Baibulo zimene zinali zitasokonezedwa kwa nthawi yaitali. Iwo anadziwa kuti Yesu anakhazikitsa mpingo wachikhristu kuti uzilalikira. Choncho anayamba ntchito yolalikira Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi. Mu 1931 anayamba kudziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova.—Werengani Machitidwe 1:8; 2:1, 4; 5:42.
4. Kodi gulu la masiku ano la Mboni za Yehova limayendetsedwa bwanji?
M’nthawi ya atumwi, mipingo yachikhristu ya m’madera ambiri inkalandira malangizo kuchokera ku bungwe lolamulira lomwe linkagonjera Yesu monga Mutu wa mpingo. (Machitidwe 16:4, 5) Masiku anonso Mboni za Yehova zimadziwa kuti Yesu ndiye Mtsogoleri wawo. (Mateyu 23:9, 10) Iwo amatsogoleredwanso ndi Bungwe Lolamulira lokhala ndi akulu odziwa bwino ntchito yawo amene amalimbikitsa komanso kupereka malangizo a m’Malemba kwa anthu a m’mipingo yoposa 100,000. Mu mpingo uliwonse mumakhala amuna oyenerera amene amatumikira monga akulu, kapena kuti oyang’anira. Anthu amenewa amasamalira mwachikondi nkhosa za Mulungu.—Werengani 1 Petulo 5:2, 3.
Mboni za Yehova ndi gulu limene limalalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa anthu. Kuti athe kuthandiza anthu kulikonse, iwo amamasulira, kusindikiza komanso kufalitsa mabuku othandiza kuphunzira Baibulo m’zinenero zoposa 500. Mofanana ndi zimene atumwi ankachita, a Mboni za Yehova amalalikira kunyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20) Komanso iwo amapempha anthu okonda choonadi kuti aziphunzira nawo Baibulo. Anthu a Yehova amayesetsa kukondweretsa Mulungu komanso kuthandiza ena ndipo zimenezi zimathandiza kuti azikhala osangalala.—Werengani Salimo 33:12; Machitidwe 20:35.
Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 19 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.