Zimene Anthu Ena Amanena Zokhudza Aramagedo
Zimene Anthu Ena Amanena Zokhudza Aramagedo
“Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa [Aramagedo].”—CHIVUMBULUTSO 16:16, onani mawu a m’munsi.
KODI mukamva mawu akuti “Aramagedo” mumaganiza za chiyani? N’kutheka kuti mumaganiza za tsoka loopsa kwambiri. Ngakhale kuti mawu amenewa amapezeka kamodzi kokha m’Baibulo lonse, anthu ofalitsa nkhani komanso atsogoleri a zipembedzo amawatchula kawirikawiri.
Kodi zimene anthu ambiri amanena zokhudza Aramagedo n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa? Kudziwa yankho la funso limeneli n’kofunika kwambiri chifukwa kungakuthandizeni kuti musamakhale ndi mantha komanso kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo. Kungakuthandizeninso kukhala ndi maganizo oyenera okhudza Mulungu.
Taonani mafunso atatu otsatirawa okhudza Aramagedo ndipo yerekezerani zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi ndi zimene anthu ambiri amaganiza.
1. KODI ARAMAGEDO NDI KUWONONGEKA KWA ZINTHU KOYAMBITSIDWA NDI ANTHU?
Kawirikawiri atolankhani komanso anthu ochita kafukufuku amagwiritsa ntchito mawu akuti “Aramagedo” pofotokoza za kuwonongeka kwa zinthu koyambitsidwa ndi anthu. Mwachitsanzo, anthu amanena kuti nkhondo yoyamba ndi yachiwiri ya padziko lonse inali Aramagedo. Nkhondozi zitatha, anthu ankada nkhawa kuti mwina mayiko a United States ndi Soviet Union akhoza kuyamba kuponyerana mabomba a nyukiliya. Ofalitsa nkhani ena anatchula nkhondo imeneyi kuti idzakhala “Aramagedo ya nyukiliya.” Masiku ano akatswiri ofufuza za chilengedwe akamaona mmene nyengo ikusinthira chifukwa cha kuwonongeka kwa chilengedwe, akumachenjeza anthu kuti kudzabwera “Aramagedo ya nyengo.”
Zimene anthu amenewa amaganiza: Tsogolo la dzikoli komanso la zamoyo zimene zili padzikoli, likudalira zimene anthu akuchita panopa. Choncho maboma akapanda kuchitapo kanthu, dziko lapansili likhoza kuwonongekeratu.
Zimene Baibulo limaphunzitsa: Mulungu sangalole kuti anthu aliwonongeretu dziko lapansili. Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova * sanalenge dzikoli “popanda cholinga.” Koma analiumba “kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Choncho Mulungu sadzalola kuti anthu awonongeretu dzikoli. M’malomwake iye ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’—Chivumbulutso 11:18.
2. KODI ARAMAGEDO IDZAKHALA TSOKA LACHILENGEDWE?
Nthawi zina atolankhani amagwiritsa ntchito mawu akuti “Aramagedo” ponena za masoka akuluakulu achilengedwe. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2010 lipoti lina linanena kuti zimene zinachitika ku Haiti, inali “‘Aramagedo’ ya ku Haiti.” Lipoti limeneli linkanena za zinthu zimene zinawonongeka komanso anthu amene anafa chifukwa cha chivomezi chachikulu chimene chinachitika m’dzikolo. Atolankhani ndi anthu okonza mafilimu amagwiritsa ntchito mawu akuti “Aramagedo” ponena za zinthu zoopsa ngati zimenezi. Iwo amagwiritsanso ntchito mawu amenewa ponena za zimene akuganiza kuti zidzachitika m’tsogolo. Mwachitsanzo, iwo amagwiritsa ntchito mawuwa ponena za ngozi imene amati ingathe kuchitika ngati nyenyezi ina itawombana ndi dziko lapansili.
Zimene anthu amenewa amaganiza: Aramagedo ndi tsoka limene lidzagwere anthu onse, ndi osalakwa omwe, ndipo pa nthawiyo aliyense adzafa. Palibe chimene munthu angapange kuti adzapulumuke tsoka limeneli.
Zimene Baibulo limaphunzitsa: Aramagedo siidzapha anthu mwachisawawa, ndi osalakwa omwe. M’malomwake, pa Aramagedo anthu oipa okha ndi amene adzawonongedwe. Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa “woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.”—Salimo 37:10.
3. KODI PA ARAMAGEDO MULUNGU ADZAWONONGA DZIKO LAPANSILI?
Anthu a m’zipembedzo zambiri amakhulupirira kuti padzakhala nkhondo yomaliza pakati pa anthu abwino ndi oipa ndipo zotsatira zake zidzakhala kutha kwa dzikoli. Komanso kafukufuku amene bungwe lina linachita ku United States anasonyeza kuti anthu 40 pa anthu 100 alionse amakhulupirira kuti dzikoli lidzatha pa “nkhondo ya Aramagedo.”—Princeton Survey Research Associates.
Zimene anthu amenewa amaganiza: Mulungu
sanalenge anthu kuti adzakhale padziko lapansili mpaka kalekale. Komanso sanalenge dzikoli kuti lidzakhaleko mpaka muyaya. Mulungu analenga anthu n’cholinga chakuti pa nthawi ina onse adzafe.Zimene Baibulo limaphunzitsa: Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu ‘wakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.’ (Salimo 104:5) Komanso ponena za anthu, Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
Monga taonera, zimene anthu ambiri amakhulupirira zokhudza Aramagedo sizigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndiye kodi zoona zenizeni ndi ziti?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.