Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

“Anapitiriza Kumamatira Yehova”

“Anapitiriza Kumamatira Yehova”

KODI umadziwa zimene kumamatira munthu kumatanthauza? * Kumatanthauza kuona munthuyo kuti ndi wofunika komanso kumukonda kwambiri ndi kumulemekeza. Tiye tikambirane za munthu wina amene Baibulo limati “anapitiriza kumamatira Yehova,” Mulungu woona. Dzina la munthu ameneyu anali Hezekiya. Tikambirana zimene tikuphunzira kwa iye.

Hezekiya ali mwana, anakumana ndi zinthu zambiri zosasangalatsa. Bambo ake Ahazi, omwe anali mfumu ya Yuda, anasiya kutumikira Yehova. Iwo anachititsa kuti anthu awo ayambe kulambira milungu yonyenga. Ahazi anafika mpaka popha mmodzi kapena angapo mwa abale ake a Hezekiya ndipo anawapereka nsembe kwa mulungu wina amene iye ankalambira. Pamenepatu ndiye kuti Ahazi anapha mng’ono wake wa Hezekiya.

Ngakhale kuti Ahazi ankachita zinthu zoipa chonchi, Hezekiya anapitiriza kumvera Yehova. Kodi ukuganiza kuti kuchita zimenezi kunali kosavuta?​— Kuyenera kuti kunali kovuta komabe Hezekiya sanasiye kumvera Yehova. Tiye tione zimene zinamuthandiza kuti amamatire Yehova komanso mmene ifeyo tingatsatirire chitsanzo chake.

Hezekiya anaphunzira za anthu ena amenenso anamamatira Yehova. Mmodzi mwa anthu oterewa anali Davide. Ngakhale kuti Davide anali atamwalira zaka zambirimbiri m’mbuyomo, Hezekiya anaphunzira za iye m’Malemba. Davide analemba kuti: “Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya, Yehova adzanditenga.”

Kodi waona zimene zinathandiza Davide kumvera Yehova?​— Ndi chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro. Iye ankakhulupirira kuti akakhala womvera, Yehova adzamuthandiza. Davide sankakayikira mpang’ono pomwe kuti Yehova adzamuthandiza. Kuganizira za Davide kunathandiza Hezekiya kumamatira Yehova komanso kumumvera. Iwenso ukamamatira Yehova ndiponso kumumvera, ungakhale ndi chikhulupiriro choti adzakuthandiza.

Nanga bwanji ngati bambo kapena mayi ako salambira Yehova?​—Mulungu amanena kuti ana ayenera kumvera makolo awo. Choncho iwenso uyenera kumvera makolo ako. Komabe makolo ako akakuuza kuti uchite zinthu zimene Mulungu amaletsa, uyenera kuwafotokozera chifukwa chake sungachite zimenezo. Komanso munthu aliyense akakuuza kuti uname, ube kapena uchite zilizonse zimene Mulungu amati n’zoipa, suyenera kumvera. Uyenera kumvera Mulungu.

Palinso zitsanzo zina zabwino zimene tingatsatire. Kuwonjezera pa chitsanzo cha Davide, Hezekiya anatengeranso chitsanzo cha agogo ake dzina lawo Yotamu. Ngakhale kuti Yotamu anamwalira Hezekiya asanabadwe, Hezekiyayo anaphunzira za Yotamu. Nafenso tingathe kuphunzira za Yotamu m’Baibulo. Kodi ungatchule zitsanzo za anthu ena amene tingatsanzire?​

N’zoona kuti m’Baibulo ungaphunzirenso za zinthu zolakwika zimene Hezekiya, Davide, Yotamu komanso anthu ena opanda ungwiro anachita. Komabe anthu amenewa ankakonda Yehova, anavomereza zolakwa zawo komanso ankayesetsa kuchita zabwino. Usaiwale kuti Yesu yekha, Mwana wa Mulungu, ndi amene anali wangwiro kapena kuti sankalakwitsa kanthu. Tiyenera kuphunzira za iye komanso kutsatira chitsanzo chake.

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera mwana nkhaniyi, mukapeza mzera muime kaye ndi kumulimbikitsa kuti anenepo maganizo ake.