Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Mumamudziwa Kuti Ndi Ndani?

Kodi Yesu Mumamudziwa Kuti Ndi Ndani?

Kodi Yesu Mumamudziwa Kuti Ndi Ndani?

Kodi mukamva za Yesu mumamuganizira ali kamwana kakhanda, munthu amene akuphedwa kapena Mfumu yaulemelero?

Baibulo limanena kuti panopa Yesu ndi mfumu yamphamvu. Koma kodi zimenezi zikukukhudzani bwanji?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti Yesu anawafera. Komabe, kodi imfa ya munthu mmodzi, yomwenso inachitika zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, ingatikhudze bwanji masiku ano?

Tikukuitanani kuti mudzamve mayankho a m’Malemba a mafunso amenewa. Mfundo zimenezi zidzafotokozedwa pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu umene Mboni za Yehova zidzakhale nawo. Chaka chino mwambo umenewu udzachitika Lachinayi, pa April 5, dzuwa litalowa.

Mukafuna kudziwa nthawi komanso malo amene kudzachitikire mwambowu, funsani Mboni za Yehova za m’dera lanu.

Mlungu wotsatira, mwambo wokumbukira imfa ya Yesu utachitika, Mboni za Yehova zidzakambanso nkhani yochititsa chidwi yochokera m’Baibulo. Nkhaniyi idzakhala ya mutu wakuti: “Kodi Mapeto Ayandikiradi?” Nkhani imeneyi idzakambidwa padziko lonse lapansi ndi cholinga chothandiza anthu onse amene amakonda choonadi komanso omwe akufuna kudziwa zambiri za Yesu. Inunso mukuitanidwa kuti mudzamvetsere nkhaniyi.