Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera ku Russia

Kufufuza Chuma Chobisika M’mapiri Agolide a ku Altay

Kufufuza Chuma Chobisika M’mapiri Agolide a ku Altay

TSIKU lina kunja kunacha bwino kwambiri. Unali mwezi wa May ndipo tinali m’dera lokongola kwambiri lotchedwa Altay Republic lomwe lili kum’mwera chakumadzulo kwa dziko la Siberia. Tikasuzumira pawindo tinkaona nkhalango yowirira ndipo chakutsogolo kwake kuli mapiri omwe ankaoneka a buluu komanso okutidwa ndi chifunga pamwamba pake. Kudera limenelo kumakhala Amwenye amtundu wotchedwa Altaic omwe amalankhula chinenero chawochawo ndipo derali ndi lamiyala komanso lili kwalokhalokha. Iwo amakhala m’mapiri a Altai ndipo dzina limeneli linachokera ku mawu a chilankhulo cha Chitheki ndi Chimongolia omwe amatanthauza “chinthu chagolide.”

Pangotha zaka zochepa kuchokera pamene ine ndi mkazi wanga tinaphunzira chinenero chamanja cha ku Russia komanso kuyamba kuchezera timagulu ndiponso mipingo ya Mboni za Yehova yolankhula chinenerochi. M’dziko la Russia muli anthu amitundu yosiyanasiyana yokwana 100 komanso a zikhalidwe zosiyanasiyana zokwana 70 koma onse amatha kulankhula Chirasha, chomwe ndi chinenero chachikulu m’dzikoli. Komabe anthu amene ali ndi vuto losamva amalankhula chinenero chawochawo, chomwe ndi chinenero chamanja cha ku Russia. Anthu amenewa ndi ogwirizana kwambiri ndipo ambiri mwa amene timakumana nawo amakonda kutifotokozera zimene akumana nazo pa moyo wawo komanso kutichereza. Umu ndi mmenenso zilili ndi anthu osamva amene amakhala m’dera la Altay.

Tili mumzinda wa Gorno-Altaysk tinamva kuti pali anthu angapo osamva amene amakhala m’mudzi winawake womwe uli pa mtunda wa makilomita 250 kuchokera mumzindawu. Tinkadziwa kuti m’mudzi umenewo muli a Mboni angapo komabe palibe amene ankadziwa chinenero chamanja. Tinayamba kuganizira za anthu amene ali ndi vuto losamvawo, ndipo tinaganiza zopita kuti tikafufuze kumene amakhala. Yury ndi mkazi wake Tatyana, omwenso ndi osamva, ataona chidwi chimene tinali nacho pofunitsitsa kuwafikira anthuwa, anavomera kuti tipitire limodzi. Tinatenga galimoto yaing’ono ya bokosibode. Tinatenganso ma DVD a chinenero chamanja, wailesi ya DVD, fulasiki yaikulu komanso zakudya zosiyanasiyana monga buledi ndi masoseji. Komanso tinatenga samusa wa kabichi ndi mbatata, chakudya chimene anthu a ku Russia amachikonda kwambiri. Kenako tinadzipopera mankhwala enaake othandiza kuti tizilombo toyambitsa matenda otupa ubongo tisatilume, popeza matendawa ndi ofala kuderali. Tinapoperanso mankhwalawa pazovala ndiponso nsapato zathu.

Msewu umene tinadutsa ndi wokhotakhota wa m’mapiri ndipo tinkaona malo okongola kwambiri. M’derali mumamveka kafungo kosangalatsa ka maluwa enaake. Tinachita chidwi kuona gulu la mphalapala za ku Siberia zomwe zinkadya msipu mwakachetechete. Anthu otchedwa Altaic amakhala m’nyumba zoyandikana, zomangidwa ndi matabwa koma zofoleledwa bwino ndi malata. Pafupi ndi nyumba zambiri pamakhalanso kanyumba kamene amakatchula kuti ayyl ndipo nthawi zambiri tinyumba timeneti timakhala tamakona 6 komanso tadenga losongoka. Tina timaoneka ngati tenti yokutidwa ndi makungwa a mtengo. Kuyambira mwezi wa May mpaka September, mabanja ambiri a anthu amenewa amakonda kukhala m’tinyumba timeneti ndipo amachokamo nthawi yozizira ikayamba.

Titafika kuderali, tinalandiridwa ndi a Mboni za Yehova a m’mudzimu ndipo anatilondolera kunyumba kwa banja lina la anthu osamva. Banjali linasangalala kwambiri litationa ndipo linali ndi chidwi chofuna kudziwa kumene tachokera komanso zomwe tabwerera. Mwamwayi, banjali linali ndi kompyuta ndipo titangotulutsa DVD, anaumirira kuti aionere nthawi yomweyo. Titangoika DVD ija, panangokhala zii ngati palibe anthu. Iwo ankangoyang’anitsitsa pakompyutapo ndipo nthawi zina ankayerekezera zomwe akuona komanso ankagwedezera mutu posonyeza kuti akugwirizana ndi zimene akuonazo. Tinachita kuwanyengerera kuti avomereze kuti tiimitse kaye DVD ija kuti tiiyambire koyamba komwe kunali zithunzi zokongola za dziko lapansi la paradaiso. Anavomerezadi kuti tiiyambirenso ndipo titaonera kwakanthawi tinaiimitsanso kaye n’kuyamba kuwafotokozera zimene Mulungu adzachitire anthu komanso anthu amene adzakhale kwamuyaya m’paradaiso. Tinasangalala kwambiri ndi chidwi chimene anthuwa anasonyeza ndipo pamapeto pa kucheza kwathu anatiuza kuti palinso banja lina la anthu osamva limene limakhala m’mudzi wina chapatali.

Tinayamba ulendo wopita kumudzi umenewu, womwe ndi waung’onopo poyerekeza ndi umene tinaliwu. Msewu womwe tinadzera umadutsa mkati mwa phiri linalake ndipo ndi wokhotakhota. Titafika tinapeza bambo, mayi, agogo aakazi komanso mwana wamwamuna, onse osamva. Anthuwa anali osangalala kwambiri chifukwa sanayembekezere kuti alandira alendo pa tsikuli. Anatilowetsa m’kanyumba kawo kotchedwa ayyl ndipo munali kafungo kabwino ka matabwa komanso mkaka. Pansonga penipeni pa denga la nyumbayi panali chibowo chomwe chinkathandiza kuti m’nyumbamo muziwala bwino. Pakona ina ya nyumbayi panali uvuni ya njerwa yopaka laimu komanso khoma lonse linali lokutidwa ndi nsalu zofiira zokongola. Banjali linatiphikira tiyi ndi madonasi ndipo ichi ndi chakudya chimene anthu a m’derali amakonda. Ndiyeno tinawafunsa ngati anaganizapo ngati zili zotheka kukhala bwenzi la Mulungu. Anayamba kuganizira funso limeneli. Kenako agogo aja anatiuza kuti nthawi ina ali mwana, anatenga chakudya n’kukachipereka nsembe kwa milungu paphiri linalake. Ndiyeno akugwedeza mapewa komanso akumwetulira anatiuza kuti: “Koma sindidziwa kuti zimenezi zinkatanthauza chiyani. Chinali chikhalidwe chathu basi.”

Tinawaonetsa DVD yonena za nkhaniyi ndipo anasangalala kwambiri. Iwo anafunitsitsa kuti tidzapitirize kucheza kwathu. Koma kodi zimenezi zikanatheka bwanji? Ngakhale kuti kulemberana mauthenga pa foni za m’manja ndi njira yothandiza kulankhulana ndi anthu osamva, kuderali kulibe netiweki. Choncho tinapangana kuti tizilemberana makalata.

Tinatsanzikana mosangalala ndipo tinayamba ulendo wathu wobwerera ku Gorno-Altaysk. Pa nthawiyi, n’kuti dzuwa likulowa ndipo tinali titatopa komabe tili osangalala kwambiri. Patapita nthawi, tinafunsa a Mboni za Yehova ena akumeneko za banjali. Iwo anatiuza kuti mlungu uliwonse bambo aja amapita ku tauni ya m’derali kukaphunzira Baibulo komanso kukasonkhana ndi a Mboni. Iwo amathandizidwa ndi mayi wina wa Mboni yemwe amadziwa chinenero chamanja. Tinasangalala kwambiri kuona kuti khama lathu linali ndi zotsatira zabwino.

Ntchito yathu yofufuza anthu osamva tingaiyerekezere ndi kufufuza chuma chobisika m’mapiri. Zimakhala zosangalatsa kwambiri tikachita mwayi n’kupeza munthu wofuna kuphunzira za Mulungu, yemwe tingamuyerekezere ndi chuma chamtengo wapatali. Ifeyo timaona kuti mapiri a Altay ndi agolide chifukwa nthawi zonse amatikumbutsa za anthu a mitima yabwino amene tinakumana nawo m’dera lamapiri limeneli.