Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Muzikondana”

“Muzikondana”

“Muzikondana”

“Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”​—YOHANE 13:34, 35.

Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? Khristu anauza otsatira ake kuti azikondana ngati mmene iyeyo anawakondera. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda anthu? Iye ankakonda kwambiri anthu ngakhale kuti pa nthawiyo khalidwe losankhana mitundu komanso lonyoza akazi linali lofala. (Yohane 4:7-10) Chifukwa cha chikondi, Yesu ankagwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zake kuti athandize ena. Iye ankagwiritsanso ntchito nthawi yake yopuma kuthandiza anthu. (Maliko 6:30-34) Pamapeto pake Khristu anasonyeza chikondi mwa njira yapadera kwambiri. Iye anati: “Ine ndine m’busa wabwino. M’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.”​—Yohane 10:11.

Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: M’nthawi ya atumwi, Akhristu ankatchulana kuti “m’bale” kapena “mlongo.” (Filimoni 1, 2) Anthu amitundu yonse anali olandiridwa mu mpingo wachikhristu poti onse ankakhulupirira kuti “palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki, popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi.” (Aroma 10:11, 12) Pentekosite wa mu 33 C.E. atatha, ophunzira a Yesu a ku Yerusalemu “anali kugulitsa malo awo ndi zina zimene anali nazo, n’kugawa kwa onse zimene apeza, aliyense malinga ndi kusowa kwake.” Kodi iwo anachita zimenezi chifukwa chiyani? Ankafuna kuti anthu amene angobatizidwa kumene akhalebe ku Yerusalemuko kuti apitirize “kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” (Machitidwe 2:41-45) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti iwo akhale ndi mtima wogawana zinthu ndi ena? Pasanathe zaka 200 kuchokera pamene atumwi anafa, munthu wina dzina lake Tertullian analemba zimene anthu ena ananena zokhudza Akhristu kuti: “Iwo amakondana kwambiri . . . ndipo ndi okonzeka ngakhale kuferana.”

Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Buku lina lolembedwa mu 1837, linanena kuti kwa zaka zambiri, anthu amene amanena kuti ndi Akhristu “akhala akuchitirana nkhanza zoopsa kuposa zimene achitiridwa ndi anthu osapemphera.” (The History of the Decline and Fall of the Roman Empire) Komanso zotsatira za kafukufuku wina amene anachitika posachedwapa ku United Stated zinasonyeza kuti anthu ambiri amene amapembedza, makamaka amene amati ndi Akhristu, amakhala atsankho. Nthawi zambiri anthu a tchalitchi chimodzi amasalana chifukwa chakuti akuchokera m’mayiko osiyana ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamathandizane pakakhala mavuto.

Mu 2004, mphepo yamkuntho inawomba kanayi motsatizana m’miyezi iwiri yokha mumzinda wa Florida. Izi zitachitika, tcheyamani wa komiti ya mumzindawu yoona zogwa mwadzidzidzi (Florida’s Emergency Operations Committee), ankafuna kuona ngati zinthu zomwe komitiyi inapereka zinkagwiritsidwa ntchito moyenera. Pambuyo pake, tcheyamaniyu ananena kuti panalibe gulu limene linkachita zinthu mwadongosolo ngati la Mboni za Yehova ndipo ananena kuti anali wokonzeka kupereka thandizo lililonse limene a Mboniwo angafunikire. Komanso izi zisanachitike, mu 1997, a Mboni za Yehova a m’mayiko ena anapita kudziko la Democratic Republic of Congo kukathandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena amene ankafunikira mankhwala, chakudya komanso zovala. Zinthu zimene anakaperekazo zinali zimene a Mboni za Yehova a ku Ulaya anapereka ndipo zinali zandalama zokwana madola 1 miliyoni a ku United States.