Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Muzisunga Mawu Anga Nthawi Zonse’

‘Muzisunga Mawu Anga Nthawi Zonse’

‘Muzisunga Mawu Anga Nthawi Zonse’

“Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—YOHANE 8:31, 32.

Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? “Mawu” a Yesu amene lembali likunena amatanthauza zimene iye anaphunzitsa, zomwe ndi zochokera kwa Mulungu. Yesu anati: “Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.” (Yohane 12:49) Pamene Yesu ankapemphera kwa Atate ake akumwamba, Yehova Mulungu, iye anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” Choncho, nthawi zambiri akamaphunzitsa, ankatchula zimene Mawu a Mulungu amanena potsimikizira kuti zimene akuphunzitsazo n’zoona. (Yohane 17:17; Mateyu 4:4, 7, 10) Chifukwa cha zimenezi, Akhristu oona ‘amasunga mawu ake nthawi zonse,’ kutanthauza kuti iwo amaona kuti Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi “choonadi.” Zinthu zonse zimene amakhulupirira kapena kuchita zimakhala zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: Nayenso mtumwi Paulo ankalemekeza Mawu a Mulungu. Iye analemba kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Amuna amene ankasankhidwa kuti aziphunzitsa Akhristu anzawo ankayenera ‘kugwira mwamphamvu mawu okhulupirika a Mulungu.’ (Tito 1:7, 9) Akhristu oyambirira analangizidwa kuti azipewa kutsatira “nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.”​—Akolose 2:8.

Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Katekisimu wa Akatolika, amanena kuti: “Zinthu zimene Tchalichi [cha Katolika] chimakhulupirira sizimachokera m’Malemba Oyera okha. Choncho, kaya mfundo ndi yochokera m’miyambo ya anthu kapena m’Malemba Oyera, iyenera kulemekezedwa ndiponso kutsatiridwa mofanana.” Komanso m’nkhani ya m’magazini ina ya ku Toronto, ku Canada, munali mawu a m’busa wina yemwe anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani tikufunika kutsatira maganizo a munthu amene anakhala ndi moyo zaka 2000 zapitazo? Ifeyo patokha tili ndi nzeru zothandiza kwambiri, koma nthawi zambiri zimaoneka ngati zosathandiza chifukwa choti timazisintha kuti zigwirizane ndi mfundo za Yesu ndiponso za m’Malemba.”​—Maclean’s magazine.

Ponena za a Mboni za Yehova, buku lina linanena kuti: “Zonse zimene amakhulupirira ndiponso kutsatira pa moyo wawo amazitenga m’Baibulo.” (New Catholic Encyclopedia) Posachedwapa ku Canada, pamene wa Mboni za Yehova wina ankafuna kunena kuti ndi wa Mboni, munthu wina anamudula mawu n’kunena kuti: “Ndadziwa kale kuti ndiwe wa Mboni chifukwa cha Baibulolo. A Mboni okha ndi amene amakonda kugwiritsa ntchito Baibulo.”