Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sali Mbali ya Dziko”

“Sali Mbali ya Dziko”

“Sali Mbali ya Dziko”

“Dziko likudana nawo, chifukwa sali mbali ya dziko.”​—YOHANE 17:14.

Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? Popeza Yesu sanali mbali ya dziko, sankalowerera ndale komanso zochitika zina za m’nthawi yake. Iye ananena kuti: “Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” (Yohane 18:36) Iye analangizanso otsatira ake kuti azipewa maganizo, malankhulidwe ndiponso makhalidwe amene Mawu a Mulungu amaletsa.​—Mateyu 20:25-27.

Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: Munthu wina amene amalemba nkhani zachipembedzo, dzina lake Jonathan Dymond, analemba kuti Akhristu oyambirira “sankamenya nawo nkhondo ngakhale zitakhala kuti kuchita zimenezi kuwaika m’mavuto monga kunyozedwa, kumangidwa kapena kuphedwa kumene.” Iwo ankalolera kuvutika kusiyana n’kuti achite nawo ndale. Komanso khalidwe lawo linkachititsa kuti azisiyana ndi anthu ena. Akhristu anauzidwa kuti: “Chifukwa chakuti simukupitiriza kuthamanga nawo limodzi m’chithaphwi cha makhalidwe oipa, anthu a m’dzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.” (1 Petulo 4:4) Munthu wina wolemba mbiri yakale, dzina lake Will Durant, analemba kuti “anthu akunja, omwe ankakonda kwambiri zinthu zosangalatsa, ankaona kuti Akhristu ankawavutitsa chifukwa Akhristuwo ankatsatira kwambiri chikhulupiriro chawo komanso anali osasunthika pa nkhani ya makhalidwe abwino.”

Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Ponena za kusalowerera ndale kwa Akhristu, buku lina linanena kuti: “Mfundo yoti Mkhristu asamalowe usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake ndi yosamveka.” (New Catholic Encyclopedia) Komanso nkhani imene inalembedwa m’nyuzipepala ina inanena kuti lipoti limene bungwe lina loona za ufulu wa anthu a ku Africa linatulutsa linasonyeza kuti matchalitchi onse anamenya nawo nkhondo ya ku Rwanda m’chaka cha 1994, “kupatulapo Mboni za Yehova zokha.”​—Reformierte Presse.

Ponena za kupha anthu mwankhanza kumene kunachitika mu ulamuliro wa Nazi, mphunzitsi wina anadandaula kuti “panalibe gulu la anthu kapena bungwe lililonse m’dzikolo lomwe linanenapo chilichonse chosonyeza kukhumudwa ndi mabodza amene ankanenedwa komanso nkhanza zomwe zinachitika nthawi imeneyi.” Koma mphunzitsiyu atapita kumalo ena osungirako zinthu zakale, kumene anasungako zinthu zokumbukira zimene zinkachitika m’nthawi ya ulamuliro wa Nazi, iye analemba kuti: “Koma panopa ndadziwa zoona zake.” Mphunzitsiyo anazindikira kuti a Mboni za Yehova anakhalabe olimba pa chikhulupiriro chawo ngakhale kuti ankazunzidwa.

Nanga bwanji za makhalidwe a Akhristu? Magazini ina ya ku United States inanena kuti: “Achinyamata ambiri a mu mpingo wa Katolika sagwirizana ndi zimene chipembedzochi chimaphunzitsa zoti mwamuna ndi mkazi asamakhalire limodzi asanakwatirane [komanso] asamagonane asanakwatirane.” (U.S. Catholic) M’magaziniyi munalinso mawu a m’busa wa tchalitchichi akuti: “Anyamata ndi atsikana ambiri akamakwatirana amakhala atayamba kale kukhalira limodzi.” Koma buku lina linanena kuti a Mboni za Yehova “amayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino zivute zitani.”​—The New Encyclopædia Britannica.