Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kucheza ndi Mnzathu—Kodi Yesu Ndi Mulungu?

Kucheza ndi Mnzathu—Kodi Yesu Ndi Mulungu?

Kucheza ndi Mnzathu​—Kodi Yesu Ndi Mulungu?

A MBONI ZA YEHOVA amakonda kukambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Kodi pali nkhani iliyonse ya m’Baibulo imene simuimvetsa? Kodi mumafuna kudziwa zimene a Mboni amakhulupirira ndiponso zinthu zina zimene iwo amachita? Ngati ndi choncho, dzafunseni a Mboni za Yehova amene mungakumane nawo. Iwo adzasangalala kukambirana nanu nkhani zimenezi.

Tiyeni tione mmene wa Mboni za Yehova angachezere ndi munthu wina. Tiyerekeze kuti mtsikana wina wa Mboni, dzina lake Linda, wafika pakhomo pa mayi William.

Kodi N’zoona Kuti a Mboni za Yehova Simukhulupirira Yesu?

Mayi William: Abusa athu anandiuza kuti a Mboni za Yehova sakhulupirira Yesu. Kodi zimenezi ndi zoona?

Linda: Zimenezo si zoona. Ife timakhulupirira Yesu. Ndipotu timakhulupirira kuti, kuti munthu adzapulumuke ayenera kukhulupirira Yesu.

Mayi William: Inenso ndimakhulupirira zimenezo.

Linda: Ndiye kuti pa nkhani imeneyi inu ndi ine timakhulupirira zofanana. Koma sindinakuuzeni dzina langa. Ine ndine Linda. Nanga inu dzina lanu ndani?

Mayi William: Ndine mayi William. Ndasangalala kukudziwani.

Linda: Inenso ndasangalala kukudziwani. Mwina mungadabwe kuti, ‘Ngati a Mboni za Yehova amakhulupiriradi Yesu, n’chifukwa chiyani anthu amanena kuti iwo samukhulupirira?’

Mayi William: Ndi zimenenso ine ndikudabwa.

Linda: Mwachidule ndinganene kuti timamukhulupirira kwambiri Yesu, koma sikuti timakhulupirira zonse zimene anthu amanena zokhudza iye.

Mayi William: Mungandipatse chitsanzo cha zimene simukhulupirirazo?

Linda: Anthu ena amanena kuti Yesu anangokhala munthu wabwino chabe. Koma ife sitikhulupirira zimenezo.

Mayi William: Nanenso sindikhulupirira zimenezo.

Linda: Ndiye kuti apanso timakhulupirira zofanana. Komanso ife a Mboni za Yehova sitikhulupirira ziphunzitso zimene sizigwirizana ndi zimene Yesu ananena zokhudza mmene amaonera Atate wake.

Mayi William: Mukutanthauza chiyani?

Linda: Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti Yesu ndi Mulungu. Ndipo mwina n’zimenenso amaphunzitsa kutchalitchi kwanu.

Mayi William: Inde, abusa athu amanena kuti Yesu n’chimodzimodzi ndi Mulungu.

Linda: Koma ndikukhulupirira kuti mungandivomereze kuti njira yabwino yodziwira choonadi chokhudza Yesu ndi kuganizira mofatsa zimene Yesu mwini wakeyo anafotokoza zokhudza iyeyo.

Mayi William: Ndikugwirizanadi ndi mfundo imeneyo.

Zimene Yesu Ananena pa Nkhaniyi

Linda: Tiyeni tione lemba limene lingatithandize kumvetsa bwino nkhaniyi. Tiyeni tiwerenge lemba la Yohane 6:38. Yesu anati: “Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.” Mawu amenewatu angakhale osokoneza zitakhala kuti Yesu ndi Mulungu.

Mayi William: Mukutanthauza chiyani?

Linda: Onani kuti Yesu ananena kuti sanabwere padziko lapansi kudzachita chifuniro chake.

Mayi William: Zoonadi, iye ananena kuti anabwera kudzachita chifuniro cha amene anamutuma.

Linda: Ndiyeno ngati Yesu ali Mulungu, kodi ndani anam’tuma kuti abwere padziko lapansi? Ndipo n’chifukwa chiyani Yesu anamvera zofuna za amene anam’tumayo?

Mayi William: Ndayambano kumvetsa zimene mukutanthauza. Koma ndikuona kuti lemba limodzi lokhali silokwanira kutsimikizira kuti Yesu si Mulungu.

Linda: Chabwino, tiyeni tikambirane zimene Yesu ananena pa nthawi ina. Ananenanso mawu ofanana ndi amene tawerengawa, m’chaputala 7 cha buku la Yohane. Kodi mungawerenge Yohane 7:16?

Mayi William: Ndikhoza kuwerenga. “Yesu anawayankha kuti: ‘Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.’”

Linda: Zikomo kwambiri. Kodi lembali likusonyeza kuti Yesu ankaphunzitsa zinthu zongoganiza yekha?

Mayi William: Ayi, iye ananena kuti zimene ankaphunzitsa zinkachokera kwa amene anamutuma.

Linda: Mwayankha bwino. Pamenepanso tingafunse kuti: ‘Kodi ndani anam’tuma Yesu? Nanga ndani anamuuza choonadi chimene ankaphunzitsa?’ Kodi sindiye kuti amene anamutumayo ndi wamkulu kuposa Yesuyo? Chifukwatu munthu amene watuma mnzake ndiye kuti ndi wamkulu koposa wotumidwayo.

Mayi William: Mfundo imeneyi ndi yochititsa chidwi. Ndinali ndisanawerengepo lemba limeneli.

Linda: Tiyeni tiwerengenso mawu a Yesu opezeka pa Yohane 14:28. Iye anati: “Mwandimva ndikukuuzani kuti, Ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu. Ngati munali kundikonda, mukanakondwera kuti ndikupita kwa Atate wanga, chifukwa Atate ndi wamkulu kuposa ine.” Potengera mawu amene ali m’vesi limeneli, mukuganiza kuti Yesu amadziona bwanji poyerekezera ndi Atate wake?

Mayi William: Iye ananena kuti Atate ndi wamkulu. Choncho ndikuona kuti Yesu amaona kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa iyeyo.

Linda: Mwayankha bwino. Kuti tione chitsanzo china, tiyeni tiwerenge lemba la Mateyu 28:18 kuti tione zimene Yesu anauza ophunzira ake. Lembali limati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Kodi apa Yesu akusonyeza kuti anali ndi ulamuliro wonse kuyambira kalekale?

Mayi William: Ayi, iye ananena kuti ulamulirowo anachita kupatsidwa.

Linda: Ngati Yesu ali Mulungu, n’chifukwa chiyani anafunikanso kupatsidwa ulamuliro wina? Nanga ndani anam’patsa?

Mayi William: Komadi pamenepa m’pofunika kupaona bwino.

Kodi Ankalankhula Ndi Ndani?

Linda: Pali mfundo inanso imene ingakhale yosokoneza kwambiri zitakhala kuti Yesu nayenso ndi Mulungu?

Mayi William: Mfundo yanji?

Linda: Mfundo yokhudza zimene zinachitika pa ubatizo wa Yesu. Tiyeni tiwerenge lemba la Luka 3:21, 22. Kodi mungawerenge?

Mayi William: “Pamene anthu onse anali kubatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Ndipo pamene anali kupemphera, kumwamba kunatseguka. Pamenepo mzimu woyera wooneka ngati nkhunda unatsika kudzamutera. Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba, akuti: ‘Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.’”

Linda: Kodi lembali lanena kuti Yesu ankatani pa nthawi imene ankabatizidwa?

Mayi William: Ankapemphera.

Linda: Mwayankha bwino. ‘Ndiye ngati Yesu ali Mulungu, tingati iye ankapemphera kwa ndani?’

Mayi William: Limenelitu ndi funso labwino. Ndikawafunsa abusa athu.

Linda: Palinso mfundo ina yofunika kuiganizira. Yesu akutuluka m’madzi panamveka mawu ochokera kumwamba. Kodi mawuwo anali oti chiyani?

Mayi William: Anali oti Yesu ndi Mwana wake wokondedwa ndipo amakondwera naye.

Linda: N’zoona. Ndiye ngati Yesu ali Mulungu, ndani ananena mawu amenewa?

Mayi William: Ndinali ndisanaganizirepo zimenezi.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amatchedwa “Atate” wa Yesu Ndipo Yesu Amatchedwa “Mwana” wa Mulungu?

Linda: Mfundo ina yofunika kuiganizira ndi iyi: Tawerenga kuti Yesu ankatchula Mulungu kuti ndi Atate wake wakumwamba. Ndipo pamene Yesu ankabatizidwa panamveka mawu ochokera kumwamba otchula Yesu kuti ndi Mwana Wake. Ndipotu Yesu ankadzitchula kuti ndi Mwana wa Mulungu. Mutakhala kuti mukufuna kundifotokozera kuti anthu awiri abanja limodzi ndi ofanana, kodi munganene kuti chibale chawo ndi chotani?

Mayi William: Ndikhoza kunena kuti ndi munthu ndi mchimwene wake.

Linda: Ndi zoona. Ndiponso mwina tingati anthuwo ndi amapasa. Komatu Yesu ananena kuti iye ndi Mwana ndipo Mulungu ndi Atate wake. Kodi mukuganiza kuti Yesu ankatanthauza chiyani pamenepa?

Mayi William: Ndamvetsa. Yesu ankatanthauza kuti wina ndi wamkulu komanso ali ndi mphamvu zambiri kuposa wina.

Linda: Zoonadi. Ndiye ngati inu mwatha kudziwa kuti anthu awiri apachibale omwe ndi ofanana amakhala munthu ndi mchimwene wake, kuli bwanji Yesu? Yesu akanakhala kuti ndi Mulungu, kodi mukuganiza kuti iye, pokhala Mphunzitsi Waluso, sakanapeza mawu abwino osonyeza kuti iye ndi Mulungu ndi ofanana?

Mayi William: N’zachidziwikire kuti akanatero.

Linda: Koma monga taonera, iye anagwiritsa ntchito mawu akuti “Atate” ndi akuti “Mwana” pofotokoza ubale umene uli pakati pa iyeyo ndi Mulungu.

Mayi William: Mwafotokoza mfundo yabwino kwambiri ndipo ndaimvetsa.

Kodi Otsatira Oyambirira a Yesu Anaphunzitsa Zotani pa Nkhaniyi?

Linda: Ndisanapite ndingakondenso kukambirana nanu mfundo yomaliza pa nkhaniyi ngati muli ndi nthawi.

Mayi William: Nthawi ilipo.

Linda: Zikanakhala kuti Yesu ndi Mulungu, kodi mukuganiza kuti otsatira ake sakananena zimenezi?

Mayi William: Komaditu.

Linda: Koma palibe lemba lililonse limene limasonyeza kuti iwo ankaphunzitsa zimenezo. Koma taonani zimene mtumwi Paulo, yemwe ndi mmodzi mwa otsatira a Yesu oyambirira, analemba pa Afilipi 2:9. Iye anafotokoza zimene Mulungu anachita Yesu atafa n’kuukitsidwa. Iye anafotokoza kuti: “Mulungu anamukweza [Yesu] n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.” Kodi vesili likunena kuti Mulungu anamuchitira chiyani Yesu?

Mayi William: Likunena kuti Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba.

Linda: Inde. Koma zikanakhala kuti Yesu asanafe anali kale wofanana ndi Mulungu, ndiyeno pambuyo pake Mulungu n’kumukweza, kodi zimenezi sizikanachititsa kuti Yesu akhale wamkulu kuposa Mulungu? Kodi zingatheke kuti wina akhale wamkulu kuposa Mulungu?

Mayi William: Ayi, sizingatheke.

Linda: Inenso ndikuona choncho. Ndiye mukaganizira mfundo zonse zimene takambiranazi, mungati Baibulo limaphunzitsa kuti Yesu ndi Mulungu?

Mayi William: Ayi, ndikuona kuti siliphunzitsa choncho. Koma limaphunzitsa kuti iye ndi Mwana wa Mulungu.

Linda: N’zoona. Komabe chimene mungadziwe n’chakuti ife a Mboni za Yehova timalemekeza kwambiri Yesu. Timakhulupirira kuti imfa yake monga Mesiya inatsegula njira yoti anthu onse okhulupirika adzapulumuke.

Mayi William: Inenso ndimakhulupirira zimenezo.

Linda: Koma mwina mungafune kudziwa kuti, ‘Kodi tingamusonyeze bwanji Yesu kuti timayamikira zimene anachita popereka moyo wake chifukwa cha ife?’ *

Mayi William: Ndingakondedi kudziwa yankho la funso limenelo.

Linda: Ndidzabweranso tsiku lina kuti tidzakambirane yankho la Baibulo la funso limeneli. Kodi nditadzabweranso mlungu wamawa nthawi ngati yomwe ino, ndingadzakupezeni?

Mayi William: Ee ndidzakhalapo.

Linda: Chabwino, basi ndapita tidzaonana tsiku limenelo.

[Mawu a M’munsi]