Mayankho a Mafunso Onena za Yesu Khristu
Mayankho a Mafunso Onena za Yesu Khristu
“Kodi anthuwa akumati ine ndine ndani?”—LUKA 9:18.
YESU anafunsa ophunzira ake funso limeneli chifukwa ankadziwa kuti anthu anali ndi maganizo osiyanasiyana ponena za iye. Komatu panalibe chifukwa choti anthu azivutikira kudziwa kuti Yesu anali ndani. Yesu sankakhala kwayekhayekha n’kumachita zinthu mwachinsinsi. M’malomwake iye ankakonda kupita kumizinda ndi kumidzi, n’kumacheza ndi anthu momasuka. Iye ankalalikira ndiponso kuphunzitsa poyera chifukwa ankafuna kuti anthu adziwe zoona zokhudza iyeyo.—Luka 8:1.
Tikhoza kudziwa zoona zokhudza Yesu kuchokera pa zonena zake komanso zimene ankachita. Zinthu zimenezi zinalembedwa m’mabuku a Uthenga Wabwino, omwe ndi Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Mbiri youziridwa imeneyi ndi imene ingatithandize kupeza mayankho a mafunso athu onena za Yesu. *—Yohane 17:17.
FUNSO: Kodi Yesu anakhalakodi?
YANKHO: Inde. Anthu ena olemba mbiri yakale monga Josephus ndi Tacitus, omwe anakhalako m’nthawi ya atumwi, anatchula Yesu m’nkhani zawo ndipo zimenezi zikusonyeza kuti Yesu anakhalakodi. Komanso, Mauthenga Abwino amasonyeza kuti Yesu analidi munthu weniweni, osati wongopeka. Mauthenga Abwino amafotokoza momveka bwino nthawi komanso malo amene zinthu zomwe akufotokozazo zinachitikira. Mwachitsanzo, pofuna kusonyeza chaka chimene Yesu anayamba utumiki wake padziko lapansi, wolemba Uthenga Wabwino, Luka, anatchula olamulira 7. Mayina a anthu amenewa amapezekanso m’mabuku a olemba mbiri yakale.—Luka 3:1, 2, 23.
N’zochititsa chidwi kwambiri kuzindikira kuti pali umboni wamphamvu wotsimikizira kuti Yesu anakhalapodi. Buku lina linati: “M’tsogolo anthu ambiri ophunzira adzazindikira kuti Yesu Khristu wa ku Nazareti anakhalapodi m’nthawi ya atumwi.”—Evidence for the Historical Jesus.
FUNSO: Kodi Yesu ndi Mulungu?
YANKHO: Ayi. Yesu sankadziona kuti ndi wofanana ndi Mulungu. M’malomwake iye mobwerezabwereza anasonyeza kuti Yehova ndi wamkulu kuposa iyeyo. * Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti “Mulungu wanga” komanso “Mulungu yekhayo amene ali woona” ponena za Yehova. (Mateyu 27:46; Yohane 17:3) Munthu amene amadziona kuti ndi wotsika kuyerekezera ndi winayo ndi amene anganene mawu ngati amenewa. Wantchito akamanena munthu amene anamulemba ntchito kuti “bwana” kapena “achikulire” ndiye kuti akusonyeza kuti amadziona kuti ndi wotsika poyerekezera ndi amene anamulemba ntchitoyo.
Yesu anasonyezanso kuti iye ndi Mulungu si munthu mmodzi. Nthawi ina Yesu anauza anthu amene ankamutsutsa kuti: “M’Chilamulo chanu chomwechi analembamo kuti, ‘Umboni wa anthu awiri ndi woona.’ Ineyo pandekha ndimadzichitira umboni, ndipo Atate amene anandituma amandichitiranso umboni.” (Yohane 8:17, 18) Choncho Yesu ndi Yehova ndi anthu awiri osiyana. Akanakhala kuti iwo ndi munthu mmodzi, Yesu sakananena kuti iwo ndi mboni ziwiri. *
FUNSO: Kodi Yesu anali chabe munthu wabwino?
YANKHO: Ayi, sikuti Yesu anangokhala munthu wabwino basi. Iye analinso ndi maudindo ambiri pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu. Ena mwa maudindo amenewa ndi awa:
● “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.” (Yohane 3:18) Yesu ankadziwa kumene anachokera. Iye analipo kale kumwamba asanabwere padziko lapansi. Iye anati: “Ndinatsika kuchokera kumwamba.” (Yohane 6:38) Yesu anali woyamba kulengedwa ndi Mulungu ndipo anathandiza nawo polenga zinthu zina zonse. Popeza Yesu yekha ndi amene analengedwa mwachindunji ndi Mulungu, m’pake kuti amatchedwa “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.”—Yohane 1:3, 14; Akolose 1:15, 16.
● “Mwana wa munthu.” (Mateyu 8:20) Nthawi zambiri Yesu ankadzitchula kuti “Mwana wa munthu” ndipo mawu amenewa amapezeka pafupifupi ka 80 m’Mauthenga Abwino. Mawuwa akusonyeza kuti iye anali munthu weniweni, osati Mulungu yemwe anangovala thupi la munthu. Kodi zinatheka bwanji kuti Mwana wobadwa yekha wa Mulungu abadwe ngati munthu padziko lapansi? Pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera, Yehova anasamutsa moyo wa Mwana wake n’kuuika m’mimba mwa namwali wachiyuda dzina lake Mariya. Zimenezi zinachititsa kuti Mariya akhale ndi pakati. Zotsatira zake zinali zakuti Yesu anabadwa wopanda uchimo ndiponso wangwiro.—Mateyu 1:18; Luka 1:35; Yohane 8:46.
● “Mphunzitsi.” (Yohane 13:13) Yesu anasonyeza kuti ntchito imene Mulungu anam’patsa inali ‘kuphunzitsa ndi kulalikira uthenga wabwino’ wa Ufumu wa Mulungu. (Yohane 13:13; Mateyu 4:23; Luka 4:43) Yesu ankafotokoza tanthauzo la Ufumu wa Mulungu komanso zimene Ufumuwo udzachite pokwaniritsa chifuniro cha Yehova. Pochita zimenezi iye ankalankhula momveka bwino komanso ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva.—Mateyu 6:9, 10.
● “Mawu.” (Yohane 1:1) Yesu anali Womulankhulira wa Mulungu ndipo izi zikutanthauza kuti Mulungu ankagwiritsa ntchito iyeyo akafuna kupereka uthenga komanso malangizo kwa ena. Yehova anagwiritsanso ntchito Yesu kupereka uthenga kwa anthu padziko lapansi.—Yohane 7:16, 17.
FUNSO: Kodi Yesu anali Mesiya amene Mulungu analonjeza?
YANKHO: Inde. Maulosi a m’Baibulo ananeneratu za kubwera kwa Mesiya, kapena kuti Khristu. Mawu akuti Mesiya komanso akuti Khristu amatanthauza “Wodzozedwa.” Munthu amene Mulungu analonjezayu anali woti adzakhala ndi udindo waukulu pokwaniritsa cholinga cha Yehova. Nthawi ina, mayi wina wachisamariya anauza Yesu kuti: “Ndikudziwa kuti Mesiya akubwera, wotchedwa Khristu.” Ndiyeno Yesu anauza mayiyo momveka bwino kuti: “Munthu ameneyo ndi ineyo amene ndikulankhula nanu.”—Yohane 4:25, 26.
Kodi pali umboni uliwonse wosonyeza kuti Yesu analidi Mesiya? Inde, pali zinthu zitatu zokhudza moyo wa Yesu zimene zimatitsimikizira kuti iye anali Mesiya. Zinthu zimenezi n’zoti sizinachitikirepo munthu wina aliyense koma Yesu yekha. Tiyeni tione zinthu zimenezi.
● Mzera wake wobadwira. Baibulo linalosera kuti Mesiya adzakhala mbadwa ya Abulahamu kudzera m’banja la Davide. (Genesis 22:18; Salimo 132:11, 12) Yesu anali mbadwa ya Abulahamu komanso Davide.—Mateyu 1:1-16; Luka 3:23-38.
● Maulosi onena za Mesiya amene anakwaniritsidwa. M’Malemba Achiheberi muli maulosi ambirimbiri onena za moyo wa Mesiya padziko lapansi. Ena mwa maulosi amenewa anafotokoza mwatsatanetsatane za kubadwa kwa Mesiya komanso za imfa yake. Maulosi onsewa anakwaniritsidwa pa Yesu. Ena mwa maulosi amenewa ndi awa: Anabadwira ku Betelehemu (Mika 5:2; Luka 2:4-11), anaitanidwa kuti atuluke ku Iguputo (Hoseya 11:1; Mateyu 2:15) komanso anaphedwa koma mafupa ake sanathyoledwe (Salimo 34:20; Yohane 19:33, 36). Sizikanatheka kuti Yesu apangitse kuti maulosi ngati amenewa okhudza Mesiya akwaniritsidwe pa iye. *
● Umboni wochokera kwa Mulungu. Pa nthawi ya kubadwa kwa Yesu, Mulungu anatumiza angelo kuti akadziwitse abusa kuti Mesiya wabadwa. (Luka 2:10-14) Ndiponso pa nthawi imene Yesu ankachita utumiki wake padziko lapansi, Mulungu analankhula kangapo konse ali kumwamba mawu osonyeza kuti ankasangalala ndi Yesu. (Mateyu 3:16, 17; 17:1-5) Komanso Yehova anathandiza Yesu kuchita zozizwitsa. Yehova anachita zimenezi pofuna kupereka umboni wakuti Yesu analidi Mesiya.—Machitidwe 10:38.
FUNSO: N’chifukwa chiyani Yesu anafunika kuvutika komanso kufa?
YANKHO: Popeza Yesu anali wosalakwa sankafunikira kuvutika. Komanso sankafunikira kukhomeredwa pamtengo ngati chigawenga kuti afe imfa yochititsa manyazi. Komabe Yesu ankayembekezera kuti achitiridwa nkhanza zimenezi ndipo analolera kuti zimenezi zimuchitikire.—Mateyu 20:17-19; 1 Petulo 2:21-23.
Maulosi onena za Mesiya ananeneratu kuti Mesiyayo anayenera kuvutika komanso kufa n’cholinga choti aphimbe machimo a anthu. (Yesaya 53:5; Danieli 9:24, 26) Yesu ananena kuti anabwera padziko lapansi “kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Onse amene amakhulupirira imfa yake yansembe yowombola anthu, ali ndi mwayi wodzamasulidwa ku uchimo ndi imfa n’kukhala kosatha padziko lapansi la Paradaiso. *—Yohane 3:16; 1 Yohane 4:9, 10.
FUNSO: Kodi n’zoona kuti Yesu anaukitsidwa?
YANKHO: Inde. Yesu ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti adzauka. (Mateyu 16:21) Tiyenera kudziwa kuti Yesu komanso anthu amene analemba Baibulo sananene kuti Yesu akadzafa, adzauka yekha. Zimenezi zikanakhala zovuta kuzikhulupirira. M’malomwake Baibulo limanena kuti: “Mulungu anamuukitsa kwa akufa mwa kumasula zopweteka za imfa.” (Machitidwe 2:24) Ngati timakhulupirira kuti Mulungu alikodi ndipo iye ndi Mlengi wa zinthu zonse, ndiye kuti tili ndi chifukwa chokhulupiriranso kuti iye anaukitsa Mwana wake.—Aheberi 3:4.
Koma kodi pali umboni wodalirika wosonyeza kuti Yesu anaukitsidwadi? Inde. Taonani umboni wotsatirawu.
● Umboni wa anthu amene anamuona. Patadutsa zaka 22 pambuyo pa imfa ya Yesu, mtumwi Paulo analemba kuti panali anthu oposa 500 amene anamuona Yesu ataukitsidwa ndipo ambiri a iwo anali adakali moyo pa nthawi imene Paulo ankalemba zimenezi. (1 Akorinto 15:6) Umboni wa munthu mmodzi kapena awiri ungathe kutsutsidwa. Koma kodi ndani angatsutse umboni wa anthu 500?
● Mboni zodalirika. Ophunzira a Yesu analalikira molimba mtima kuti Yesu anaukitsidwadi. Umenewu unali umboni wodalirika chifukwa iwo ankadziwa zonse zimene zinachitika. (Machitidwe 2:29-32; 3:13-15) Ndipotu, iwo ankaona kuti chiphunzitso chakuti Yesu anaukitsidwa n’chofunika kwambiri kwa Akhristu. (1 Akorinto 15:12-19) Ophunzira amenewa anali okonzeka kufa m’malo mosiya kukhulupirira Yesu. (Machitidwe 7:51-60; 12:1, 2) Kodi pali munthu amene angalolere kufa akudziwa kuti mfundo imene akuferayo ndi yabodza?
Taona mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso 6 onena za Yesu. Mayankho amenewa atithandiza kudziwa kuti Yesu ndi ndani kwenikweni. Koma kodi kudziwa mayankho olondola a mafunso amenewa kuli ndi phindu lililonse? Kapena tifunse kuti, kodi pali vuto lililonse ndi zimene mungasankhe kukhulupirira ponena za Yesu?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Kuti mudziwe kusiyana kwa nkhani za Mauthenga Abwino za m’Baibulo ndi zolemba za anthu, werengani nkhani yakuti, “Kodi Pali Mabuku Ena a Uthenga Wabwino Amene Amafotokoza Nkhani za Yesu Zimene M’Baibulo Mulibe?” patsamba 18 ndi 19.
^ ndime 9 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.
^ ndime 10 Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kucheza ndi Mnzathu—Kodi Yesu Ndi Mulungu?” patsamba 20 mpaka 22.
^ ndime 21 Kuti muone maulosi ena amene anakwaniritsidwa pa Yesu, werengani tsamba 200 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
^ ndime 25 Kuti mudziwe zambiri ponena za dipo lowombola anthu limene Yesu anapereka kudzera mu imfa yake, onani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?