Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi ‘mpando woweruzira milandu’ umene Ayuda anamutengerako mtumwi Paulo unali chiyani?

Nkhani imene ili pa Machitidwe 18:12, 13 imanena kuti Ayuda a ku Korinto ankamuimba Paulo mlandu wolalikira mosemphana ndi chilamulo ndipo anamutengera “kumpando woweruzira milandu,” kapena kuti beʹma (omwe ndi mawu achigiriki otanthauza “malo okwera”). Mumzinda wakale wa Korinto munali malo enaake okwera omwe anali mkati mwa malo a zamalonda ndipo ayenera kuti anali pafupi ndi sunagoge. Malowa anali abwino kuimapo polankhula kwa anthu ambiri. Malowa anamangidwa ndi miyala ya mabo yabuluu komanso yoyera ndipo anali okongoletsedwa ndi zithunzi zochita kugoba. Malo oima munthu amene akulankhula anali ndi zipinda ziwiri zoyembekezerera zomwe zinali ndi mipando yopangidwa ndi miyala ya mabo ndipo pansi pake panali pokongoletsedwa mochititsa kaso.

Zikuoneka kuti malo oima munthu amene akulankhulawo ndi amene anatchulidwa kuti mpando woweruzira milandu kumene Ayuda anamupititsa mtumwi Paulo kuti akaonekere pamaso pa Galiyo, yemwe anali bwanamkubwa wachiroma wa chigawo cha Akaya. Pamalo amenewa ndi pamene pankakhala akuluakulu amene ankamvetsera mlandu komanso amene ankalengeza chigamulo kwa anthu amene abwera kudzamvetsera mlanduwo.

Nthawi zambiri anthu a m’mizinda ya ku Girisi ankasonkhana m’malo oterewa akafuna kukambirana nkhani zaboma. Pa nkhani yokhudza mlandu wa Yesu imene ili pa Mateyu 27:19 ndi pa Yohane 19:13, imene Mateyu ndi Yohane analemba m’Chigiriki, anafotokoza kuti Pontiyo Pilato ankalankhula ndi khamu la anthu atakhala pampando wake woweruzira milandu (kapena kuti beʹma).​—Machitidwe 12:21.

Kodi n’chifukwa chiyani Ayuda ena ankaona kuti mmene Yesu anafera ndi chinthu chokhumudwitsa?

Ponena za Akhristu oyambirira, mtumwi Paulo anati: “Ife timalalikira za Khristu amene anapachikidwa. Kwa Ayuda, chimenechi ndi chinthu chokhumudwitsa ndipo kwa mitundu ina ndi kupusa.” (1 Akorinto 1:23) Kodi n’chifukwa chiyani mmene Yesu anafera inali nkhani yokhumudwitsa kwa anthu ena?

Pofotokoza za mmene Yesu anafera komanso chikhalidwe cha anthu akale a ku Middle East, Ben Witherington III, yemwe anali katswiri wa Baibulo, ananena kuti imeneyi inali “imfa yochititsa manyazi kwambiri malinga ndi kaonedwe ka anthu akumeneko. Iwo ankaona kuti imfa yotereyi siyoyenera kwa munthu amene akufera anthu ena.” Witherington ananenanso kuti: “Pa nthawiyo anthu a ku Middle East ankakhulupirira kuti njira imene munthu wafera imasonyeza khalidwe limene munthuyo anali nalo. Tikatengera zimenezi, ndiye kuti anthu ankamuona Yesu ngati munthu wovutitsa ndiponso woukira boma amene ankafunika kulandira chilango chimene chinkaperekedwa kwa akapolo oukira.” Tikaganizira chikhalidwe cha anthuwa, n’zachidziwikire kuti Akhristu oyambirira sanangopeka nkhani zokhudza imfa komanso kuukitsidwa kwa Yesu.