Kodi Zimene Akhristu Amaphunzitsa Zimathandiza Bwanji Anthu a M’dera Lawo?
Kodi Zimene Akhristu Amaphunzitsa Zimathandiza Bwanji Anthu a M’dera Lawo?
NKHANI zapitazi zafotokoza chifukwa chake Akhristu oona samalowerera nawo ndale. Koma kodi Akhristu angasonyeze bwanji kuti akufuna kuthandiza anthu a m’dera lawo? Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kutsatira lamulo la Yesu lakuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mateyu 28:19, 20.
Lamulo la Yesu lakuti otsatira ake ayenera ‘kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira’ ndi logwirizana ndi malangizo akuti Akhristu ayenera kukhala ngati mchere komanso kuwala kwa dziko lapansi. (Mateyu 5:13, 14) Kodi kugwirizana kwake n’kotani? Nanga kodi ntchito yopanga ophunzira imathandiza bwanji anthu?
Uthenga wa Khristu Umateteza Komanso Kuunikira Anthu
Mchere umateteza zinthu kuti zisawonongeke. Nawonso uthenga umene Yesu analamula otsatira ake kuti aziphunzitsa uli ndi mphamvu yoteteza. Anthu amene amatsatira zinthu zimene Yesu anaphunzitsa amatetezeka ku makhalidwe oipa omwe ndi ofala kwambiri masiku ano. Kodi iwo amatetezeka bwanji? Amaphunzira mmene angapewere makhalidwe amene angawononge thanzi lawo, monga kusuta fodya ndiponso makhalidwe ena oipa. Iwo amakhala ndi makhalidwe monga chikondi, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima ndi ubwino. (Agalatiya 5:22, 23) Anthu amene amakhala ndi makhalidwe amenewa amakhala nzika zabwino m’dera limene amakhala. Akhristu akamauza anthu ena uthenga wotetezawu amakhala akugwira ntchito yofunika kwambiri yothandiza anthu a m’dera lawo.
Nanga kodi mawu amene Yesu ananena oti otsatira ake ayenera kukhala ngati kuwala akutanthauza chiyani? Mofanana ndi mmene mwezi umasonyezera kuwala kochokera ku dzuwa, otsatira a Khristu amasonyeza “kuwala” kochokera kwa Yehova Mulungu. Iwo amasonyeza kuwala kumeneku akamalalikira komanso kudzera m’ntchito zabwino zimene amachita.—1 Petulo 2:12.
Yesu anapitiriza kufotokoza kufanana kumene kulipo pakati pa kuwala ndi kukhala wophunzira wake. Iye anati: “Anthu akayatsa nyale, saivundikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale ndipo imaunikira onse m’nyumbamo. Momwemonso, onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu.” Nyale imene yayatsidwa n’kuiika pachoikapo chake, imaonekera kwa anthu onse amene ali pamalopo. Momwemonso kulalikira komanso ntchito zabwino zimene Akhristu amachita, ziyenera kuonekera kwa anthu onse. Kodi n’chifukwa chiyani ziyenera kuonekera kwa anthu onse? Yesu ananena kuti anthu amene angaone ntchito zabwinozo adzalemekeza Mulungu, osati Akhristuwo.—Mateyu 5:14-16.
Akhristu Onse Ayenera Kulalikira
Pamene Yesu ankanena kuti, “Inu ndinu kuwala kwa dziko” komanso kuti “onetsani kuwala kwanu,” ankauza ophunzira ake onse. Ntchito imene Yesu anaperekayi singakwaniritsidwe ndi anthu ochepa okha komanso amene ali m’zipembedzo zosiyanasiyana. M’malomwake, okhulupirira onse ndi “kuwala.” Choncho a Mboni za Yehova onse okwana 7 miliyoni, omwe amakhala m’mayiko oposa 235, amakhulupirira kuti ayenera kugwira ntchito yolalikira uthenga umene Khristu anafuna kuti otsatira ake azilengeza kwa anthu a m’dera lawo.
Kodi mfundo yaikulu ya zimene a Mboni za Yehova amalalikira ndi yotani? Pamene Yesu ankalamula otsatira ake kuti azilalikira, sanawalamule kuti azilalikira nkhani zandale, zachitukuko, za mgwirizano wa pakati pa tchalitchi ndi boma, kapena maganizo aliwonse a anthu. M’malomwake, iye analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Choncho, pomvera malangizo a Yesuwa, Akhristu oona masiku ano amalalikira za Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma lokhalo limene lidzathetse ulamuliro woipa wa Satanawu ndi kubweretsa dziko latsopano lachilungamo.
Ndipotu m’Mauthenga Abwino muli zinthu ziwiri zikuluzikulu zimene Yesu anachita mu utumiki wake zimene zimakhudzanso ntchito ya Akhristu oona masiku ano. Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti uthenga umene Akhristu amalalikira uli ngati mchere?
[Mawu Otsindika patsamba 9]
N’chifukwa chiyani tinganene kuti uthenga umene Akhristu amalalikira uli ngati nyale imene yaikidwa mu mdima?