Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Lili Ndi Malangizo Othandiza

Baibulo Lili Ndi Malangizo Othandiza

Baibulo Lili Ndi Malangizo Othandiza

“Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, ndi kuwala kounikira njira yanga.”​—SALIMO 119:105.

KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? Pali mabuku ambiri otchuka komanso olembedwa mwaluso komabe mabuku amenewa samapereka malangizo othandiza pa moyo wa munthu. Mabuku ambiri a malangizo amafunika kukonzedwanso nthawi ndi nthawi. Koma Baibulo limanena kuti “zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.”​—Aroma 15:4.

CHITSANZO: Ngakhale kuti cholinga chachikulu cha Baibulo sikupereka malangizo okhudza mmene tingakhalire ndi thanzi labwino, m’Baibulo muli malangizo abwino onena za zimene tingachite kuti tikhale ndi thanzi labwino. Mwachitsanzo Baibulo limanena kuti: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” (Miyambo 14:30) Limachenjezanso kuti: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (Miyambo 18:1) Ndiponso Baibulo limati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

ZIMENE AKATSWIRI APEZA: Kudekha, kuwolowa manja komanso kukhala ndi mabwenzi abwino kungakuthandizeni kukhala ndi thanzi labwino. Magazini ina inanena kuti: “Azibambo amene amapsa mtima kwambiri amakhala pangozi yoti akhoza kudwala matenda a kufa ziwalo kuposa azibambo amene amaugwira mtima.” (The Journal of the American Medical Association) Pa kafukufuku amene anachitika kwa zaka 10 ku Australia anapeza kuti anthu achikulire amene “ankacheza pafupipafupi ndi anzawo komanso anali ndi anthu owauza nkhani zawo zachinsinsi,” ankakhala ndi moyo wautali. Zotsatira za kafukufuku amene anachitika ku Canada komanso ku America m’chaka cha 2008, zinasonyeza kuti “munthu amene amagwiritsa ntchito ndalama zake pothandiza ena amakhala wosangalala kuposa munthu amene amangogwiritsa ntchito ndalama zake pa zofuna zake.”

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi mungakhulupirire malangizo okhudza thanzi labwino opezeka m’buku lomwe linalembedwa zaka zoposa 2,000 zapitazo? Koma monga taonera, Baibulo lili ndi malangizo othandiza ngakhale kuti linalembedwa zaka zoposa 2,000 zapitazo. Kodi umenewu si umboni wosonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Ndimaona kuti Baibulo ndi buku lothandiza kwambiri . . . chifukwa lili ndi malangizo abwino pa nkhani yokhudza mmene munthu angakhalire ndi thanzi labwino.”​—HOWARD KELLY, M.D., MPHUNZITSI WA YUNIVESITE YA ZAMANKHWALA YA JOHNS HOPKINS