Baibulo Ndi Lolondola pa Nkhani Zaukhondo
Baibulo Ndi Lolondola pa Nkhani Zaukhondo
“Kodi sindinakulembere zinthu zolangiza ndi zophunzitsa, n’cholinga chakuti ndikusonyeze kudalirika kwa mawu oona, kuti uthe kubwezera mawu oonadi?”—MIYAMBO 22:20, 21.
KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? Mabuku akale ambiri ali ndi mfundo zosadalirika zomwenso ndi zosagwirizana ndi njira zamakono zaukhondo. Masiku anonso nthawi ndi nthawi olemba mabuku amafunika kusintha zinthu zina ndi zina m’mabuku awo kuti zigwirizane ndi mfundo zimene zangotulukiridwa kumene. Koma Baibulo, popeza kuti linalembedwa ndi Mlengi, Mawu ake “amakhala kosatha.”—1 Petulo 1:25.
CHITSANZO: M’Chilamulo cha Mose, Aisiraeli analamulidwa kuti akafuna kudzithandiza azipita kumalo amene ankakhala “kunja kwa msasa” ndipo akamaliza azikwirira zonyansazo. (Deuteronomo 23:12, 13) Komanso Aisiraeli akakhudza nyama yakufa kapena mtembo wa munthu ankayenera kuchapa zovala zawo. (Levitiko 11:27, 28; Numeri 19:14-16) Pa nthawi imeneyo odwala khate ankakhala kwaokha mpaka wansembe atatsimikizira kuti khate lawo latha ndipo sangapatsirenso anthu ena.—Levitiko 13:1-8.
ZIMENE A ZAUMOYO APEZA: Kukhala ndi zimbudzi, kusamba m’manja, komanso kuika kwaokha anthu odwala matenda opatsirana, ndi njira zothandiza kwambiri kuteteza matenda. Ngati mukukhala pamalo oti palibe zimbudzi pafupi, bungwe lina la ku America loona za kapewedwe ka matenda osiyanasiyana linanena kuti: “Muzipita pamalo a mtunda wamamita 30 kuchokera pamene pali mtsinje, mjigo kapena chitsime, muzikumba n’kudzithandiza ndipo mukamaliza muzikwirira zonyansazo.” (U.S. Centers for Disease Control and Prevention) Malinga ndi zimene Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse limanena, kukhala ndi zimbudzi kumachepetsa matenda otsegula m’mimba. Komanso zaka zosachepera 200 zapitazo, madokotala anazindikira kuti anapatsira matenda anthu odwala ambiri chifukwa chosasamba m’manja atamaliza kugwira anthu amene amwalira. Bungwe la ku America lija linanenanso kuti kusamba m’manja ndi “njira yothandiza kwambiri pa njira zonse zopewera kutenga matenda.” Nanga bwanji za kuika kwaokha anthu akhate komanso odwala matenda ena opatsirana? Posachedwapa, magazini ina inati: “Mliri wa matenda ukangoyamba, kusunga kwaokha anthu amene akudwalawo ndi njira imene imathandiza kuti matenda asafalikire kwa ena.”—Saudi Medical Journal.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi palinso buku lina lachipembedzo limene mfundo zake zaukhondo zimagwirizana ndi mfundo zimene a zaumoyo apeza masiku ano? Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?
[Mawu Otsindika patsamba 6]
“Palibe amene sangachite chidwi akamawerenga malangizo okhudza nkhani zaukhondo amene anaperekedwa m’nthawi ya Mose.”—MANUAL OF TROPICAL MEDICINE, LOLEMBEDWA NDI DR. ALDO CASTELLANI NDI DR. ALBERT J. CHALMERS