Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amalalikira Kunyumba ndi Nyumba?
▪ M’Baibulo muli lamulo ili limene Yesu anauza otsatira ake: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mateyu 28:19, 20) Kodi lamulo limeneli likukhudza Akhristu onse? Ophunzira a Yesu oyambirira ankaona kuti lamuloli limakhudza Akhristu onse. Mwachitsanzo, mtumwi Petulo anati: “[Yesu] anatilamula kuti tilalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira.” (Machitidwe 10:42) Nayenso mtumwi Paulo anati: “Ndinalamulidwa kutero. Ndithudi, tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino!”—1 Akorinto 9:16.
Si mtumwi Paulo ndi Petulo okha amene anamvera lamulo limene Yesu anaperekali. Nawonso Akhristu onse a nthawi ya atumwi anamvera lamuloli. Iwo ankaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri pa zochita zawo zonse. (Machitidwe 5:28-32, 41, 42) Masiku anonso a Mboni za Yehova amaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Iwo amalalikira uthenga wofanana ndi umene Yesu ankalalikira wonena za “ufumu wakumwamba.”—Mateyu 10:7.
Kodi uthenga wa Ufumu uyenera kulalikidwa kwa ndani? Yesu anasonyeza kuti uthengawu uyenera kulalikidwa kulikonse komanso kwa anthu onse. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) Yesu analoseranso kuti mapeto a nthawi ino asanafike, “uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni.” (Mateyu 24:14) Kuti akwanitse ntchito imene anapatsidwayi, Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankachita khama kulalikira kwa anthu onse, osati anzawo okha kapena anthu amene alibe chipembedzo. (Akolose 1:23; 1 Timoteyo 2:3, 4) Mofanana ndi zimenezi, masiku ano a Mboni za Yehova amayesetsa kulalikira kwa aliyense. *
Kodi njira yabwino kwambiri yolalikirira uthenga wa Ufumu ndi iti? Yesu, yemwe ankadziwa bwino mmene tingalalikirire kwa anthu ambiri, anatumiza ophunzira ake kumizinda, kumidzi, komanso kunyumba za anthu. (Mateyu 10:7, 11, 12) Yesu atafa komanso kuukitsidwa, ophunzira ake anapitiriza kulalikira “kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 5:42) Mofanana ndi Yesu, iwo ankalalikiranso kwa anthu amene angokumana nawo komanso m’malo amene mumapezeka anthu ambiri. (Yohane 4:7-26; 18:20; Machitidwe 17:17) Masiku ano a Mboni za Yehova amagwiritsanso ntchito njira zimenezi polalikira kwa anthu onse.
Yesu anasonyeza kuti si anthu onse amene adzamvetsera uthenga wa Ufumu. (Mateyu 10:14; 24:37-39) Ndiye kodi zimenezi ziyenera kugwetsa ulesi Akhristu n’kuwachititsa kusiya kulalikira? Taganizirani chitsanzo ichi: Mukanakhala kuti mukugwira nawo ntchito yopulumutsa anthu pa nthawi imene kwachitika chivomezi, kodi mungasiye kufufuza anthu chifukwa choona kuti pambuyo pofufuza kwa nthawi yaitali mwangopeza anthu amoyo ochepa okha? N’zodziwikiratu kuti simungachite zimenezo. M’malomwake mungapitirizebe kufufuza makamaka ngati mukuona kuti pali chiyembekezo choti mupeza munthu wina. Yesu anauza ophunzira ake kuti ayenera kupitirizabe kulalikira ngati pali chiyembekezo choti papezeka enaake omwe angamvetsere uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 10:23; 1 Timoteyo 4:16) A Mboni za Yehova amasonyeza kuti amakonda Mulungu komanso anthu ena akamafunafuna anthu amene angamvetsere uthenga wabwino pamene akulalikira kunyumba ndi nyumba. Iwo amachita zimenezi chifukwa amadziwa kuti anthuwo afunika kumvetsera uthenga wa Ufumu kuti adzapulumuke.—Mateyu 22:37-39; 2 Atesalonika 1:8.
Magazini imene mukuwerengayi ili ndi uthenga wa m’Baibulo umenewo. Ngati mukufuna kudziwa zambiri, dzafunseni a Mboni za Yehova akadzafikanso kunyumba kwanu kapena lembani kalata n’kuitumiza kwa Mboni za Yehova pa adiresi iyi: P.O. Box 30749, Lilongwe 3, kapena gwiritsani ntchito adiresi yoyenerera pa maadiresi amene ali patsamba 4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Panopa a Mboni za Yehova akulalikira m’mayiko okwana 236. Chaka chatha, iwo anathera maola 1.7 biliyoni akulalikira ndipo anachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba okwana 8.5 miliyoni padziko lonse.