Maulosi Onse a M’baibulo Amakwaniritsidwa
Maulosi Onse a M’baibulo Amakwaniritsidwa
“Pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe.”—YOSWA 23:14.
KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? M’nthawi yakale, zimene ankanena olosera ambiri sizinkakwaniritsidwa ndipo n’chimodzimodzinso masiku ano. Anthu olosera amayesa kufufuza kuti adziwe zam’tsogolo potengera mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Koma maulosi a m’Baibulo amafotokoza zinthu mwatsatanetsatane ndipo nthawi zonse amakwaniritsidwa, ngakhale zitakhala kuti zinthuzo zinanenedwa kutatsala zaka zambirimbiri kuti zichitike.—Yesaya 46:10.
CHITSANZO: M’zaka za m’ma 500 B.C.E., mneneri Danieli anaona masomphenya amene ananeneratu kuti ufumu wa Mediya ndi Perisiya udzagonjetsedwa ndi ufumu wa Girisi. Masomphenyawa anasonyezanso kuti mfumu ya Girisi ‘ikadzangokhala yamphamvu’ nthawi yomweyo ‘idzathyoledwa.’ Kodi ndani amene anali kudzalowa m’malo mwake? Danieli analemba kuti: “Pali maufumu anayi amene adzauke mu mtundu wake, koma sadzakhala ndi mphamvu ngati zake.”—Danieli 8:5-8, 20-22.
ZIMENE AKATSWIRI A MBIRI YAKALE ANENA: Patapita zaka zoposa 200 kuchokera m’nthawi ya Danieli, Alekizanda Wamkulu anakhala mfumu ya Girisi. Patangotha zaka 10, Alekizanda anagonjetsa ufumu wa Mediya ndi Perisiya ndipo ulamuliro wake unafika mpaka kum’tsinje wa Indase (kumene masiku ano ndi ku Pakistan). Koma ali ndi zaka 32 anamwalira mwadzidzidzi. Kenako zotsatira za nkhondo imene inachitikira m’mudzi wa Isasi ku Asia Minor zinachititsa kuti ufumu wa Girisi ugawikane. Anthu anayi amene anapambana pa nkhondoyi anagawana Ufumu wa Girisi. Komabe palibe amene anafanana mphamvu ndi Alekizanda.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi palinso buku lina limene maulosi ake amakwaniritsidwa ngati Baibulo? Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?
[Mawu Otsindika patsamba 4]
“M’Baibulo muli maulosi . . . ambirimbiri moti n’zosatheka kuti maulosi onsewa akwaniritsidwe mwangozi.”—A LAWYER EXAMINES THE BIBLE, LOLEMBEDWA NDI IRWIN H. LINTON
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
© Robert Harding Picture Library/SuperStock