Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. N’chifukwa chiyani Mulungu anadzipatsa dzina?

N’zachidziwikire kuti mumasangalala munthu akakuitanani ndi dzina lanu lenileni, m’malo mongokuitanani kuti “abambo inu” kapena “amayi inu.” Dzina limathandiza kusiyanitsa munthu ndi munthu wina. Mulungu amadziwikanso ndi mayina aulemu monga akuti “Ambuye Wamkulu Koposa,” “Mulungu Wamphamvuyonse,”ndi “Mlengi Wamkulu.” (Genesis 15:2; 17:1; Mlaliki 12:1) Komabe Mulungu ali ndi dzina lenileni lomwe anadzipatsa yekha n’cholinga choti tithe kukhala naye pa ubwenzi. Dzina la Mulungu ndi Yehova.​—Werengani Yesaya 42:8.

Ngakhale kuti anthu ambiri pomasulira Baibulo anachotsa dzina lakuti Yehova n’kuikamo “Mulungu” kapena “Ambuye,” dzinalo limapezeka pafupifupi ka 7,000 m’mipukutu yakale ya Baibulo imene inalembedwa m’Chiheberi. Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amafuna kuti anthu adziwe dzina lake.​—Werengani Yesaya 12:4.

2. Kodi n’chifukwa chiyani kudziwa dzina la Mulungu kuli kofunika?

Kudziwa dzina la Mulungu kumatanthauza zambiri, osati kungodziwa katchulidwe kake. Kudziwa dzina la Mulungu kumatanthauza kudziwa bwinobwino Mulungu yemwe ndi mwini wake wa dzinalo komanso kukhala naye pa ubwenzi. Dzina lakuti Yehova limatanthauza “Iye Amachititsa Kukhala.” Tanthauzo la dzina la Mulunguli likutitsimikizira kuti iye angathe kukhala chilichonse kuti akwaniritse cholinga chake. Choncho kudziwa dzina la Mulungu kumatanthauzanso kukhulupirira kuti iye adzakwaniritsa malonjezo ake. (Salimo 9:10) Chikhulupiriro chimene anthu amene amadziwa ndi kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu amakhala nacho, chimawapangitsa kumudalira ndiponso kumuika pamalo oyamba m’moyo wawo. Anthu oterewa Yehova Mulungu adzawateteza.​—Werengani Salimo 91:14.

3. Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti anthu adziwe dzina lake?

Mulungu amafuna kuti anthu amudziwe komanso adziwe dzina lake chifukwa amene amamudziwa amapindula kwambiri. Kudziwa Mulungu kumathandiza anthuwo kukhala mabwenzi ake, komanso kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. N’chifukwa chake Yehova amafuna kuti tithandize anthu ena kudziwa dzina lake.​—Werengani Yohane 17:3; Aroma 10:13, 14.

Yesu anadziwikitsa dzina la Mulungu kwa anthu powaphunzitsa zimene Mulungu amafuna, malamulo Ake ndiponso malonjezo Ake. Masiku ano otsatira a Yesu akupitirizabe kugwira ntchito yothandiza anthu amitundu yonse kudziwa dzina la Mulungu. Amachita zimenezi mogwirizana, monga ‘anthu odziwika ndi dzina la Mulungu.’​—Werengani Machitidwe 15:14; Yohane 17:26.

4. Kodi Mulungu adzayeretsa bwanji dzina lake?

Yehova Mulungu akufuna kuyeretsa dzina lake chifukwa anthu akhala akulinenera zabodza. Mwachitsanzo, ena amanena kuti iye si Mlengi ndipo palibe chifukwa choti anthu azitsatira malamulo ake. Enanso amanena kuti iye satidera nkhawa ndipo ndi amene amachititsa mavuto padzikoli. Anthu amene amanena zimenezi amanyozetsa dzina la Mulungu. Koma anthu amenewa sadzachita zimenezi mpaka kalekale chifukwa Mulungu adzawononga anthu onse amene amanyozetsa dzina lake.​—Werengani Salimo 83:17, 18.

Yehova adzayeretsa dzina lake pamene adzawononge maulamuliro onse a anthu ndi kubweretsa mtendere kwa anthu. (Danieli 2:44) Posachedwapa aliyense adzadziwa kuti Mulungu woona ndi Yehova.​—Werengani Ezekieli 36:23; Mateyu 6:9.

Kodi inuyo muyenera kuchita chiyani? Yandikirani Mulungu mwa kuphunzira Mawu ake komanso kusonkhana ndi anthu amene amamukonda. Kuchita zimenezi n’kofunika chifukwa Yehova akamadzayeretsa dzina lake, sadzaiwala atumiki ake okhulupirika.​—Malaki 3:16.

Kuti mudziwe zambiri werengani mutu 1 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 16]

Dzina la Mulungu m’mipukutu yakale yachiheberi