Nkhani Zomwe Zili M’baibulo Sinthano Chabe
Nkhani Zomwe Zili M’baibulo Sinthano Chabe
“Ndafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi.”—LUKA 1:3.
KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? Nkhani zimene zimafotokozedwa m’mabuku a nthano zimakhala zoti sizinachitikedi. Mabukuwa satchulanso malo enieni amene zinthu zinachitikira, nthawi ngakhale mayina a anthu a m’mbiri yakale. Koma m’Baibulo muli nkhani zofotokozedwa mwatsatanetsatane ndipo zimenezi zimathandiza owerenga kukhulupirira kuti zimene Baibulo limanena “ndi choonadi chokhachokha.”—Salimo 119:160.
CHITSANZO: Baibulo limanena kuti “Nebukadinezara mfumu ya Babulo, . . . anatengera Yehoyakini [mfumu ya Yuda] ku Babulo.” Kenako “Evili-merodaki mfumu ya Babulo anakhala mfumu, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya Yuda ndi kumutulutsa m’ndende.” Komanso “tsiku lililonse [Yehoyakini] ankapatsidwa chakudya kuchokera kwa mfumuyo, masiku onse a moyo wake.”—2 Mafumu 24:11, 15; 25:27-30.
ZIMENE AKATSWIRI OFUFUZA ZINTHU ZAKALE APEZA: M’mabwinja a Babulo wakale, akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza makalata a boma omwe analembedwa pa nthawi ya ulamuliro wa Nebukadinezara Wachiwiri. M’makalatawa analembamo zinthu zimene zinkaperekedwa kwa akaidi komanso anthu ena amene ankakhala kunyumba yachifumu. Ena mwa anthu amene anatchulidwa m’makalatawa anali “Yaukini [Yehoyakini],” amene anali “mfumu ya Yahudi (Yuda),” pamodzi ndi banja lake. Nanga kodi panapezeka umboni uliwonse wosonyeza kuti Evili-merodaki, yemwe analowa m’malo mwa Nebukadinezara, anakhalakodi? Mphika wa maluwa umene unapezedwa pafupi ndi mzinda wa Susa unali ndi mawu akuti: “Nyumba yachifumu ya Amil-Marduk [Evili-merodaki], Mfumu ya Babulo, mwana wa Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo.”
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi pali buku lililonse lachipembedzo limene limafotokoza mbiri yakale molondola ngati mmene Baibulo limachitira? Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?
[Mawu Otsindika patsamba 5]
“Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya nthawi imene zinthu zinachitika komanso malo amene zinachitikira, n’zolondola ndiponso zodalirika kuposa zimene mabuku ena akale amanena.”—A SCIENTIFIC INVESTIGATION OF THE OLD TESTAMENT, LOLEMBEDWA NDI ROBERT D. WILSON
[Chithunzi patsamba 5]
Chikalata cha ku Babulo chimene chinatchula Mfumu Yehoyakini ya Yuda
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
© bpk, Berlin/Vorderasiatisches Museum, SMB/Olaf M. Tessmer/Art Resource, NY