Phunzitsani Ana Anu
Poyamba Anakana Kumvera Koma Kenako Anamvera
KODI unayamba wakana kuchita zimene wauzidwa?— * Mwina nthawi ina unaonera pulogalamu ya pa TV imene mayi kapena bambo ako anakuletsa kuti usamaonere. N’kutheka kuti pambuyo pake unaona kuti walakwa posawamvera. Panalinso munthu wina amene poyamba anakana kumvera. Munthu ameneyu dzina lake ndi Namani. Tiye tikambirane zimene zinamuthandiza kuti amvere.
Tiye tiyerekezere kuti tinalipo zaka zoposa 3,000 zapitazo. Pa nthawi imeneyo Namani anali mkulu wa gulu la asilikali a mfumu ya Siriya. Iye ndi amene ankauza asilikaliwo zoyenera kuchita ndipo iwo ankamumvera. Koma Namani anadwala matenda oopsa apakhungu otchedwa khate. Matendawa anachititsa kuti iye asamaoneke bwino komanso kuti azimva kuwawa kwambiri.
Mkazi wa Namani anali ndi kamtsikana ka ntchito ka ku Isiraeli. Tsiku lina kamtsikanaka kanauza abwana ake aakaziwo za munthu wina wa kwawo, ku Isiraeli, dzina lake Elisa. Iye ananena kuti Elisa akhoza kuchiritsa Namani. Namani atamva zimenezi, nthawi yomweyo ananyamuka ulendo wopita ku Isiraeli kukaonana ndi Elisa. Anatenga mphatso zambiri komanso anapita ndi asilikali ake. Iye anafikira kwa mfumu ya Isiraeli ndipo anafotokoza chimene anabwerera.
Elisa atamva za nkhaniyi anatumiza uthenga kwa mfumu woti auze Namani kuti apite kwa iye. Namani atafika kunyumba kwa Elisa, Elisa anangotumiza munthu kuti akamuuze kuti akasambe maulendo 7 mu Mtsinje wa Yorodano. Elisa ananena kuti Namani akachita zimenezi achira khate lake. Kodi ukuganiza kuti Namani anamva bwanji atauzidwa zimenezi?—
Namani anakwiya kwambiri. Choncho anakana kumvera zimene mneneri wa Mulunguyu ananena. Iye anauza asilikali ake kuti: ‘Kwathu kuja kuli mitsinje yabwino kuposa Yorodano. Sibwenzi nditangosamba komwe kuja?’ Atatero anayamba ulendo wobwerera kwawo. Koma kodi ukudziwa zimene asilikali ake aja anamufunsa?— Iwo anam’funsa kuti: ‘Kodi mneneriyo akanakuuzani kuti muchite chinthu chachikulu, simukanachita? Nanga bwanji mukulephera kumvera atakuuzani kuti muchite chinthu chosavuta?’
Namani anamvera ndipo anachita zimene asilikali ake ananena. Iye ankadumphira m’madzi muja kenako n’kutuluka ndipo anachita zimenezi kwa maulendo 6. Koma pamene ankatuluka m’madzimo pa ulendo wa 7 anadabwa kwambiri chifukwa khate lake lija linali litachoka. Iye anali atachiriratu. Nthawi yomweyo anabwerera kwa Elisa kukamuthokoza ndipo unali ulendo wamakilomita 48. Namani ankafuna kumupatsa Elisa mphatso zodula koma iye anakana kulandira mphatsozo.
Choncho Namani anapempha Elisa kuti amupatse kanthu kena. Kodi ukudziwa chimene anapempha?— Iye anapempha kuti: ‘Mundipatse dothi lotha kunyamulidwa ndi nyulu ziwiri.’ Kodi ukudziwa chifukwa chimene ankafunira dothilo?— Namani ananena kuti ankafuna kukapereka nsembe kwa Mulungu padothi lochokera ku Isiraeli, lomwe linali dziko la anthu a Mulungu. Kenako Namani analonjeza kuti sadzalambiranso mulungu wina koma Yehova yekha. Namani analeka kukhala wosamvera ndipo anayamba kumvera Mulungu woona.
Kodi ungatani kuti ukhale ngati Namani?— Ngati poyamba unali wosamvera, ungathe kusintha. Ukhoza kukhala womvera ngati utamatsatira malangizo abwino amene ena angakupatse.
Werengani Mavesi awa
^ ndime 3 Ngati mukuwerengera mwana nkhaniyi, mukapeza mzera muime kaye ndi kumulimbikitsa kuti anenepo maganizo ake.