Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Aliyense Amene Amamvetsera Tikamapemphera?

Kodi Pali Aliyense Amene Amamvetsera Tikamapemphera?

Kodi Pali Aliyense Amene Amamvetsera Tikamapemphera?

“Poyamba ndinkakayikira zoti kuli Mulungu komabe nthawi zina ndinkapemphera. Ndinkakayikira ngati pali wina amene ankamvetsera ndikamapemphera komabe ndinkaona kuti payenera kuti pali winawake amene amamvetsera. Pa nthawiyi, sindinkasangalala ndiponso sindinkaona chifukwa chokhalira ndi moyo. Komanso sindinkakhulupirira Mulungu chifukwa ndinkaganiza kuti munthu wanzeru zake sangakhulupirire zoti kuli Mulungu.”​—PATRICIA, * IRELAND.

KODI nanunso muli ndi maganizo ngati amenewa? Kodi mumakayikira zoti kuli Mulungu komabe n’kumapemphera? Ngati ndi choncho, dziwani kuti pali anthu enanso ambiri amene amakayikira ngati kuli Mulungu. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

▪ Pa anthu 2,200 amene anafunsidwa pa kafukufuku wina ku Britain, anthu 22 okha pa 100 alionse ndi amene ananena kuti amakhulupirira zoti kuli Mulungu amene analenga dziko lapansili komanso zoti Mulunguyo amamvetsera tikamapemphera. Komabe, anthu opitirira hafu ya anthu 2,200 amenewa nthawi zina amapemphera.

▪ Zotsatira za kafukufuku wina amene anachitika pa anthu 10,000 ochokera m’mayiko osiyanasiyana zinasonyeza kuti anthu pafupifupi 3,000 amene ankati samakhulupirira Mulungu, amapemphera.

Kodi N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Amakayikira Zoti Kuli Mulungu?

Munthu wina wa ku England, dzina lake Allan, ananena kuti: “Sindinkakhulupirira zoti kuli Mulungu chifukwa ndinkaona kuti anthu anangoyambitsa chipembedzo n’cholinga choti azilamulira anthu anzawo ndiponso ngati njira yopezera ndalama. Ndinkaganizanso kuti, kukanakhala kuti kuli Mulungu sibwenzi padzikoli pakuchitika zinthu zopanda chilungamo. Komabe nthawi zina ndinkapemphera ngakhale kuti sindinkadziwa kuti ndikulankhula ndi ndani. Komanso nthawi zina ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi zinatheka bwanji kuti ndikhale ndi moyo?’”

Pali zifukwa zosiyanasiyana zimene zimachititsa anthu kukayikira ngati pali aliyense amene amamvetsera tikamapemphera. Nthawi zambiri anthu amakayikira zoti kuli Mulungu chifukwa cholephera kupeza mayankho amafunso ngati awa:

▪ Kodi pali amene analenga zinthu zonse?

▪ N’chifukwa chiyani nthawi zambiri chipembedzo chimachita zinthu zoipa?

▪ Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?

Kudziwa mayankho a mafunso amenewa kungakuthandizeni kuti musamakayikire zoti pemphero ndi lothandiza.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina ena m’nkhani zoyambirirazi asinthidwa.