Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

ANTHU ena amapempherabe ngakhale kuti amakayikira zoti kuli Mulungu. Kodi n’chifukwa chiyani amakayikira? Mwina n’chifukwa choti iwo amaona kuti m’dzikoli muli mavuto ambiri. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?

Popeza panopa anthu ndi opanda ungwiro komanso amavutika, kodi mmenemu ndi mmene Mulungu anawalengera? Palibe amene angafune kulambira mulungu amene amafuna kuti anthu azivutika. Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti mukuyang’anitsitsa galimoto yokongola ndipo kenako mukuona kuti penapake m’pophwanyika, kodi mungaganize kuti ndi mmene inapangidwira? N’zodziwikiratu kuti simungaganize choncho. Muyenera kuti mungadziwe kuti inapangidwa bwinobwino koma pali munthu wina kapena chinachake chimene chinaphwanya galimotoyo.

N’chimodzimodzinso ndi chilengedwe. Tikayang’ana zinthu zonse zochititsa chidwi zimene Mulungu analenga, n’kuona mavuto amene anthu amakumana nawo, kodi tingaganize kuti ndi mmene Mulungu anatilengera? Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu analenga anthu awiri oyambirira ali angwiro koma patapita nthawi iwo anachita zinthu zimene zinachititsa kuti asakhalenso angwiro. (Deuteronomo 32:4, 5) Koma chosangalatsa n’chakuti Mulungu walonjeza kuti anthu omvera adzakhalanso angwiro. Komabe kodi n’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti anthu avutike kwa nthawi yaitali chonchi?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Anthu Avutike Kwa Nthawi Yaitali Chonchi?

Nkhani yagona poti, kodi ndani ali woyenera kulamulira anthu? Yehova sanalenge anthu kuti azidzilamulira okha. Iye ndi amene anayenera kukhala Wolamulira wawo. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu awiri oyambirira anasankha kupandukira ulamuliro wa Mulungu. Zimenezi zinachititsa kuti iwo akhale ochimwa. (1 Yohane 3:4) Zotsatira zake zinali zakuti iwo anakhala opanda ungwiro komanso anadzibweretsera okha mavuto ndipo anabweretsanso mavuto kwa anthu onse.

Kwa zaka zambiri Yehova walola kuti anthu azidzilamulira okha ndipo zimene zakhala zikuchitika zasonyeza kuti anthu sangathe kudzilamulira bwinobwino. Zimene zakhala zikuchitika zasonyeza kuti maulamuliro a anthu amayambitsa mavuto. Palibe boma limene lathetsa nkhondo, kuphwanya malamulo, kupanda chilungamo komanso matenda.

Kodi Mulungu Adzakonza Bwanji Zinthu Padzikoli?

Baibulo limanena kuti posachedwapa Mulungu abweretsa dziko latsopano lachilungamo. (2 Petulo 3:13) Anthu okhawo amene amasankha mwakufuna kwawo kukonda Mulungu komanso anthu ena ndi amene adzaloledwe kukhala m’dziko limenelo.—Deuteronomo 30:15, 16, 19, 20.

Baibulo limanenanso kuti pa ‘tsiku lachiweruzo,’ lomwe lili pafupi kwambiri, Mulungu adzachotsa mavuto onse komanso anthu onse amene amayambitsa mavutowo. (2 Petulo 3:7) Kenako Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, adzalamulira anthu omvera. (Danieli 7:13, 14) Kodi Yesu adzachita chiyani mu ulamuliro wake? Baibulo limati: “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11.

Monga Mfumu yakumwamba, Yesu adzathetsa matenda, ukalamba komanso imfa. Mavuto amenewa anayamba chifukwa choti anthu oyambirira anapandukira Yehova, yemwe ndi “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Yesu adzachiritsa anthu onse amene amagonjera ulamuliro wake womwe ndi wachikondi. Mu ulamuliro wake malonjezo a m’Baibulo awa adzakwaniritsidwa:

▪ “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’ Anthu okhala mmenemo adzakhala amene machimo awo anakhululukidwa.”—Yesaya 33:24.

▪ “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti posachedwapa Mulungu akwaniritsa lonjezo lake ndipo athetsa mavuto onse. Ngakhale kuti pakalipano Mulungu walola kuti anthu azivutika, tiyenera kukhala otsimikizira kuti iye amamva mapemphero athu.

Muyenera kukhala ndi chikhulupiriro choti Mulungu alipo ndipo amamva mukamapemphera n’kumamuuza mavuto anu. Ndipo iye amafunitsitsa kuti inuyo mudzakhale ndi moyo wosatha. Pa nthawi imeneyo simudzakayikiranso zoti iye alipo ndipo simudzakhalanso ndi vuto lililonse.