Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yandikirani Mulungu

Yandikirani Mulungu

Yandikirani Mulungu

ANTHU ambiri amene amati amakhulupirira Mulungu, sangathe kufotokoza chifukwa chenicheni chimene amamukhulupirira. Sangathenso kufotokoza chifukwa chake chipembedzo chimachita zinthu zoipa kapenanso chifukwa chake Mulungu walola kuti anthu azivutika. Chimene iwo amadziwa ndi kupemphera basi ngakhale kuti Mulungu samumvetsa.

Koma kodi mukudziwa kuti n’zotheka kumudziwa Mulungu bwinobwino? Mukhoza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ngati mutamudziwa Mulungu ndipo zimenezi zingachititse kuti muzimukonda komanso muziona kuti ndi wofunika kwambiri kwa inu. Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chenicheni ngati ali ndi umboni wa zimene akukhulupirirazo. (Aheberi 11:1) Kuphunzira zoona zokhudza Mulungu kungakuthandizeni kuti mumudziwe komanso kuti muzilankhula naye momasuka monga bwenzi lanu. Taonani zitsanzo za anthu ena amene ankapemphera kwa Mulungu ngakhale kuti ankakayikira zoti aliko.

Patricia, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, ananena kuti: “Tsiku lina anzanga omwe analipo pafupifupi 10 anayamba kukambirana nkhani yachipembedzo. Chimene chinachititsa kuti ayambe kukambirana nkhaniyi n’chakuti, ndinawauza anzangawo kuti ndinali nditachoka kunyumba chifukwa sindinkafuna kumvetsera zimene bambo anga, womwe sankakhulupirira zoti kuli Mulungu, ankakambirana ndi munthu wina wa Mboni za Yehova. Ndiyeno mnzanga wina ananena kuti, ‘Mwina zimene a Mboni za Yehova amanena n’zoona.’

“Ndipo mnzanga wina anayankha kuti, ‘Bwanji tsiku lina tidzapite ku misonkhano yawo kuti tikamve ngati amanenadi zoona.’ Ndipo tinapitadi. Ngakhale kuti tinkakayikira zimene tinamva kumeneko, ine ndi anzanga ena tinapitirizabe kumapita ku misonkhano ya Mboni chifukwa tinkaona kuti anthu ake ndi ochezeka.

“Komabe Lamlungu lina ndinamvetsera nkhani imene inasintha mmene ndinkaganizira. Munthu amene anakamba nkhaniyi anafotokoza chifukwa chake anthufe timavutika. Ineyo ndinali ndisanamvepo zoti munthu analengedwa ali wangwiro ndipo uchimo ndi imfa zinayamba ndi munthu mmodzi kenako n’kufalikira kwa anthu onse. Wokamba nkhaniyo anafotokozanso chifukwa chake imfa ya Yesu inali yofunika kuti ithandize anthu kupezanso zimene munthu woyambirirayo anataya. * (Aroma 5:12, 18, 19) Pasanapite nthawi ndinaona kuti zonse zimene ankanena zinali zomveka. Ndinayamba kuganiza kuti, ‘Ndiye kuti kuli Mulungu amene amatidera nkhawa anthufe.’ Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo pasanapite nthawi ndinayamba kuona kuti ndingathe kupemphera kwa winawake amene alipodi. Aka kanali koyamba kuti ndikhale ndi maganizo amenewa.”

Allan, yemwenso tamutchula m’nkhani yoyamba ija, ananena kuti: “Tsiku lina a Mboni za Yehova anafika kunyumba kwathu ndipo mkazi wanga anawalowetsa m’nyumba. Iye anachita zimenezi chifukwa ankafuna kudziwa zambiri zokhudza nkhani imene iwo ananena yoti anthu adzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Zimenezi zinandikwiyitsa kwambiri, choncho ndinamuitanira mkazi wanga kukhitchini n’kumuuza kuti, ‘Ine sindifuna zopusa. Zimene a Mboni amaphunzitsa si zoti ungamazikhulupirire.’

“Koma mkazi wanga anandiyankha kuti: ‘Bwanji tikamvetsere limodzi kuti mukatsimikize ngati amaphunzitsadi zabodza.’

“Koma nditamvetsera zimene a Mboniwo ankalankhula sindinapeze umboni woti zinali zabodza. Ndinaona kuti iwo anali anthu okoma mtima ndipo popita anandisiyira buku limene limafotokoza kuti zamoyo zinachita kulengedwa osati zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Bukuli linali ndi mfundo zomveka bwino komanso zokhala ndi umboni moti ndinaganiza kuti ndi bwino kuti ndidziwe zambiri za Mulungu. Ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni ndipo pasanapite nthawi yaitali ndinazindikira kuti zimene Baibulo limanena ndi zosiyana kwambiri ndi zimene ndinkaganiza zokhudza chipembedzo. Pamene ndinkapitiriza kuphunzira za Yehova ndinayamba kupemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima. Ndinali ndi makhalidwe ena omwe sanali abwino choncho ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kusiya makhalidwe amenewo. Ndikukhulupirira kuti Yehova anayankha mapemphero anga.”

Andrew, yemwe amakhala ku England, anati: “Ngakhale kuti ndinkachita chidwi kwambiri ndi sayansi, ndinkangokhulupirira mfundo yoti zinthu zinachita kusintha chifukwa choti anthu ena ankanena kuti pali umboni wa zimenezi. Sindinkakhulupirira zoti kuli Mulungu chifukwa cha zinthu zoipa zimene zimachitika padziko lapansili.

“Komabe nthawi zina ndinkaganiza kuti: ‘Ngati Mulungu alikodi, ndiye ndingafunike kumudziwa kuti ndi wotani. Mwachitsanzo, ndinkafuna kudziwa kuti n’chifukwa chiyani amalola kuti padzikoli pazichitika nkhondo ndi zinthu zina zoipa?’ Nthawi zina ndikakhala pa mavuto ndinkapemphera koma sindinkadziwa kuti ndikulankhula ndi ndani.

“Ndiyeno tsiku lina munthu wina anam’patsa mkazi wanga kapepala kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova kakuti, Kodi Dzikoli Lidzapulumuka? Limeneli linali funso limene ndinkadzifunsa nthawi zambiri. Kapepalaka kanachititsa kuti ndiyambe kuganizira kuti mwina ndi bwino kuti ndione mayankho a m’Baibulo a mafunso osiyanasiyana. Kenako pa nthawi ina ndili pa tchuthi, munthu wina anandipatsa buku lakuti, Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? * Nditazindikira kuti Baibulo ndi lolondola pa nkhani zasayansi, ndinaona kuti ndiyenera kuphunzira zambiri zimene limaphunzitsa. Choncho ndinavomera munthu wina wa Mboni za Yehova atandiuza kuti aziphunzira nane Baibulo. Nditayamba kumvetsa cholinga cha Yehova, ndinayamba kuona kuti iye ndi weniweni ndipo ndingathe kulankhula naye momasuka m’pemphero.”

Jan, mtsikana yemwe amakhala ku London ndipo anakulira m’banja lachipulotesitanti, ananena kuti: “Zinthu zachinyengo zimene zipembedzo zimachita komanso kuchuluka kwa mavuto padzikoli zinachititsa kuti ndisiye kupita kutchalitchi. Pa nthawiyi n’kuti ndili ku koleji choncho ndinasiyanso sukulu ndipo ndinayamba kuimba nyimbo kuti ndizipeza ndalama. Kenako ndinayamba kucheza ndi mnyamata wina dzina lake Pat. Iye anakulira m’banja lachikatolika koma nayenso anali atasiya kupita kutchalitchi.

“Tinkakhala ndi anzathu ena m’nyumba inayake imene eniake anachokamo. Anzathuwo nawonso anali atasiya sukulu ndipo ankachita chidwi ndi zipembedzo za ku Asia. Nthawi zina tinkafika mpaka usiku tikukambirana zokhudza mmene zinthu zamoyo zinayambira. Ngakhale kuti ine ndi Pat sitinkakhulupirira kuti kuli Mulungu, tinkaona kuti payenera kuti pali winawake amene analenga zinthu zamoyo.

“Kenako tinasamukira kumpoto kwa England kukafuna ntchito yoimba ndipo kumeneku n’kumene mwana wathu woyamba anabadwira. Tsiku lina usiku mwanayu anadwala ndipo ndinangopezeka kuti ndayamba kupemphera kwa Mulungu ngakhale kuti sindinkakhulupirira kuti aliko. Pasanapite nthawi yaitali ine ndi Pat tinayambana choncho ndinatenga mwana uja n’kuchoka. Apanso ndinapemphera poganiza kuti mwina pali winawake amene amamva mapemphero. Pambuyo pake ndinazindikira kuti Pat nayenso anapemphera.

“Patapita maola angapo, anthu awiri a Mboni za Yehova anafika kunyumba ya Pat ndipo anakambirana naye malangizo a m’Baibulo. Zitatero, Pat anandiitana n’kundifunsa ngati ndingakonde kuti tiziphunzira Baibulo ndi a Mboni. Titayamba kuphunzira Baibulo tinazindikira kuti tinkafunika kulembetsa ukwati wathu kuboma kuti tisangalatse Mulungu. Tikaganizira mmene banja lathu linalili, tinkaona kuti kuchita zimenezi n’kovuta kwambiri.

“Tinkafuna kudziwa zambiri zokhudza kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo, chifukwa chake padzikoli pali mavuto komanso kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani. Kenako tinazindikira kuti Mulungu amadera nkhawa anthu, ndipo tinayamba kufuna kuchita zimene iye amanena. Choncho tinalembetsa ukwati wathu. Malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu atithandiza kulera ana athu atatu. Tikukhulupirira kuti Yehova anayankha mapemphero athu.”

Muyenera Kufufuza Kuti Mupeze Umboni

Anthu amene atchulidwa m’nkhaniyi anapewa kupusitsidwa ndi chipembedzo chonyenga ndipo anadziwa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti padzikoli pakhale mavuto. Kodi mwaona kuti kumvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa n’kumene kunathandiza anthu onsewa kuti ayambe kukhulupirira zoti Yehova amayankha mapemphero?

Kodi mukufuna kupeza umboni woti Mulungu aliko? A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani kuphunzira zoona zokhudza Yehova komanso kukuthandizani kudziwa zimene mungachite kuti mukhale pa ubwenzi ndi “Wakumva pemphero” ameneyu.—Salimo 65:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kuti mudziwe zambiri ponena za dipo lowombola anthu limene Yesu anapereka kudzera mu imfa yake, onani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 12 Buku limeneli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

“Nditayamba kumvetsa cholinga cha Yehova, ndinayamba kuona kuti iye ndi weniweni ndipo ndingathe kulankhula naye momasuka m’pemphero”

[Chithunzi patsamba 9]

Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chenicheni ngati ali ndi umboni wa zimene akukhulupirirazo komanso ngati akufunitsitsa kudziwa zoona za Mulungu