Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi?—Mfundo Zitatu Zimene Anthu Amene Samakhulupirira Zozizwitsa Amanena

Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi?—Mfundo Zitatu Zimene Anthu Amene Samakhulupirira Zozizwitsa Amanena

Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi?​—Mfundo Zitatu Zimene Anthu Amene Samakhulupirira Zozizwitsa Amanena

YOYAMBA: N’zosatheka chifukwa sizigwirizana ndi mmene zinthu zimayendera m’chilengedwe. Timakhulupirira kuti zinthu m’chilengedwechi zimachitika mwanjira yakutiyakuti potengera zimene asayansi aona zikuchitika m’chilengedwe. Komabe sikuti timadziwa zonse zokhudza mmene zinthu zimayendera m’chilengedwechi. (Yobu 38:4) Mwachitsanzo, katswiri wa sayansi akhoza kutenga zaka zambiri akuphunzira n’cholinga choti amvetse mmene zinthu zinazake zimachitikira m’chilengedwe. Koma chinthu chimodzi chokha chikachitika mosiyana ndi zimene iye wakhala akukhulupirira, zimapangitsa kuti akaikire zonse zomwe wakhala akukhulupirirazo.

Pali nkhani ina imene imasonyeza kuti nthawi zina munthu angathe kuganiza kuti zinthu zina n’zosatheka asanamvetsetse nkhani yonse. John Locke, amene anabadwa mu 1632 n’kumwalira mu 1704, anafotokoza nkhani ina yonena za kazembe wa dziko la Holland ndi mfumu ya ku Siam. Pamene kazembeyo ankafotokozera mfumuyo za dziko lake, ananena kuti nthawi zina njovu ikhoza kuyenda pamwamba pa madzi. Mfumuyo inatsutsa zimenezi ndipo inaona kuti kazembeyo akunama. Koma kazembeyo sankanama kungoti zimene ankanenazo, zinali zoti mfumuyo inali isanazionepo. Mfumuyo sinkadziwa kuti madzi akazizira kwambiri amaundana n’kukhala ngati chimwala choti njovu ikhoza kuyendapo. Choncho, chifukwa choti mfumuyo sinkadziwa kuti zimenezi zimachitika, inkaona ngati n’zosatheka kuti njovu iyende pamadzi.

Taganizirani zinthu izi zimene anthu apanga masiku ano zomwe zinkaoneka ngati zosatheka zaka zingapo zapitazo:

● Ndege imatha kutenga anthu okwana 800 n’kuuluka kuchokera dziko lina kupita dziko lina lakutali osaima paliponse komanso pa liwiro la makilomita 900 pa ola limodzi.

● Anthu amatha kukambirana nkhani ngati kuti akulankhulana pamasom’pamaso koma ali m’mayiko osiyana pogwiritsa ntchito kompyuta.

● Anthu amasunga nyimbo zambirimbiri m’kachipangizo kakang’ono kuposa bokosi la machesi.

● Madokotala amatha kumuika munthu mtima wina kapena ziwalo zina.

Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa mfundo zimenezi? Ngati anthu akutha kuchita zinthu zomwe zinkaoneka ngati zosatheka zaka zingapo zapitazo, kuli bwanji Mulungu amene analenga zinthu zonse? Iye angachite zinthu zodabwitsa kwambiri zimene pakalipano sitingathe kuzimvetsa. *​—Genesis 18:14; Mateyu 19:26.

YACHIWIRI: Baibulo limafotokoza zozizwitsa n’cholinga choti anthu azilikhulupirira. Baibulo silitiuza kuti tizikhulupirira zozizwitsa zonse. Ilo limatichenjeza kuti tizikhala osamala kwambiri ndipo tisamangokhulupirira zozizwitsa zonse. Taonani chenjezo lomveka bwino ili: “Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana zoonetsedwa mu zozizwitsa zonse, zizindikiro ndi zodabwitsa za chinyengo ndi mtundu uli onse wazoipa umene upusitsa.”​—2 Atesalonika 2:9, 10, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Komanso Yesu Khristu anachenjeza kuti anthu ambiri azidzanena kuti amamutsatira koma sadzakhala otsatira ake enieni. Iye anati ena azidzanena kuti: “Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?” (Mateyu 7:22) Koma Yesu ananena kuti adzawakana anthu amenewa. (Mateyu 7:23) Choncho, Yesu sanaphunzitse kuti zozizwitsa zonse zimachitika mwa mphamvu ya Mulungu.

Mulungu sauza anthu amene amamulambira kuti azingodalira zozizwitsa zokha pa chikhulupiriro chawo. M’malomwake ayenera kukhulupirira zinthu zokhazo zimene zili ndi umboni wokwanira.​—⁠Aheberi 11:1.

Mwachitsanzo, tiyeni tikambirane nkhani yokhudza kuukitsidwa kwa Yesu Khristu, yomwe ndi chimodzi mwa zozizwitsa zolembedwa m’Baibulo zimene anthu amazidziwa bwino kwambiri. Patapita zaka zambiri Yesu ataukitsidwa, Akhristu ena a ku Korinto anayamba kukayikira ngati Yesu anaukitsidwadi. Kodi mtumwi Paulo anathandiza bwanji Akhristu amenewa? Kodi iye anangowauza kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro champhamvu”? Ayi. Taonani mmene iye anawakumbutsira umboni wosatsutsika wokhudza nkhaniyo. Iye anafotokoza kuti: “[Yesu] anaikidwa m’manda, kenako anaukitsidwa tsiku lachitatu, mogwirizana ndi Malemba. . . . Anaonekera kwa Kefa, kenako kwa atumwi 12 aja. Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambiri a iwo akali ndi moyo mpaka lero.”​—1 Akorinto 15:4-8.

Kodi kukhulupirira chozizwitsa chimenechi kunali kofunika kwa Akhristuwo? Paulo anapitiriza ndi mawu akuti: “Ngati Khristu sanauke, kulalikira kwathu n’kopanda pake, ndipo chikhulupiriro chathu n’chopanda pake.” (1 Akorinto 15:14) Paulo ankaona kuti nkhani yokhudza kuukitsidwa kwa Yesu ndi yofunika kwambiri. Ndipo iye ankaona kuti nkhaniyi ndi yoona chifukwa panali anthu ambiri amene anaona Yesu ataukitsidwa ndipo ambiri a iwo anali adakali ndi moyo pa nthawiyo. Ndipotu anthu amenewa anali okonzeka kufa m’malo mosiya kulankhula zimene anaona.​—1 Akorinto 15:17-19.

YACHITATU: Zozizwitsa ndi zochitika zachilengedwe kungoti anthu osaphunzira sazimvetsa. Akatswiri ena amanena kuti zozizwitsa zimene zinalembedwa m’Baibulo ndi zinthu wamba zoti zikhoza kuchitika ndipo si Mulungu amene anachititsa zinthu zimenezi. Iwo amaona kuti maganizo amenewa angathandize kuti zimene Baibulo limanena zikhale zosavuta kuzikhulupirira. N’zoona kuti nthawi zina zinthu zochitika mwachilengedwe monga zivomezi, miliri, komanso kugumuka kwa nthaka, zinagwiritsidwa ntchito popanga zozizwitsa. Koma anthu amene amanena kuti zozizwitsa ndi zochitika zachilengedwe amaiwala mfundo yakuti zozizwitsazo zinkachitika pa nthawi imene Malemba ananena kuti zichitika.

Mwachitsanzo, anthu ena amanena kuti mliri woyamba umene unagwera Aiguputo, pomwe madzi a mu Mtsinje wa Nailo anasintha n’kukhala magazi, sichinali chozizwitsa koma zinachitika chifukwa cha dothi lofiira komanso tizilombo tina tofiira zimene zinakokolokera mumtsinjewo. Koma Baibulo limanena kuti mtsinjewo unasanduka magazi, osati matope ofiira. Lemba la Ekisodo 7:​14-21 limasonyeza kuti chozizwitsa chimenechi chinachitika pamene Mose anauza Aroni kuti amenye Mtsinje wa Nailo ndi ndodo yake. Ngakhale zitakhala kuti kusintha kwa madzi a mumtsinjewo kunangochitika mwachilengedwe, tinganenebe kuti chinali chozizwitsa popeza kunachitika pa nthawi imene Aroni anamenya mtsinjewo ndi ndodo yake.

Chitsanzo china ndi zimene zinachitika pa nthawi imene mtundu wa Isiraeli unali pafupi kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Iwo anafika pa Mtsinje wa Yorodano ndipo pa nthawiyo n’kuti mtsinjewo utasefukira. Baibulo limatiuza zimene zinachitika. Limati: “Onyamula Likasawo atangofika kumtsinje wa Yorodano, n’kuponda madzi a m’mphepete mwa mtsinjewo . . . , madzi otsika kuchokera kumtunda anayamba kuima. Madziwo anakwera m’mwamba, ndipo anasefukira n’kupanga damu, limene linafika kutali kwambiri. Izi zinachitikira ku Adamu.” (Yoswa 3:15, 16) Kodi tingati zimenezi zinachitika chifukwa cha chivomezi kapena kugumuka kwa nthaka? Baibulo silinena choncho. Zimene zinachitikazi ndi chozizwitsa chifukwa zinachitika pa nthawi yeniyeni imene Yehova ananena kuti zichitika.​—Yoswa 3:7, 8, 13.

Baibulo limanena kuti zinthu zimenezi sizinangochitika mwachilengedwe koma zinali zozizwitsa. Ndiye kodi tinganene kuti zinthu zimenezi n’zosatheka chifukwa chakuti sizichitika tsiku ndi tsiku?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Ngati mumakayikira zoti Mulungu aliko, onani kabuku kakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? kapena kachingelezi kakuti Was Life Created? Kapenanso mungafunse wa Mboni za Yehova amene anakupatsani magaziniyi.

[Chithunzi patsamba 5]

Kale anthu ambiri ankaganiza kuti n’zosatheka kuti anthu angamayende pa ndege ulendo wautali pa nthawi yochepa