Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kucheza ndi Munthu Wina—Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?

Kucheza ndi Munthu Wina—Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?

Kucheza ndi Munthu Wina​—Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?

A MBONI ZA YEHOVA amakonda kukambirana ndi anzawo nkhani za m’Baibulo. Kodi muli ndi funso lililonse pa nkhani ya m’Baibulo limene mumafuna kudziwa yankho lake? Kodi mumafuna kudziwa zambiri zokhudza zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira ndiponso chifukwa chake amakhulupirira zimenezo? Ngati ndi choncho, dzafunseni wa Mboni za Yehova aliyense amene mungadzakumane naye. Adzasangalala kukambirana nanu nkhani zimenezi.

Tiyeni tione mmene wa Mboni za Yehova angachezere ndi munthu wina. Tiyerekeze kuti bambo ena a Mboni, dzina lawo a Samson, afika pakhomo pa a Owen.

Kodi Anthu Opita Kumwamba Adzakachitako Chiyani?

A Samson: Mukamaganizira za m’tsogolo, kodi mumaona kuti zinthu zidzaipa kwambiri kuposa panopa, zidzayamba kuyenda bwino kapena zidzangokhala mmene zilirimu?

A Owen: Ndimaganiza kuti zinthu zidzasintha. Ndimayembekezera kuti ndidzapita kumwamba kukakhala ndi Ambuye.

A Samson: Zimenezo ndi zosangalatsa. Baibulo limanena zambiri pa nkhani ya mmene kumwamba kuliri komanso za mwayi umene ena ali nawo wodzapita kumwamba. Komano kodi munaganizapo kuti anthu amenewa adzakachita chiyani kumwambako?

A Owen: Tidzakakhala ndi Mulungu ndipo tizidzamutamanda mpaka kalekale.

A Samson: Chimenechi ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri. Koma n’zochititsa chidwi kudziwa kuti Baibulo silimangonena za madalitso amene anthu opita kumwamba adzapeze, limanenanso za ntchito imene adzakhale nayo kumeneko.

A Owen: Adzagwira ntchito yotani?

A Samson: Ntchito imeneyi ndi imene yatchulidwa palemba la Chivumbulutso 5:10. Lemba limeneli limati: “[Inu Yesu] munawasandutsa mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu, moti adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” Kodi mwaona ntchito imene anthu amenewa adzagwire?

A Owen: Lembali lanena kuti adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.

A Samson: Mfundo imeneyitu ndi yosangalatsa, si choncho?

Kodi Iwo Azidzalamulira Ndani?

A Samson: Ndiye kodi sizoona kuti, ngati opita kumwambawo adzakhale mafumu ndiye kuti payeneranso kukhala anthu oti iwowo azidzawalamulira? Ndipo kodi pangakhale boma ngati palibe nzika?

A Owen: Ndayamba kumvetsa zimene mukutanthauza.

A Samson: Ndiyetu funso lofunika kuliganizira lingakhale lakuti, Kodi iwo adzalamulira ndani?

A Owen: Ndikuganiza kuti tizidzalamulira anthu omwe adzakhale adakali padzikoli amene sanafe n’kupita kumwamba.

A Samson: Zimenezi zikhoza kukhala zomveka zitakhala kuti anthu onse abwino amapita kumwamba. Koma pali nkhani ina imene mungafunikenso kuiganizira. Kodi n’kutheka kuti pali anthu ena abwino amene sadzapita kumwamba?

A Owen: Sindinamvepo zimenezo.

A Samson: Ndafunsa funso limeneli chifukwa cha zimene lemba la Salimo 37:29 limanena. Kodi mungawerenge lemba limeneli?

A Owen: Ndikhoza kuwerenga. Lembali likuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”

A Samson: Zikomo kwambiri. Kodi lembali likuti anthu ambiri abwino adzakhala kuti?

A Owen: Lembali lanena kuti adzakhala padziko lapansi.

A Samson: Mwayankha bwino, ndipotu sikuti adzakhalapo nthawi yochepa. Lembali lati: “Adzakhala mmenemo kwamuyaya.”

A Owen: Mwina lembali likutanthauza kuti padzikoli nthawi zonse pazikhala anthu abwino. Ifeyo tikafa n’kupita kumwamba anthu ena abwino amabadwanso n’kumakhala padzikoli.

A Samson: Anthu ambiri amamasulira choncho vesi limeneli. Koma vesili silikutanthauza zimenezo. Zimene likutanthauza ndi zoti, anthu abwino adzakhala padzikoli kwamuyaya.

A Owen: Pamenepa sindikumvetsa.

Dziko Lapansi Lidzakhala Paradaiso

A Samson: Tiyeni tione zimene lemba lina limanena zokhudza mmene moyo udzakhalire padzikoli m’tsogolo. Tiwerenge lemba la Chivumbulutso 21:⁠4. Ponena za anthu amene adzakhalepo pa nthawi imeneyo, lembali limati: “Iye [Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Kodi chiyembekezo chimenechi sichosangalatsa?

A Owen: N’chosangalatsa. Koma ndikuona kuti akunena mmene moyo udzakhalire kumwamba.

A Samson: N’zoona kuti opita kumwamba adzalandiranso madalitso amenewa. Koma taonaninso lembali, kodi likuti n’chiyani chidzachitikire imfa?

A Owen: Likunena kuti, “imfa sidzakhalaponso.”

A Samson: Zoona. Koma kuti chinthu chisakhaleponso, ndiye kuti poyamba chinalipo, eti?

A Owen: Inde.

A Samson: Komatu kumwamba kulibe imfa, padziko lapansi pano m’pamene anthu amafa, si choncho?

A Owen: Ndinali ndisanaganizepo zimenezo.

A Samson: N’zoona kuti Baibulo limaphunzitsa kuti anthu ena adzapita kumwamba koma limaphunzitsanso kuti anthu ambiri adzakhala padziko lapansi pompano mpaka kalekale. Ndikukhulupirira kuti munamvapo mawu otchuka awa: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.”​​—⁠Mateyu 5:⁠5.

A Owen: Eee ndinamvapo, lembali amaliwerenga nthawi zambiri kutchalitchi kwathu.

A Samson: Ngati Baibulo likunena kuti anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, kodi zimenezi sizikutanthauza kuti anthu adzakhala padzikoli? Anthu amene adzakhale padziko lapansili ndi amene adzasangalale ndi madalitso amene atchulidwa palemba la Chivumbulutso lija. Pa nthawiyo zinthu zidzasintha kwambiri chifukwa Mulungu adzakhala atachotsa zoipa zonse, ndi imfa yomwe.

A Owen: Ndikumvetsa zimene mukunena, koma sindingakhulupirire chifukwa cha malemba awiri okhawa.

A Samson: N’zoonadi. Koma sikuti pali malemba awiri okhawa amene amanena zimenezi. Palinso malemba ambiri amene amanena mmene moyo udzakhalire padzikoli m’tsogolo. Ngati muli ndi nthawi ndingakusonyezeni lemba lina, limenenso ineyo ndimalikonda kwambiri.

A Owen: Eee, ndisonyezeni.

“Woipa Sadzakhalakonso”

A Samson: Poyamba paja tinawerenga Salimo 37 vesi 29. Panopa tiyeni tiwerenge vesi 10 ndi 11. Kodi mungawerenge?

A Owen: Eee ndikhoza kuwerenga. “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”

A Samson: Zikomo kwambiri. Kodi vesi 11 likuti “anthu ofatsa” kapena kuti abwino, adzakhala kuti?

A Owen: Likunena kuti “adzalandira dziko lapansi.” Komabe ndikuona kuti vesi limeneli likunena zimene zikuchitika panopa chifukwa anthu abwino alipo padziko lapansili.

A Samson: Alipodi. Koma onani kuti vesili likunenanso kuti anthu abwino adzasangalala ndi “mtendere wochuluka.” Kodi panopa tikusangalala ndi mtendere wochuluka?

A Owen: Ayi.

A Samson: Ndiye kodi mukuganiza kuti lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa bwanji? Mwina tiyerekeze motere: Tinene kuti inuyo muli ndi nyumba yomwe mumachititsa lendi. Alendi anu ena ndi anthu abwino ndipo amasamalira nyumbayo komanso amayesetsa kukhala bwino ndi anthu ena. Inuyo mumasangalala kuti anthuwo azikhalabe m’nyumba mwanumo. Koma alendi anu ena ndi opanda khalidwe ndipo amawononga nyumba yanuyo komanso satha kukhala bwino ndi ena. Ngati alendi amenewa sakufuna kusintha khalidwe lawo loipali, kodi inuyo mungatani?

A Owen: Ndikhoza kuwathamangitsa.

A Samson: N’zimenenso Mulungu adzachite kwa anthu oipa amene ali padzikoli. Onaninso vesi 10, likuti: “Woipa sadzakhalakonso.” M’mawu ena tingati Mulungu “adzathamangitsa” anthu amene amachita zoipa. Zikadzatero anthu abwino azidzakhala mwamtendere. Ndikudziwa kuti mfundo yoti anthu abwino adzakhala padziko lapansi kosathayi, ndi yosiyana ndi zimene mwakhala mukukhulupirira.

A Owen: N’zoonadi, kutchalitchi kwathu satiphunzitsa zimenezi.

A Samson: Komanso, monga mmene munanenera poyamba paja, sikokwanira kungoona mavesi awiri okha. N’zofunika kuganizira zimene Baibulo lonse limanena zokhudza tsogolo la anthu abwino. Koma mukaganizira malemba amene takambirana lerowa, kodi sizoona kuti palinso anthu ambiri abwino amene adzakhale padziko lapansi?

A Owen: N’kuthekadi. Chifukwa malinga ndi malemba amene tawerengawa, zikuonekadi kuti pali ena opita kumwamba komanso pali ena ambiri omwe adzakhale padziko lapansi. Ndikuona kuti ndiyenera kuiganiziranso bwino nkhani imeneyi.

A Samson: Ndiyeno mukamaiganizira nkhaniyi, mwina mungakhalenso ndi mafunso ena awa: Nanga bwanji za anthu abwino amene anakhalako kalekale? Kodi anthu amenewa anapita kumwamba? Ngati sanapite kumwamba, ndiye kuti ali kuti?

A Owen: Amenewa ndi mafunso ochititsadi chidwi.

A Samson: Mwina ndisanapite, ndikulembereni mavesi angapo okhudza nkhani imeneyi kuti mukatsala muwerenge. * Ndiyeno ndidzabweranso kuti tidzakambirane bwinobwino malembawa.

A Owen: Mukatero muchita bwino kwambiri. Zikomo kwambiri.

[Mawu a M’munsi]