Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo wa Anthu Akale—Msodzi

Moyo wa Anthu Akale—Msodzi

Moyo wa Anthu Akale​—Msodzi

Pamene anali kuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, Yesu anaona amuna awiri apachibale akuponya ukonde wophera nsomba m’nyanja, pakuti anali asodzi. Mayina awo anali Simoni wotchedwa Petulo ndi Andireya. Iye anawauza kuti: ‘Nditsatireni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.’”​—MATEYU 4:18, 19.

NKHANI zonena za nsomba, asodzi komanso usodzi, zimatchulidwa kawirikawiri m’Mauthenga Abwino. Ndipotu Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo ambiri onena za usodzi. Izi n’zosadabwitsa chifukwa choti nthawi zambiri iye ankalalikira m’mbali mwa Nyanja ya Galileya. (Mateyu 4:13; 13:1, 2; Maliko 3:7, 8) Nyanja imeneyi ndi yokongola komanso madzi ake si amchere. Ndi yaitali makilomita pafupifupi 21 ndipo m’mbali mwake ndi yotambalala makilomita oposa 11. Zikuoneka kuti ambiri mwa atumwi a Yesu, monga Petulo, Andireya, Yakobo, Yohane, Filipo, Tomasi ndi Natanayeli, anali asodzi.​—Yohane 21:2, 3.

Kodi asodzi a nthawi ya Yesu ankagwira bwanji ntchito yawo, nanga ankagwiritsa ntchito zipangizo zotani? Tiyeni tikambirane za anthu amenewa. Zimenezi zikuthandizani kumvetsa ntchito imene atumwi ena ankagwira poyamba. Zikuthandizaninso kumvetsa bwino zimene Yesu anachita komanso mafanizo amene anagwiritsa ntchito. Choyamba, tiyeni tione mmene ntchito yausodzi inkayendera pa Nyanja ya Galileya.

“Panyanjapo Panabuka Mphepo Yamphamvu”

Nyanja ya Galileya ili pamalo otsika kwambiri. M’mbali mwake muli miyala ikuluikulu ndipo kumpoto kwake kuli phiri lalikulu komanso lokongola la Herimoni. M’nyengo yozizira, mphepo yamkuntho imachititsa kuti nthawi zina panyanjayi pachite mafunde. Nthawi yotentha, pamwamba pa nyanjayi pamakhala mpweya wotentha. Nthawi zina mphepo yamkuntho imawomba kuchokera m’mapiri a m’mbali mwa nyanjayi ndipo imasokoneza anthu amene akuwoloka nyanjayi. Nthawi ina Yesu ndi ophunzira ake anakumana ndi mphepo yotereyi.​—Mateyu 8:23-27.

Asodzi ankagwiritsa ntchito mabwato athabwa omwe kawirikawiri ankakhala aatali mamita oposa 8 komanso otambalala mamita oposa awiri. Mabwato ambiri ankakhala ndi chimtengo chachitali chopita m’mwamba ndipo kumbuyo kwake kunkakhala malo okhala ngati kachipinda. (Maliko 4:35-41) Mabwato amenewa ankayenda pang’onopang’ono komabe anali amphamvu moti ankatha kukoka ukonde wolemera kwinaku akuwombedwa ndi mphepo.

Asodzi ankapalasa mabwatowa ndi nkhafi zimene ankazimangirira m’mbali mwa mabwatowo. M’bwato munkakwera asodzi okwana 6 kapena kuposerapo. (Maliko 1:20) Ayenera kuti ankanyamula zinthu monga nsalu (1), chingwe (2), nkhafi (3), nangula wamwala (4), zovala zosinthira (5), zakudya (Maliko 8:14) (6), madengu (7), mapilo (Maliko 4:38) (8) ndi ukonde (9). N’kuthekanso kuti ankanyamula zinthu zothandiza kuti ukonde uziyandama (10), kapena uzimira (11), zipangizo zosokera ukonde (12) ndi zounikira (13).

“Anakola Nsomba Zochuluka Kwambiri”

Kuyambira kale, nsomba za m’Nyanja ya Galileya zimapezeka kwambiri m’malo amene mitsinje imakumana ndi nyanjayi. M’malo oterewa mumapezeka zomera zosiyanasiyana zimene zakokoloka ndi madzi ndipo nsomba zimabwera kudzadya zomerazo. Pofuna kuti aphe nsomba zambiri, asodzi a nthawi ya Yesu ankakonda kusodza usiku ndipo ankagwiritsa ntchito zounikira. Nthawi ina ophunzira ena a Yesu anagwira ntchito usiku wonse osapha nsomba. Koma tsiku lotsatira, atauzidwa ndi Yesu, anaponyanso makoka awo m’madzi ndipo anagwira nsomba zambiri moti mabwato awo anatsala pang’ono kumira.​—Luka 5:6, 7.

Nthawi zina asodzi ankapita kukapha nsomba pakati panyanja. Pogwira nsombazo, magulu awiri ankagwirira ntchito limodzi ndipo gulu lililonse linkakhala ndi bwato lake. Asodzi a gulu lina ankagwira mbali imodzi ya ukonde ndipo ena ankagwira mbali inayo. Akatero bwato lililonse linkalowera kwalokha n’kukakumana kutsogolo ndipo pa nthawiyi ankakhala atakokolola nsomba mu ukondewo. Mabwatowo akakumana ndiye kuti ukondewo umakhala utatsekeka moti nsombazo sizingatulukenso. Kenako asodziwo ankakoka zingwe zimene zinkakhala m’makona a ukondewo kuti nsombazo zikhuthukire m’bwato. N’kutheka kuti ukondewo unkakhala wautali kuposa mamita 30 ndiponso wotambalala mamita oposa awiri. Ukonde waukulu chonchi unali wokwanira kukokolola nsomba zonse zomwe zinali pamalopo. M’mwamba mwa ukondewo munkakhala zinthu zoyandama ndipo m’munsi mwake munkakhala zinthu zolemera. Asodzi akakhuthula nsombazo ankakonza ukondewo n’kuwuponyanso m’madzi ndipo ankabwereza zimenezi tsiku lonse.

Koma akamapha nsomba pamalo osaya, asodziwo ankagwiritsa ntchito njira ina. Iwo ankagwiritsa ntchito bwato limodzi ndipo ankagwira mbali imodzi ya ukonde n’kukazungulira nayo m’madzi kuti ukondewo ukokolole nsomba kenako ankabwereranso m’mbali mwa madzi. Asodzi ena amene ankaima kumtunda ankakoka ukondewo, kukhuthula nsombazo pamchenga, kenako n’kuyamba kuzisankha. Nsomba zabwino ankaziika m’zonyamulira ndipo zina ankazigulitsa kunyanja komweko zidakali zaziwisi. Koma zambiri ankaziyanika n’kuzithira mchere kapena kuzifutsa. Akatero ankazisunga m’mitsuko yadothi n’kuzitumiza ku Yerusalemu kapena mayiko ena. Nsomba zopanda mamba kapena zipsepse ankaziona kuti n’zodetsedwa ndipo ankazitaya. (Levitiko 11:9-12) Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha usodzi umenewu pamene anayerekezera “ufumu wakumwamba” ndi khoka. Anayerekezeranso nsomba zabwino ndi anthu abwino ndipo zoipa anaziyerekeza ndi anthu oipa.​—Mateyu 13:47-50.

Msodzi akakhala yekha, ankagwiritsa ntchito mbedza kapena ukonde waung’ono wooneka ngati kathumba, umene ena amautchula kuti tchafi. Akamagwiritsa ntchito ukonde woterewu, iye ankalowa m’madzi n’kugwira ukondewo dzanja limodzi n’kuuponya. Ukondewo unkatambasuka n’kugwera m’madzi, kenako n’kumira. Ndiyeno ankaukoka pogwiritsa ntchito chingwe chomwe chinkakhala pakati pa ukondewo ndipo akachita mwayi, ankakola nsomba zingapo.

Maukondewa anali okwera mtengo komanso ovuta kukonza akawonongeka, choncho ankawagwiritsa ntchito mosamala kwambiri. Msodzi ankakhala nthawi yambiri akusoka, kutsuka komanso kuyanika maukonde. Ankagwira ntchito zimenezi tsiku lililonse akamaliza kusodza. (Luka 5:2) Mtumwi Yakobo ndi m’bale wake Yohane anali m’ngalawa n’kumasoka maukonde awo pamene Yesu anawaitana kuti akhale otsatira ake.​—Maliko 1:19.

Asodzi akale ankagwira nsomba zosiyanasiyana, kuphatikizapo nsomba zooneka ngati chambo zomwe zinkapezeka zambiri m’Nyanja ya Galileya. Anthu ambiri a ku Galileya ankakonda kudya nsomba zamtundu umenewu. N’kutheka kuti nayenso Yesu anadyapo nsomba zimenezi zomwe zinkakhala zokoma kwambiri. Mwinanso nsomba ziwiri zouma zimene anagwiritsa ntchito pa chozizwitsa chimene anadyetsa khamu la anthu zinali zamtundu womwewu. (Mateyu 14:16, 17; Luka 24:41-43) Nthawi zambiri nsomba zamtundu umenewu zimasambira zitanyamula ana ake m’kamwa. Ngati sizinanyamule ana, zimatha kunyamula kamwala kokongola kapena kandalama kachitsulo kamene zakapeza pansi pa madzi.​—Mateyu 17:27.

Asodzi amene ankakhala odekha, akhama komanso opirira pa ntchito yawo zinthu zinkawayendera bwino. Anthu amene anavomera Yesu atawaitana kuti azigwira ntchito yophunzitsa anthu, ankafunikiranso makhalidwe amenewa kuti zinthu ziwayendere bwino pa ntchito yawo monga “asodzi a anthu.”​—Mateyu 4:18, 19.

[Chithunzi patsamba  19]

(Onani m’magazini yeniyeni)