Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzitetezera Choonadi

Muzitetezera Choonadi

Mwambo wa Omaliza Sukulu ya Giliyadi​—Gulu la Nambala 132

Muzitetezera Choonadi

PA MARCH 10, 2012 linali tsiku losaiwalika ku Patterson, New York kumene kumachitikira maphunziro osiyanasiyana a Mboni za Yehova. Anthu ambirimbiri, kuphatikizapo ochokera m’mayiko osiyanasiyana, anasonkhana pamodzi pa mwambo wa omaliza Sukulu ya Giliyadi ya gulu la nambala 132. Anthu ambiri anasonkhana ku Patterson pamene ena anaonera mwambowu kudzera pa mawailesi a kanema. Onse amene anamvetsera pologalamuyi analipo 9,042.

Anthu ankayembekezera mwachidwi pologalamuyi, ndipo onse amene anachita maphunzirowa anali kale mu utumiki wapadera wa nthawi zonse, zimene zinali zosiyana ndi makalasi a m’mbuyomu. Anthuwo ankatumikira pa Beteli, ena anali apainiya apadera, oyang’anira oyendayenda komanso amishonale omwe anali asanapite ku Sukulu ya Giliyadi. Anthu amene anali pa mwambowu ankadzifunsa kuti, kodi ophunzira amenewa auzidwa zotani?

Sipanatenge nthawi kuti adziwe yankho la funso limeneli. M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova amene anali tcheyamani pa mwambowu anakamba nkhani yoyamba. Iye anafunsa funso lochititsa chidwi lakuti, “Kodi Mumatetezera Choonadi?” Iye anafotokoza kuti Akhristu ayenera kutetezera choonadi chimene ndi ziphunzitso zonse zachikhristu. Kutetezera choonadi sikumangotanthauza kuphunzitsa anthu choonadicho ayi koma kumatanthauzanso kuthandiza anthu kukonda choonadi chimenechi.

M’bale Lösch anafunsa kuti, “kodi timatsimikizira bwanji kuti ichi ndi choonadi?” Kuchuluka kwa anthu amene ali m’choonadi si kumene kumatsimikizira kuti chimenechi ndiye choonadi. Ngakhale kuti masiku ano pali anthu ambirimbiri amene akulambira Yehova, ndi anthu ochepa chabe pa Pentekosite wa mu 33 C.E. amene anayamba kulambira Yehova. M’baleyu anafotokoza njira zisanu zimene timadziwira kuti ichi ndi choonadi: (1) Timatsatira zimene Yesu anaphunzitsa, (2) timakondana, (3) timatsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino, (4) sitilowerera m’ndale ndiponso (5) timadziwika ndi dzina la Mulungu.

“Muzikatsatira Malangizo Amene Mwapatsidwa”

Anthu amene anali pa mwambowu anadabwa ataona M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira atatulukira papulatifomu atatenga sutikesi. Mutu wa nkhani yake unali wakuti, “Muzikatsatira Malangizo Amene Mwapatsidwa,” imene inachokera palemba la Yesaya 50:5. Pofotokoza ulosi wokhudza Yesu Khristu, lembali limanena kuti: “Ineyo sindinapanduke. Sindinatembenukire kwina.”

M’bale Jackson analangiza ophunzirawo kuti azikamvera malangizo amene Yehova amapereka kudzera mwa mzimu woyera, Baibulo komanso gulu lake. M’fanizo la matalente limene likupezeka palemba la Mateyu 25:14-30, tinganene kuti kapolo aliyense analandira ndalama zofanana chifukwa aliyense anapatsidwa ndalama zogwirizana ndi zimene akanakwanitsa kuchita malinga ndi luso lake. Iwo ankafunika kugwiritsa ntchito ndalamazo mogwirizana ndi zimene anauzidwa. Mbuye wawo anayamikira akapolo awiri ndipo anawatchula kuti ‘akapolo abwino ndi okhulupirika.’ Munthu sakhala wokhulupirika chifukwa cha phindu limene wapeza. Munthu wokhulupirika ndi amene amamvera ndiponso kutsatira malangizo amene wapatsidwa.

Kapolo wachitatu anatchulidwa kuti, ‘kapolo woipa ndi waulesi’ komanso ‘wopanda pake.’ Kodi vuto lake linali chiyani? Iye anakwirira talente imene anapatsidwa. Talenteyi sinali ndalama imodzi yachitsulo koma zinali ndalama zolemera ngati madinari 6,000 omwe ankalemera makilogalamu 20. Makilogalamu amenewa ndi amene munthu amaloredwa kunyamula akakhala pa ulendo wapandege. Sinali ntchito yophweka kukwirira ndalama zimenezi zomwe zinali zolemera ngati sutikesi yomwe muli katundu wolemera makilogalamu 20. Choncho kapolo ameneyu anagwira ntchito ndithu pokwirira talenteyi, koma kungoti si zimene anauzidwa. Mofanana ndi zimenezi mmishonale angakhale wotanganidwa ndi kulemba makalata, kufufuza zinthu pa Intaneti, kumangosangalala ndi moyo basi kapena kuchita bizinezi. Pamene tsiku likutha munthu ameneyu amakhala atatopa chifukwa chochita zimenezi. Koma iye amakhala atatopa ndi zinthu zimene sanauzidwe kuchita. M’bale Jackson anamaliza nkhaniyi ndi mawu akuti: “Nthawi zonse muzitsatira malangizo amene mwapatsidwa.”

“Musakhale Ndi Mtima Wokayikira”

Umenewu unali mutu wa nkhani imene M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira anakamba. Iye ananena kuti: “Baibulo limasonyeza kuti chikhulupiriro ndi kukayikira siziyendera limodzi.” Choncho, “chikhulupiriro chingatithandize kuti tisamakayikire.” Satana anachititsa Hava amene anali wangwiro kukhala ndi mtima wokayikira. Choncho, iye angatichititsenso kuti tikhale ndi mtima wokayikira. M’bale Morris anapitiriza kunena kuti: “Limbitsani chikhulupiriro chanu ndipo mukatero simudzakhala ndi mtima wokayikira.” Iye anafotokoza za Petulo yemwe ‘anayenda pamadzi’ koma kenako, “ataona mphepo yamkuntho,” anachita mantha ndipo anayamba kumira. Yesu atamugwira dzanja anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani wakayikira?” (Mateyu 14:29-31) M’bale Morris ananenanso kuti: “Popeza kuti mudzakhala wotanganidwa mu utumiki wa nthawi zonse, anthu ena angachite chidwi ndi utumiki umene mukuchita ngati kuti mukuyenda pamadzi. Koma pamene mwakumana ndi mavuto ngati mphepo yamkuntho musakayambe kukayikira.”

M’bale Morris ananenanso kuti kupirira pamene munthu akukumana ndi mavuto kumakhala kovuta. Koma chosangalatsa n’chakuti m’kupita kwa nthawi mavutowo amatha. Iye analimbikitsa ophunzirawo kuti akakumana ndi mavuto aziganizira zimene Paulo ndi Sila anachita ataikidwa m’ndende ku Filipi. Lemba la Machitidwe 16:25 limanena kuti: “Chapakati pa usiku, Paulo ndi Sila anali kupemphera ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo, ndipo akaidi ena anali kuwamva.” Lembali likusonyeza kuti iwo sikuti ankangopemphera koma ankaimbanso nyimbo. Iwo ankaimba mokweza moti akaidi enanso ankamva. M’bale Morris ananenanso kuti ambirife sititha kuimba mwaluso koma tisamachite manyazi kuimba makamaka pa nthawi imene tili pa mavuto. Iye anamaliza nkhani yake powerenga mawu a nyimbo nambala 135 yakuti: “Pirirani Mpaka pa Mapeto,” yochokera m’buku la nyimbo lakuti Imbirani Yehova.

Nkhani Zinanso Zolimbikitsa

“Kodi Mukufuna Kukhala Ndi Moyo Wabwino Kwa Masiku Ambiri?” Uwu unali mutu wa nkhani imene M’bale Robert Luccioni wa m’Dipatimenti Yogula Zinthu anakamba. Mutuwu unali wochokera palemba la Salimo 34:12 omwe ndi mawu a Mfumu Davide. M’nkhani yakeyi, M’bale Luccioni anafotokoza zimene munthu angachite pa nthawi yamavuto n’cholinga choti akhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Tingaphunzire zambiri kuchokera palemba la 1 Samueli 30:1-31. Pa nthawi ina, Davide, anthu amene anali naye komanso mabanja awo anathawa Mfumu Sauli ndipo ankakhala ku Zikilaga. Pamene mabanja awo anatengedwa ukapolo ndi Aamaleki, amuna amene anali ndi Davidewo anamuukira ndipo ankafuna kumuponya miyala. Kodi Davide anatani? Iye sanafooke koma “anadzilimbitsa mwa Yehova Mulungu wake.” (1 Samueli 30:6) Davide anapempha Yehova kuti amuthandize, anatsatira malangizo amene anam’patsa ndipo anapulumutsa anthu amene anatengedwa ukapolowo. M’bale Luccioni anatsimikizira ophunzirawo kuti ngati angakhulupirire ndi kutsatira malangizo a Yehova, adzakhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri ndipo adzasangalala ndi utumiki wawo.

“Muziganizira Zabwino Zimene Mudzapeze Mukapirira.” Iyi inali nkhani imene M’bale Michael Burnett, yemwe ndi mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi, anakamba. Aisiraeli ankagawa usiku m’magawo atatu ndipo gawo lililonse linkakhala ndi maola anayi. Gawo lomalizira linkayamba 2 koloko usiku n’kutha 6 koloko m’mawa ndipo nthawi imeneyi inkakhala yozizira kwambiri ndiponso yovuta kukhala maso. Wamasalimo ankakonda kusinkhasinkha mawu a Yehova pa ulonda wausiku umenewu kuti asagone. (Salimo 119:148) M’bale Burnett anauza ophunzirawo kuti: “Muyenera kukhala maso. Nthawi zina mudzakumana ndi mavuto m’dzikoli. Choncho muyenera kukonzekeratu zimene mungachite pa nthawi yamavuto.” Iye anakumbutsanso ophunzirawo kuti ayenera kumaphunzira Mawu a Mulungu mozama n’cholinga choti azikhala maso. M’baleyu anafotokoza kuti: “Tsiku lililonse mumapemphera kwa Yehova chifukwa mumafuna kuti mukhale naye pa ubwenzi. Choncho inunso muzilola kuti Yehova azikulankhulani tsiku lililonse kudzera m’Baibulo. Mavuto amene timakumana nawo atsala pang’ono kutha. Choncho muyenera kuganizira zinthu zabwino zimene mudzachite m’tsogolo ndipo mukamachita zimenezi mudzapitirizabe kukhala maso pa nthawi imene mukukumana ndi mavuto.”

“Mwaphunzitsidwa Kuti Mukagwire Bwino Ntchito Yanu.” Umenewu unali mutu wa nkhani imene M’bale Mark Noumair, yemwe ndi mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi, anakamba ndipo unachokera palemba la 1 Petulo 5:10. Iye anafunsa ophunzirawo kuti: “Inuyo ndinu atumiki odziwa kale ntchito yanu, ndiye n’chifukwa chiyani mwaitanidwa kusukuluyi?” Iye anayankha kuti: “Chifukwa choti muli ndi luso pa ntchito imeneyi. Anthu ambiri odziwa bwino ntchito yawo amapitanso kusukulu kuti akawonjezere luso lawo. M’miyezi isanu yapitayi, Yehova wakhala ‘akukulimbitsani’ ndi ‘kukupatsani mphamvu’ mwa kukuphunzitsani mozama Mawu ake komanso mmene gulu lake limayendera n’cholinga choti mukathe kutumikira m’maudindo osiyanasiyana. Matabwa olimba sawonongeka msanga kapena kupindika. Mmene muzikachitira zinthu ndi abale ndi alongo anu ndi zimene zikasonyeze ngati mwapinduladi ndi sukuluyi kapena ayi. Kodi mukalola kuti mavuto akuchititseni kusiya kutsatira mfundo za Mulungu kapena mukapitirizabe kuzitsatira mogwirizana ndi zimene mwaphunzira m’Mawu ake? Chinthu cholimba n’chimene chingakwanitse kunyamula katundu wolemera. Kulimba kwa thabwa kumadalira mtundu wa mtengo. Inunso kuti muzitha kupirira mavuto zimadalira ngati muli olimba mwauzimu. Yehova wakuphunzitsani kuti mukhale olimba komanso odalirika pa utumiki umene mudzapatsidwe m’tsogolo. Choncho tinganene kuti iye wachita mbali yake ndipo pemphero lathu ndi lakuti inunso muchite mbali yanu ndipo mulole kuti ‘Mlangizi Wamkulu,’ yemwe ndi Yehova, amalizitse kukuphunzitsani.”

Zokumana Nazo Komanso Kucheza Ndi Ophunzira

Nthawi zonse zimakhala zolimbikitsa pa mwambowu kumva ophunzira akufotokoza okha zimene anakumana nazo ndipo izi n’zimenenso zinachitika. Ophunzirawo anachita zitsanzo zosonyeza zina zimene anakumana nazo. Mwachitsanzo, banja lina la ku France linakhala maola 6 pabwalo la ndege likuyembekezera kukwera ndege pa ulendo wawo wopita ku Sukulu ya Giliyadi. Ali pamalo odyera a pabwalo la ndegewo, anayamba kukambirana ndi anthu awiri omwenso ankayembekezera kukwera ndege. Pamene mmodzi wa anthuwa ananena kuti ndi wa ku Malawi, iwo anayamba kulankhulana naye m’Chichewa. Iye anadabwa kuona kuti akulankhula chinenero chake. Iwo ananena kuti ndi amishonale a ku Malawi. Pamene wina uja ananena kuti ndi wa ku Cameroon, iwo anayamba kulankhula naye m’Chifulenchi ndipo zimenezi zinamudabwitsa kwambiri. Anthuwo anachita chidwi kwambiri ndi Mboni za Yehova ndipo zimenezi zinachititsa kuti amishonalewo apeze mpata wowalalikira.

M’bale Nicholas Ahladis, yemwe ali m’Dipatimenti Yothandiza Omasulira, anafunsa mafunso mabanja awiri. Banja lina ndi la ku Australia ndipo limatumikira ngati amishonale m’dziko la East Timor lomwe munali nkhondo. Banja linalo ndi la ku Korea ndipo limatumikira ku Hong Kong. Mabanja onsewa anali okonzeka kubwerera ku mayiko amene ankatumikirawo kuti akagwiritse ntchito zimene anaphunzira kusukuluyi.

Ophunzirawo atalandira zikalata zosonyeza kuti amaliza maphunziro awo, mmodzi mwa ophunzirawo anawerenga kalata yothokoza chifukwa cha malangizo amene analandira. M’mawu ake omaliza, M’bale Lösch, anagwiritsa ntchito mawu ambiri ophiphiritsa. Iye ananena kuti choonadi ndi chokongola ngati utawaleza. Anayerekezeranso choonadi ndi chitsime cha madzi m’chipululu komanso ndi nangula amene amathandiza sitima kuti isamire pa nthawi ya mphepo yamkuntho. Iye anauza ophunzirawo kuti: “Muli ndi mwayi waukulu kudziwa choonadi. Muzitetezera choonadi chimenechi ndipo muzithandizanso ena kuti azichitetezera.”

[Tchati/​Mapu patsamba 31]

ZA OPHUNZIRAWO

Mayiko amene ophunzirawo anachokera: 12

Avereji ya zaka zobadwa: 36

Avereji ya zaka zimene akhala Mboni kuchokera pamene anabatizidwa: 20

Avereji ya zaka zimene achita utumiki wa nthawi zonse: 15

[Mapu]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ophunzirawa anatumizidwa kumayiko amene ali pansipa:

KUMENE OPHUNZIRA ANATUMIZIDWA

BELIZE

BENIN

CAMBODIA

CAMEROON

CAPE VERDE

CÔTE D’IVOIRE

DOMINICAN REPUBLIC

EAST TIMOR

ECUADOR

GABON

GEORGIA

GUINEA

HONG KONG

LIBERIA

MADAGASCAR

MALAWI

PERU

SAMOA

SÃO TOMÉ AND PRÍNCIPE

UNITED STATES OF AMERICA

ZIMBABWE

[Chithunzi patsamba 31]

Gulu la Nambala 132 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Pamndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mumzera uliwonse, mayina tawandandalika kuyambira dzina la munthu amene ali kumanzere kupita kumanja.

(1) Iap, R.; Iap, J.; Ng, T.; Ng, P.; Laurino, F.; Laurino, B.; Won, S.; Won, S.

(2) Morales, N.; Morales, M.; Zanutto, J.; Zanutto, M.; Rumph, I.; Rumph, J.; Germain, D.; Germain, N.

(3) Atchadé, Y.; Atchadé, Y.; Thomas, C.; Thomas, E.; Estigène, C.; Estigène, P.

(4) Ehrman, D.; Ehrman, A.; Bray, J.; Bray, A.; Amorim, M.; Amorim, D.; Seo, Y.; Seo, Y.

(5) Simon, J.; Simon, C.; Seale, C.; Seale, D.; Erickson, J.; Erickson, R.

(6) McCluskey, D.; McCluskey, T.; Brown, A.; Brown, V.; Mariano, D.; Mariano, C.; Loyola, Y.; Loyola, C.

(7) Rutgers, P.; Rutgers, N.; Foucault, P.; Foucault, C.; Wunjah, J.; Wunjah, E.