Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yandikirani Mulungu

Yehova Amadana ndi Zinthu Zopanda Chilungamo

Yehova Amadana ndi Zinthu Zopanda Chilungamo

MUNTHU wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Mawu amenewa, omwe analembedwa zaka 3,000 zapitazo, akufotokoza bwino mmene zinthu zilili m’dzikoli masiku ano. Anthu ambiri amakonda kugwiritsa ntchito molakwa mphamvu ndipo zimenezi zimachitika kulikonse. Nthawi zambiri anthu audindo amapondereza aumphawi, osauka ndi ovutika. Kodi Yehova amamva bwanji akamaona kupanda chilungamo kotereku? Yankho la funso limeneli likupezeka palemba la Ezekieli 22:6, 7, 31.​—Werengani.

M’Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisiraeli, munali lamulo lomveka bwino loti anthu audindo asamagwiritse ntchito mphamvu zawo molakwika. Yehova akanadalitsa mtunduwo pokhapokha ngati atsogoleri ake akanati azisonyeza kukoma mtima komanso kuganizira anthu osauka. (Deuteronomo 27:19; 28:15, 45) Koma m’nthawi ya Ezekieli atsogoleri a ku Yerusalemu ndi Yuda ankagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. Kodi iwo ankachita zimenezi motani?

Atsogoleriwa ankagwiritsa ntchito ‘dzanja lawo modzipereka kuti akhetse magazi.’ (Vesi 6) Mawu akuti “dzanja” akutanthauza mphamvu kapena udindo. N’chifukwa chake Baibulo lina linamasulira vesi limeneli kuti: “Akazembe a Isiraeli . . . akhulupirira mphamvu yawo kuti akhetse magazi.” M’dziko simungakhale chilungamo ngati atsogoleri ake, omwe amayenera kulimbikitsa anthu kuti azitsatira malamulo, akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika komanso akupha anthu osalakwa.

Chifukwa cha zimenezi Ezekieli anadzudzula atsogoleriwo komanso anthu amene ankawatsanzira posamvera Chilamulo cha Yehova. Ezekieli ananena kuti: “Anthu anyoza abambo ndi amayi awo.” (Vesi 7) Anthuwa sankalemekeza makolo awo ngati mmene Yehova ankafunira. Choncho iwo anachititsa kuti mtundu wawo usakhale wamphamvu chifukwa mabanja olimba ndi amene akanachititsa kuti mtunduwo ukhale wamphamvu.​—Ekisodo 20:12.

Anthu oipawa ankadyera masuku pamutu anthu osauka. Iwo akamaphwanya Chilamulo cha Mulungu ankasonyeza kuti sakuzindikira kuti Yehova anawapatsa Chilamulocho chifukwa chowakonda. Mwachitsanzo, Chilamulo cha Mulungu chinawauza Aisiraeli kuti aziganizira anthu amene sanali Aisiraeli omwe ankakhala pakati pawo. (Ekisodo 22:21; 23:9; Levitiko 19:33, 34) Koma Aisiraeliwo ankachitira mlendo “zinthu mwachinyengo.”​—Vesi 7.

Aisiraeli ankazunzanso “mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye,” ndipo anthu amenewa analibe wowathandiza. (Vesi 7) Yehova amadera nkhawa kwambiri ana ndiponso akazi amasiye. Iye analonjeza kuti adzapereka chilango kwa amene amazunza anthu amenewa.​—Ekisodo 22:22-24.

Mwa zochita zawozi, Aisiraeli anasonyeza kuti sankalemekeza Chilamulo cha Mulungu chimene iye anawapatsa chifukwa chowakonda. Kodi Yehova anachita chiyani? Iye ananena kuti: “Ndidzawadzudzula mwamphamvu.” (Vesi 31) Yehova anachitadi zimenezi chifukwa mu 607 B.C.E., analola kuti Ababulo awononge Yerusalemu n’kutenga Aisiraeli kupita nawo kuukapolo.

Mawu a palemba la Ezekieli 22:6, 7, 31 akutiphunzitsa mfundo ziwiri zokhudza mmene Yehova amaonera zinthu zopanda chilungamo. Choyamba, Yehova amadana ndi zinthu zopanda chilungamo. Chachiwiri, iye amachitira chifundo anthu amene akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamozo. Mulungu sanasinthe. (Malaki 3:6) Iye walonjeza kuti posachedwapa adzachotsa kupanda chilungamo komanso anthu onse amene amachita zinthu zopanda chilungamo. (Miyambo 2:21, 22) Tikukulimbikitsani kuti muphunzire zambiri za Mulungu ameneyu, yemwe “amakonda chilungamo” komanso zimene mungachite kuti mumuyandikire.​—Salimo 37:28.

Mavesi amene mungawerenge mu August:

Ezekieli 21-38

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Yehova anapereka lamulo lomveka bwino loti anthu audindo asamagwiritse ntchito mphamvu zawo molakwika