Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zozizwitsa Zimene Zichitike Posachedwapa

Zozizwitsa Zimene Zichitike Posachedwapa

Zozizwitsa Zimene Zichitike Posachedwapa

NGATI mutapezeka kuti muli ndi vuto linalake lofunika opaleshoni, kodi mungamve bwanji mutadziwa kuti dokotala amene akuchiteni opaleshoniyo sanachitepo opaleshoni yamtundu umenewo? Mosakayikira mungakhale ndi nkhawa. Komano bwanji mutadziwa kuti dokotalayo ndi katswiri ndipo wapangapo maopaleshoni ambirimbiri ofanana ndi imene akufuna kukupanganiyo? Kodi simungamudalire kuti akuthandizani?

M’dzikoli muli mavuto ambiri, choncho tingati likufunika opaleshoni. Kudzera m’Mawu ake, Baibulo, Yehova Mulungu walonjeza kuti adzabwezeretsa dzikoli kuti likhalenso Paradaiso. (2 Petulo 3:13) Koma kuti zimenezi zitheke, Mulungu adzachotsa kaye mavuto onse amene ali padzikoli. (Salimo 37:9-11; Miyambo 2:21, 22) Zinthu zonse zoipa zimene zimachitika padzikoli ziyenera kuchotsedwa kaye, Mulungu asanabwezeretse dzikoli kukhalanso paradaiso. Zimene Mulungu adzachitezi tingatinso ndi zozizwitsa.​—Chivumbulutso 21:4, 5.

A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti zimenezi zichitika posachedwapa. Iwo amakhulupirira zimenezi chifukwa zozizwitsa zimene Yehova Mulungu wachita kale zimasonyeza kuti ali ndi mphamvu yokwaniritsa malonjezo ake. Taonani zozizwitsa 6 zotsatirazi, zimene zinalembedwa m’Baibulo, ndipo muziyerekeze ndi zimene limalonjeza kuti zidzachitika m’tsogolo.

Pitirizani kuphunzira Baibulo kuti mudziwe zimene Mulungu akulonjeza kudzatichitira m’tsogolomu. Kukhulupirira kwambiri Yehova kungakuthandizeni kuti muzikhulupiriranso kuti malonjezo ake adzakwaniritsidwadi ndipo mudzasangalala pa nthawi imene Yehova adzachite zozizwitsa zinanso zambiri.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 9, 10]

CHOZIZWITSA:

YESU ANACHULUKITSA MITANDA YA MKATE NDI NSOMBA ZOCHEPA N’KUDYETSA KHAMU LA ANTHU.​—MATEYU 14:13-21; MALIKO 8:1-9; YOHANE 6:1-14.

LONJEZO:

“Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.”​SALIMO 67:6.

ZIMENE ZIDZACHITIKE:

PALIBE ALIYENSE AMENE ADZAVUTIKENSO NDI NJALA.

CHOZIZWITSA:

YESU ANACHIRITSA ANTHU AKHUNGU.​—MATEYU 9:27-31; MALIKO 8:22-26.

LONJEZO:

“Maso a anthu akhungu adzatsegulidwa.”​YESAYA 35:5.

ZIMENE ZIDZACHITIKE:

ANTHU ONSE AKHUNGU ADZACHIRITSIDWA.

CHOZIZWITSA:

YESU ANACHIRITSA ANTHU OLUMALA.​—MATEYU 11:5, 6; YOHANE 5:3-9.

LONJEZO:

“Munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo.”​YESAYA 35:6.

ZIMENE ZIDZACHITIKE:

KULUMALA KWA MTUNDU ULIWONSE SIKUDZAKHALAPONSO.

CHOZIZWITSA:

YESU ANACHIRITSA MATENDA OSIYANASIYANA.​—MALIKO 1:32-34; LUKA 4:40.

LONJEZO:

“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”​YESAYA 33:24.

ZIMENE ZIDZACHITIKE:

MATENDA ONSE OSACHIRITSIKA ADZATHA NDIPO ALIYENSE ADZAKHALA NDI THANZI LABWINO.

CHOZIZWITSA:

YESU ANALETSA MPHEPO NDI MAFUNDE.​—MATEYU 8:23-27; LUKA 8:22-25.

LONJEZO:

“Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzagwira ntchito pachabe.”​YESAYA 65:21, 23.

“Kuponderezedwa udzatalikirana nako, ndipo sudzaopa aliyense. Chilichonse choopsa udzatalikirana nacho, pakuti sichidzakuyandikira.”YESAYA 54:14.

ZIMENE ZIDZACHITIKE:

SIKUDZAKHALANSO MASOKA ACHILENGEDWE.

CHOZIZWITSA:

YESU ANAUKITSA AKUFA.​—MATEYU 9:18-26; LUKA 7:11-17.

LONJEZO:

“Onse ali m’manda achikumbutso . . . adzatuluka.”​YOHANE 5:28, 29.

“Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi manda zinapereka akufa amene anali mmenemo.”​CHIVUMBULUTSO 20:13.

ZIMENE ZIDZACHITIKE:

OKONDEDWA ATHU AMENE ANAMWALIRA ADZAUKITSIDWA.