Mavuto Amene Akazi Amakumana Nawo
“Ndikaona mmene amuna amazunzira azimayi, sindifuna nditakhala mzimayi.”—ZAHRA, WAZAKA 15, mawu akewa akupezeka m’magazini ina yachifulenchi.
MAWU amene mtsikana ameneyu analankhulawa akusonyeza kuti padziko lonse atsikana ndiponso azimayi amachitidwa nkhanza komanso kusalidwa. Zimenezi zimawakhudza kwambiri pa moyo wawo wonse. Taonani zinthu zina zimene akazi amakumana nazo.
Kusalidwa. Ku Asia, makolo ambiri amakonda ana aamuna kuposa aakazi moti lipoti lina, limene bungwe la United Nations linatulutsa m’chaka cha 2011, linasonyeza kuti ku Asia ana akazi pafupifupi 134 miliyoni anafa chifukwa cha kuchotsa mimba, kuphedwa ali akhanda komanso kutayidwa.
Maphunziro. Pa chiwerengero cha anthu onse amene ali padziko lonse lapansi, pali atsikana ndi azimayi opitirira hafu ya chiwerengerochi amene sanapite kusukulu kapena anangopita zaka zinayi zokha.
Kugonedwa mokakamiza. Azimayi oposa 2 biliyoni amagonedwa ndi amuna awo mowakakamiza ndipo m’mayiko ambiri zimenezi sizionedwa ngati mlandu.
Zaumoyo. M’mayiko amene akukwera kumene, pa mphindi ziwiri zilizonse, mayi mmodzi amafa pamene ali woyembekezera kapena nthawi imene akubereka chifukwa chosowa thandizo loyenera la chipatala.
Kagawidwe ka katundu ndi malo. Ngakhale kuti azimayi ndi amene amalimbikira kwambiri pa ulimi, m’mayiko ambiri mulibe malamulo oti azimayi azipatsidwa katundu kapena malo.
Kodi n’chifukwa chiyani azimayi amakumana ndi mavuto onsewa? N’chifukwa choti anthu ambiri amatsatira miyambo yachipembedzo komanso zikhalidwe zimene zimalimbikitsa kuchitira nkhanza akazi. M’nyuzipepala ina ya ku France muli mawu a loya wina wa ku India, yemwe anati: “Malamulo a zipembedzo zonse amalimbikitsa kusala akazi.”
Kodi inunso mumaona choncho? Kodi mumaona kuti Baibulo limasonyeza kuti akazi ndi otsika ngati mmene mabuku ambiri achipembedzo amanenera? Anthu ena amaona ngati mavesi ena a m’Baibulo amasonyeza zimenezi. Koma kodi Mulungu, yemwe analemba Baibulo, amaona kuti akazi ndi otsika? Ngakhale kuti anthu ambiri ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi, kufufuza zimene Baibulo limanena kungatithandize kupeza yankho lolondola.