Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ziphuphu Zidzatha

Ziphuphu Zidzatha

“Yembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake . . . Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.”—SALIMO 37:34.

KODI nanunso mumaona kuti n’zosatheka kupewa kuchita ziphuphu? Ndipo mumaona kuti ziphuphu sizidzatha monga mmene anthu ambiri amaganizira? N’zomveka kuganiza choncho. Kuyambira kale, anthu ayesa maboma osiyanasiyana. Komabe iwo alephera kuthetsa ziphuphu. Kodi tingayembekezere kuti pa nthawi ina anthu onse azidzachita zinthu mwachilungamo popanda kuchita ziphuphu?

N’zosangalatsa kudziwa kuti Baibulo limanena kuti Mulungu adzachita zimenezi. Ilo limanena kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa ziphuphu padzikoli. Kodi adzachita motani zimenezi? Iye adzagwiritsira ntchito Ufumu wake, umene ndi boma limene lidzathetse ziphuphu. Ufumu umenewu ndi umene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti aziupempherera. M’pemphero limene limatchedwa Pemphero la Ambuye kapena la Atate Wathu, Yesu anati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Ponena za Yesu Khristu, yemwe ndi Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu, Baibulo linalosera kuti: “Pakuti adzalanditsa wosauka wofuulira thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.” (Salimo 72:12-14) Onani kuti Yesu amamvera chisoni anthu amene amavutika chifukwa cha ziphuphu ndipo adzathetsa kupondereza anthu. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri.

Mu ulamuliro wa Yesu, yemwe ndi wachifundo komanso wamphamvu, Ufumu wa Mulungu udzathetseratu ziphuphu padzikoli. Kodi udzachita bwanji zimenezi? Udzachita zimenezi mwa kuchotsa zinthu zitatu zimene zimayambitsa ziphuphu.

Mphamvu ya Uchimo

Anthufe timalimbana ndi chibadwa chofuna kuchita zinthu zoipa chimene chimatipangitsa kuchita zinthu modzikonda. (Aroma 7:21-23) Komabe pali anthu ena abwino amene amafuna kuchita zoyenera. Iwo amakhulupirira dipo la magazi a Yesu ndipo machimo awo amakhululukidwa. * (1 Yohane 1:7, 9) Anthu amenewa adzapindula kwambiri ndi chikondi chachikulu cha Mulungu monga limanenera lemba la Yohane 3:16 kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

Mulungu adzachitira anthu okhulupirika zinthu zabwino kwambiri. M’dziko latsopano limene likubwera, lomwe mudzakhala anthu okhulupirika okhaokha, Mulungu pang’onopang’ono adzachotsa uchimo ndipo anthu adzakhalanso angwiro ndi olungama. (Yesaya 26:9; 2 Petulo 3:13) Mu Ufumu wa Mulungu uchimo sudzachititsanso anthu kuchita zinthu zoipa ndipo iwo ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda.’—Aroma 8:20-22.

Dziko Loipali

N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu ambiri amasangalala akamavutitsa anthu ena. Iwo amapondereza osauka ndi anthu wamba komanso amachititsa ena kuti azichita zinthu zachinyengo. Baibulo limachenjeza anthu oterewa kuti: “Munthu woipa asiye njira yake ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.” Anthu amenewa atalapa, Baibulo limanena kuti Mulungu ‘angawakhululukire ndi mtima wonse.’—Yesaya 55:7.

Komabe anthu oterewa akapanda kulapa n’kusintha, Mulungu sadzachitira mwina koma kuwawononga. Lonjezo ili la m’Baibulo lidzakwaniritsidwa mu Ufumu wa Mulungu: “Yembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake, . . . Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.” * (Salimo 37:34) Anthu oipa osafuna kusintha njira zawo akadzawonongedwa, anthu okhulupirika sadzavutikanso ndi anthu ochita ziphuphu.

Mphamvu ya Satana Mdyerekezi

Woipa kwambiri pa onse ndi Satana Mdyerekezi. Koma n’zosangalatsa kuti posachedwapa Yehova sadzamulolanso kuti azisocheretsa anthu. M’kupita kwa nthawi Mulungu adzawonongeratu Satana, yemwe ndi wankhanza kwambiri, ndipo Satanayo sadzapangitsanso anthu kuchita zoipa.

Kwa anthu ena mfundo yakuti Mulungu adzathetsa zimene zimayambitsa ziphuphu ingaoneke ngati yosatheka. Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi Mulungu alidi ndi njira imene angathetsere ziphuphu? Ngati ali nayo n’chifukwa chiyani sanazithetse nthawi yonseyi?’ N’zomveka kufunsa mafunso amenewa ndipo dziwani kuti Baibulo lili ndi mayankho ogwira mtima pa nkhaniyi. * Tikukulimbikitsani kuti mufufuze m’Baibulo kuti mudziwe zimene Mulungu adzachite posachedwapa pamene sikudzakhalanso ziphuphu.

^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri ponena za dipo lowombola anthu limene Yesu anapereka kudzera mu imfa yake, werengani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 12 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.