Zimene Owerenga Amafunsa . . .
Kodi Kukhala Ndi Chikhulupiriro N’kusaganiza Bwino?
Munthu yemwe amadzinyenga saona zinthu moyenera komanso amalephera kuganiza bwino. Mwachitsanzo, anthu ena amadzinyenga pa nkhani ya mowa. Iwo amaona kuti kumwa mowa kumawathandiza kuti akhale olimba mtima komanso kuti aiwale mavuto. Koma pamapeto pake, zimawabweretsera mavuto. Kodi chikhulupiriro chingavulaze munthu monga mmene mowa umachitira?
Anthu ena amaganiza kuti kukhala ndi chikhulupiriro n’kuchita zinthu m’chimbulimbuli. Iwo amati anthu amene ali ndi chikhulupiriro safuna kuganiza pa okha kapena sakhala ndi umboni weniweni wa zimene amakhulupirirazo. Amaonanso kuti anthu amene ali ndi chikhulupiriro cholimba sadziwa zolondola.
Baibulo limafotokoza zambiri zokhudza chikhulupiriro. Ndipo palibe vesi lililonse m’Baibulo limene limalimbikitsa kuti munthu azingokhulupirira zilizonse. M’malomwake Baibulo limalimbikitsa kuti munthu ayenera kumaganiza komanso kufufuza kuti adziwe zinthu molondola. Ndiponso limati anthu omwe amangokhulupirira zilizonse ndi osadziwa zinthu kapena opusa. (Miyambo 14:15, 18) Kungakhaledi kupusa kumangokhulupirira zinthu usanafufuze kuti utsimikizire ngati zili zoona. Kuchita zimenezi kungafanane ndi munthu amene akudumpha msewu umene umadutsadutsa magalimoto atatsizina chifukwa chakuti munthu wina wamuuza kuti achite zimenezo.
Baibulo silitilimbikitsa kumangokhulupirira zilizonse, m’malo mwake limatilimbikitsa kuti tiyenera kukhala maso kuti tisanamizidwe. (Mateyu 16:6) Tingadziwe zinthu zoyenera ngati tili ndi “luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1) Baibulo limatiphunzitsa kuti tiyenera kufufuza kaye kuti tipeze umboni wa zimene timakhulupirira. Tiyeni tione zitsanzo zina kuchokera pa zimene mtumwi Paulo analemba.
Pamene Paulo analembera kalata mpingo wa ku Roma, sanafune kuti anthuwo angokhulupirira Mulungu chifukwa choti iye wawauza kuti amukhulupirire. M’malomwake iwo anayenera kufufuza okha umboni wosonyeza kuti Mulungu ndi weniweni. Iye analemba kuti: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo [omwe safuna kuti Mulungu aziwalamulira] alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.” (Aroma 1:20) Paulo anatchulanso mfundo yomweyi pamene analembera Aheberi. Iye anati: “N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheberi 3:4) M’kalata yake imene analembera Akhristu a ku Tesalonika, Paulo anawalimbikitsa kuti asamangokhulupirira zilizonse. Iye ankafuna kuti iwo ‘azitsimikizira zinthu zonse.’—1 Atesalonika 5:21.
Munthu amene amangokhulupirira zinthu popanda umboni wokwanira anganyengedwe mosavuta ndipo akhoza kugwera m’mavuto. Ponena za anthu opembedza a m’nthawi yake, Paulo analemba kuti: “Ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola.” (Aroma 10:2) Choncho n’zothandiza kwambiri kutsatira malangizo amene mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Roma. Iye anati: “Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Chikhulupiriro chimene munthu amakhala nacho chifukwa choti akudziwa zolondola sikuti n’kusaganiza bwino koma m’malomwake chikhulupiriro choterocho chimakhala ngati “chishango chachikulu” chimene chingatiteteze ku zinthu zomwe zingativulaze mwauzimu.—Aefeso 6:16.