Kupatsana Mphatso
“Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—MACHITIDWE 20:35.
Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.
Monga mmene Yesu ananenera, kupatsa kumathandiza kuti munthu wopereka komanso wolandirayo asangalale. Pofuna kupeza chisangalalo chimenechi, anthu ambiri amaona kuti Khirisimasi ndi nthawi yabwino yopatsana mphatso. Mwachitsanzo, kafukufuku wina anasonyeza kuti chaka chatha ku Ireland, ngakhale kuti kunali mavuto azachuma, banja lililonse linkayembekezera kuwononga ndalama zokwana madola 660 a ku America kugula mphatso za Khirisimasi.
Pamene pagona vuto.
Anthu ambiri amaona kuti kugula mphatso za Khirisimasi kumangowawonjezera mavuto m’malo mowathandiza kukhala osangalala. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho? Anthu ambiri amakakamizika kugula mphatso za ndalama zambiri kuposa ndalama zimene amapeza. Komanso popeza kuti pa nthawiyi, anthu ambiri amagula zinthu, m’malo ogulitsira zinthu mumakhala mizere italiitali ndipo izi zimakhala zotopetsa.
Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.
Yesu anati: “Khalani opatsa.” * (Luka 6:38) Iye sananene kuti pali nthawi inayake imene anthu ayenera kupatsana mphatso. M’malomwake iye analimbikitsa otsatira ake kuti akhale ndi chizolowezi chopatsana mphatso nthawi zonse.
“Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” (2 Akorinto 9:7) Buku lina linanena kuti malangizo a Paulo palembali ndi akuti: “Munthu sayenera kupereka kanthu asakufuna ngati kuti wachita ‘kukakamizidwa.’” Mosiyana ndi mmene mphatso za Khirisimasi zimakhalira, “munthu wopereka mokondwera” saona kuti zivute zitani ayenera kupereka mphatso inayake kwa munthu winawake pa nthawi inayake.
“Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe, osati zimene sangathe.” (2 Akorinto 8:12) Mulungu safuna kuti Akhristu azichita kutenga ngongole kuti agulire anzawo mphatso zodula. Koma munthu akagula mphatso mogwirizana ndi “zimene angathe,” mphatso yakeyo imakondweretsa Mulungu. Choncho si bwino kungotsatira zimene otsatsa malonda amanena, chifukwatu iwo amalimbikitsa anthu kuti azigula zinthu pa ngongole.
^ ndime 8 Mabaibulo ena anamasulira lemba limeneli kuti “Patsani.” Koma m’Chigiriki choyambirira, mawu amene anawagwiritsa ntchito amatanthauza kuchita zinthu mopitiriza. Choncho pofuna kupereka tanthauzo lenileni la mawu amene Yesu anagwiritsa ntchito palembali, Baibulo la Dziko Latsopano linamasulira lembali kuti “khalani opatsa.”