Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zinachitika ku Estonia

Zimene Zinachitika ku Estonia

Pa 14 June, 2007, boma la Estonia linatulutsa sitampu imene yasonyezedwa kumanjayi. Potulutsa sitampuyi analengeza kuti: “Sitampu imeneyi yatulutsidwa pofuna kukumbukira anthu amene anazunzidwa ndi ulamuliro wa nkhanza wa Stalin m’dziko muno.” Kuyambira m’chaka cha 1941 mpaka 1951, anthu ambirimbiri a ku Estonia anathamangitsidwa m’dzikolo.

N’ZOSATHEKA kusintha zinthu zimene zinachitika kale. Koma pali zimene tingaphunzire kuchokera pa zinthuzo. Mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Zonsezi ndaziona ndipo mtima wanga unaganizira za ntchito iliyonse imene yachitidwa padziko lapansi pano, pa nthawi imene munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9.

Umboni wakuti Mawu a m’Baibulo amenewa ndi oona, ndi zimene zinachitika zaka zapitazo ku Estonia komanso m’mayiko ena a kum’mawa kwa Ulaya. Maboma a m’mayiko amenewa anazunza anthu ambirimbiri osalakwa komanso anawasamutsa m’mayiko awo n’kuwapititsa kundende kumene ankawagwiritsa ntchito zakalavulagaga.

Malinga ndi zimene olemba mbiri a ku Estonia ananena, kuyambira mu 1941 kukafika 1951, anthu opitirira 46,000 a m’dziko laling’ono limeneli anazunzidwa komanso kuthamangitsidwa m’dzikoli. Ambiri mwa anthuwa ankazunzidwa pa zifukwa zandale, mtundu wawo komanso chifukwa cha udindo umene anali nawo. Koma a Mboni za Yehova ankazunzidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Atumiki a Mulungu Anazunzidwa Kwambiri

Malinga ndi zimene wolemba mbiri wina, dzina lake Aigi Rahi-Tamm ananena m’kafukufuku amene yunivesite ina inachita mu 2004, “kuchokera mu 1948 mpaka mu 1951, a Mboni za Yehova komanso anthu ena amene ankasonkhana ndi Mbonizo okwana 72 anamangidwa. Komabe akuluakulu a boma anakonza zoti athamangitse Mboni zonse pa usiku wa pa 1 April, 1951 ndipo anachitadi zimenezi. Iwo anathamangitsa a Mboni omwe ankakhala ku Estonia, Latvia, Lithuania, Moldova, kumadzulo kwa Ukraine ndi ku Belorussia.”

Chisanafike chaka cha 1951, a Mboni za Yehova ku Estonia ankamangidwa, kufunsidwa mafunso ndi a polisi ndiponso kuikidwa m’ndende. Koma zimene anachita akuluakulu a bomawa mu 1951, cholinga chawo chinali chofuna kuthamangitsa Mboni zonse m’dzikoli.

Sitampu imene yatchulidwa pamwambayi inali ndi deti la 1 April, 1951. Nambala ya 382 imene ili pa sitampuyi, chinali chiwerengero cha a Mboni komanso ana awo omwe anathamangitsidwa pa tsikuli. Chiwerengero chimenechi chikuphatikizaponso achibale komanso anthu ena omwe sanali a Mboni. Pa tsikuli panamangidwa anthu ambirimbiri m’dzikoli. Kutada anthu amene anamangidwawa, akuluakulu ndi ana omwe, anakwezedwa m’mabogi a sitima onyamula ziweto ndipo anawapititsa ku Siberia.

Ella Toom, * yemwe pa nthawiyi anali ndi zaka 25, ndi wa Mboni za Yehova. Iye amakumbukirabe zimene zinachitika pa tsiku limene ankafunsidwa ndi apolisi. Iye anati: “Wapolisi wina anandiopseza n’kundiuza kuti ndisiye kulalikira. Nthawi ina iye anandifunsa kuti: ‘Kodi ukufuna kukhala ndi moyo, kapena ukufuna kukafera ku Siberia ndi Mulungu wakoyo?’” Koma Ella anapitirizabe kulalikira uthenga wabwino mopanda mantha. Iye anatumizidwa ku Siberia ndipo anakhala m’ndende zosiyanasiyana kwa zaka pafupifupi 6.

Mmodzi mwa Mboni zambirimbiri zimene zinathamangitsidwa popanda mlandu wawo kuweruzidwa anali mayi wina, dzina lake Hiisi Lember. Pofotokoza zimene zinachitika usiku wa pa 1 April 1951, iye anati: “Apolisi anangobwera mwadzidzidzi n’kutiuza kuti, ‘Longedzani zinthu zanu msangamsanga ndipo tinyamuka pakangotha mphindi 30.’” Kusanache, Hiisi ndi mwana wake wazaka 6 anawatenga n’kupita nawo ku siteshoni ya sitima. Panali sitima imene inkayenda m’masiteshoni onse n’kumatenga a Mboni. Hiisi anati: “Tinakwezedwa m’bogi yonyamula ziweto. Mwamwayi, ndowe za ziwetozo zinali zitaundana chifukwa cha kuzizira, apo ayi zikanakhala zovuta kwambiri chifukwa tikanasowa poponda. Anangotilowetsa m’bogimo ngati nyama.”

Ulendowu unali wowawa komanso wotopetsa kwambiri ndipo anayenda kwa milungu iwiri. Ankakhala mothithikana m’mabogiwo komanso mabogiwo anali auve. Anangowasakaniza, ana ndi akulu omwe, ndipo zinali zochititsa manyazi kwambiri. Anthu ena ankalira komanso ankakana kudya. Komabe a Mboni ankathandizana ndiponso kulimbikitsana poimba nyimbo zawo zotamanda Mulungu. Iwo ankagawananso chakudya chimene anali nacho. Anthuwa ankauzidwa kuti sadzabwereranso ndipo akafera konko.

Hiisi amakumbukirabe mmene a Mboni anzawo anawathandizira pa nthawi yovuta imeneyi. Iye anati: “Titafika pasiteshoni ina, sitima yathu inaima pafupi ndi sitima yochokera ku Moldova. Tinangomva munthu wina akutifunsa kuti ndife ndani komanso tikupita kuti. Tinamuuza kuti ndife a Mboni za Yehova a ku Estonia koma sitikudziwa kumene tikupita. A Mboni anzathu a ku Moldova anamva zimene tinamuyankha munthuyu. Choncho iwo anatiponyera buledi komanso zipatso.” Hiisi ananenanso kuti: “Tsopano tinazindikira kuti si ife tokha amene tinali titamangidwa. Nawonso a Mboni za Yehova a m’mayiko onse a mu Soviet Union anali atamangidwa.”

Atsikana awiri a Mboni, Corinna ndi mng’ono wake Ene, anali atasiyana ndi mayi awo kwa zaka zoposa 6. Mayi awowo, omwenso anali a Mboni, anali atamangidwa kale m’mbuyomo n’kutumizidwa kundende ina. Ndiyeno pa tsikuli, atsikanawa nawonso anatengedwa limodzi ndi a Mboni amene anaikidwa m’mabogi a sitima aja. Corinna amayamikira zimene mayi wina anawachitira. Iye anati: “Tili m’sitimamo, mayi ena a Mboni, omwenso anali ndi ana awiri, anatiuza kuti azitisamalira ndipo anatitsimikizira kuti tizikakhala nawo limodzi ngati ana awo.”

Kodi chinachitika n’chiyani atafika ku Siberia komwe kunali kozizira kwambiri? Tsiku lotsatira, anthu ochokera m’minda yapafupi anabwera n’kumadzasankha anthu oti azikawagwirira ntchito m’minda yawo ndipo zinkangokhala ngati akugula akapolo. Corinna anafotokoza kuti: “Tinkamva anthuwo akukangana, kuti: ‘Iwe uli kale ndi dalaivala wa thirakitala. Uyu ndi wanga,’ komanso ankati, ‘Ine ndatenga kale anthu awiri okalamba. Iwenso utengeko enawa.’”

Corinna ndi Ene anali atsikana olimba mtima. Ngakhale kuti ankalakalaka kuonananso ndi mayi awo, anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu komanso anali ansangala. Iwo anati: “Tinkalakalaka titaona mayi athu ndiponso kukumbatirana nawo.” Corinna anafotokozanso kuti: “Komabe zinakhala bwino kuti sitinaikidwe ndende imodzi ndi amayi. Iwo akanamva chisoni kwambiri kumationa tikuzizidwa chifukwa nthawi zina tinkagwira ntchito panja kukuzizira kwambiri, tilibe zovala za mphepo.”

Kunena zoona, anthu ambiri osalakwa a ku Estonia komanso madera ena anavutika kwambiri chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zomwe anachitiridwa ndipo ena mwa anthu amenewa anali a Mboni za Yehova. (Onani bokosi lakuti “Zinali ‘Zoopsa Kwambiri.’”) Ngakhale kuti a Mboniwo anazunzidwa choncho pa nthawiyo, panopa Mboni za Yehova zikupezekabe ku Estonia ndipo zikupitiriza kutumikira Mulungu wawo mosangalala.

Zabwino Zili M’tsogolo

Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova Mulungu amadana ndi kupanda chilungamo. Limati: “Aliyense wochita zimenezi, aliyense wosachita chilungamo, n’ngonyansa kwa Yehova Mulungu wako.” (Deuteronomo 25:16) Ngakhale kuti Mulungu analola kuti anthu osalakwa azunzidwe, posachedwapa adzathetsa kupanda chilungamo komanso kuipa konse padzikoli. Baibulo limati: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.

Ndithudi, tikudziwa kuti m’tsogolo tidzasangalala kwambiri. Ngakhale kuti n’zosatheka kusintha zinthu zimene zinachitika kale, zomwe tingachite panopo zingatithandize kudzakhala ndi moyo wosangalala m’tsogolo. Yesetsani kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo phunzirani zimene mungachite kuti nanunso mudzakhale ndi moyo wabwino m’tsogolo, zinthu zopanda chilungamo zikadzatha.—Yesaya 11:9.