Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Kodi dzina la Mulungu ndani?
Achibale athu onse ali ndi mayina. Anthu ena amapereka mayina ngakhale kwa ziweto, ngati galu kapena mphaka. Ndiye kodi si zomveka kuti Mulungu nayenso ali ndi dzina? Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ali ndi mayina ambiri audindo monga Mulungu Wamphamvuyonse, Ambuye Wamkulu Koposa ndi Mlengi. Komabe iye ali ndi dzina lake lenileni.—Werengani Yesaya 42:8.
M’Mabaibulo ambiri dzina la Mulungu limapezeka pa Salimo 83:18. Mwachitsanzo M’Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, lemba limeneli limati: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”
N’chifukwa chiyani tiyenera kutchula dzina la Mulungu?
Mulungu amafuna kuti tizitchula dzina lake tikamanena za iye kapena tikamalankhula naye m’pemphero. Tikamalankhula ndi anthu amene timakondana nawo, monga anzathu apamtima, timatchula dzina lawo, makamaka ngati iwowo anatiuza kuti tiziwatchula dzina. Kodi sitiyenera kuchitanso chimodzimodzi ndi Mulungu? Ndipotu Yesu Khristu analimbikitsa anthu kuti azitchula dzina la Mulungu.—Werengani Mateyu 6:9; Yohane 17:26.
Komabe kuti tikhale mabwenzi a Mulungu, tiyenera kudziwa zambiri zokhudza iye, osati dzina lake lokha. Mwachitsanzo, kodi Mulungu ndi wotani? Kodi n’zotheka kumuyandikira, kapena kuti kukhala naye pa ubwenzi? Mungapeze mayankho a mafunso amenewa m’Baibulo.