Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kwa Owerenga Magazini Athu

Kwa Owerenga Magazini Athu

Magazini ya Nsanja ya Olonda inayamba kufalitsidwa mu July 1879. Kuyambira nthawi imeneyo, zinthu padzikoli zakhala zikusintha ndipo n’chimodzimodzinso ndi magaziniyi. (Onani zithunzi zili pamwambazi.) Kuyambira ndi magazini ya January, Nsanja ya Olonda yasinthanso zina ndi zina. Kodi ndi zinthu ziti zimene zasintha?

Anthu ambiri m’mayiko osiyanasiyana akukonda kuwerenga zinthu pa Intaneti. Iwo amaona kuti njira imeneyi ndi yabwino chifukwa amapeza mosavuta zinthu zambirimbiri zowerenga zimene zimapezeka pa Intaneti pokha. Munthu akhoza kuwerenga mabuku, magazini komanso nyuzipepala pa Intaneti.

Chifukwa cha zimenezi, posachedwapa tasintha zina ndi zina pa Webusaiti yathu ya www.pr418.com kuti munthu azipeza zinthu mosavuta pa Webusaiti yathuyi. Anthu amene amawerenga zinthu pa Webusaitiyi, angawerenge mabuku athu m’zinenero zoposa 430. Komanso kuyambira mwezi wa January, anthu angathenso kuwerenga pa Webusaiti yathuyi nkhani zina zimene poyamba zinkapezeka m’magazini athu koma panopa zizingopezeka pa Webusaitiyi. *

Popeza kuyambira ndi magazini ino, nkhani zina zizipezeka pa Intaneti pokha, Nsanja ya Olonda yogawira yasinthidwa ndipo izikhala ndi masamba 16 okha m’malo mwa masamba 32. Panopa Nsanja ya Olonda imapezeka m’zinenero 195. Koma kusinthaku kuthandiza kuti magaziniyi izipezeka m’zinenero zambiri kuposa pamenepa.

Tikukhulupirira kuti kusintha kumeneku kuthandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wa m’Baibulo womwe ndi wothandiza kuti adzapeze moyo wosatha. Tipitirizabe kuthandiza anthu kudziwa zolondola pogwiritsa ntchito magazini osindikizidwa ndi opezeka pa Intaneti, n’cholinga chothandiza anthu amene amakhulupirira Baibulo ndipo amafuna kudziwa zimene limaphunzitsa.

Ofalitsa

^ ndime 5 Zina mwa nkhani zimene zizipezeka pa Webusaitiyi ndi “Zoti Achinyamata Achite,” komanso “Zimene Ndikuphunzira m’Baibulo.” Nkhani “Zoti Achinyamata Achite,” zimathandiza achinyamata kufufuza zinthu m’Baibulo ndipo “Zimene Ndikuphunzira m’Baibulo,” zinakonzedwa n’cholinga choti zizithandiza makolo kuphunzitsa ana awo a zaka zosapitirira zitatu.