Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO: KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI KWA MOSE?

Kodi Mose Anali Ndani?

Kodi Mose Anali Ndani?

Kodi n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamva dzina loti Mose? Kodi mumaganiza za . . .

  • Mwana amene mayi ake anamubisa m’kabokosi mu mtsinje wa Nailo?

  • Mnyamata amene analeredwa ndi mwana wamkazi wa Farao ku Iguputo koma sanaiwale kuti anali Mwisiraeli?

  • Munthu amene anali m’busa ku Midiyani kwa zaka 40?

  • Munthu amene analankhula ndi Yehova * pachitsamba choyaka moto?

  • Munthu amene analimba mtima kukalankhula ndi mfumu ya Iguputo kuti ilole Aisiraeli kuti amasulidwe ku ukapolo?

  • Munthu amene, motsogozedwa ndi Mulungu, anachenjeza za Miliri 10 imene inagwa m’dziko la Iguputo pamene mfumu yake inakana kumvera Mulungu woona?

  • Munthu amene anatsogolera Aisiraeli pa ulendo wochoka ku Iguputo?

  • Munthu amene Mulungu anamugwiritsa ntchito kulekanitsa madzi a m’Nyanja Yofiira?

  • Munthu amene anapatsa Aisiraeli Malamulo Khumi ochokera kwa Mulungu?

MOSE anachita zonsezi komanso zina zambiri. Choncho, n’zosadabwitsa kuti Mose amalemekezedwa kwambiri ndi Akhristu, Ayuda komanso Asilamu.

Monga taonera, Mose anali mneneri amene anachita “zinthu zazikulu ndi zoopsa.” (Deuteronomo 34:10-12) Iye analola kuti Mulungu amugwiritse ntchito m’njira zosiyanasiyana. Komatu Mose anali munthu ngati ife tomwe. Mofanana ndi mneneri Eliya, amene anaonekera m’masomphenya limodzi ndi Moseyo pamene Yesu anali padziko lapansi, iye anali “munthu monga ife tomwe.” (Yakobo 5:17; Mateyu 17:1-9) Mose anakumana ndi mavuto ofanana ndi amene anthufe timakumana nawo, koma anakhalabe wokhulupirika.

Kodi mukufuna kudziwa zimene zinathandiza Mose? Tiyeni tione makhalidwe atatu amene Mose anali nawo komanso zimene tingaphunzire pa chitsanzo chake.

^ ndime 7 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.