Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Choonadi

Choonadi

Kodi choonadi tingachipeze kuti?

Kodi chingakuthandizeni bwanji inuyo komanso banja lanu?

Tikukuitanani ku msonkhano wa Mboni za Yehova womwe udzachitike masiku atatu ndipo padzakambidwa nkhani zomwe zidzayankha mafunso amenewa.

MUTU WA MSONKHANO:

‘Mawu a Mulungu Ndi Choonadi’

Mutu umenewu wachokera pa Yohane 17:17.

NKHANI ZINA ZA PA MSONKHANOWU:

Nkhani yamutu wakuti “Kodi Choonadi N’chiyani” idzafotokoza chifukwa chake tiyenera kukhulupirira Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu.

Masewero awiri a nkhani zochokera m’Baibulo adzatiphunzitsa mfundo zabwino kwambiri zimene zingatithandize pa moyo wathu.

KODI NDANI AYENERA KUDZAFIKA PA MSONKHANOWU?

Aliyense. Simudzalipiritsidwa ndalama iliyonse komanso pamsonkhanowu sipadzayendetsedwa mbale ya zopereka.

NTHAWI KOMANSO MALO:

Kuti mudziwe kumene kudzachitikire msonkhanowu m’dera lanu fufuzani pa Webusaiti yathu ya www.pr418.com. (Fufuzani pa mawu akuti NKHANI ZOKHUDZA MBONI ZA YEHOVA/MISONKHANO)

Mukhozanso kuona pulogalamu ya msonkhanowu pa Webusaiti ya www.pr418.com. (Fufuzani pa mawu akuti MABUKU/MABUKU NDI MABULOSHA)