Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

”Ndinkafuna Kudzakhala Wansembe”

”Ndinkafuna Kudzakhala Wansembe”
  • CHAKA CHOBADWA: 1957

  • DZIKO: MEXICO

  • POYAMBA: ANALI KU SUKULU YA ANSEMBE KOMANSO SANKACHEDWA KUPSA MTIMA

KALE LANGA:

Ndinabadwira m’tawuni yaing’ono ya Texcoco. Pa nthawi imeneyo misewu yambiri inali yopanda tala komanso yafumbi. Anthu a m’midzi ina ankadzagulitsa zinthu zawo zomwe ankazinyamulira pa abulu. M’banja lathu munali ana 9 ndipo tinali osauka kwambiri. Ine ndinali wanambala 7. Bambo anga ankasoka masilipasi kuti azitha kupeza ndalama. Koma anamwalira ndili ndi zaka 7. Kuyambira pamenepo, mayi anga ankavutika kwambiri kuti apeze chakudya cha banja lonse.

Agogo anga aamuna ankaimba vayolini komanso anali wotsogolera nyimbo makamaka zatchalitchi. Aliyense m’banja mwathu ankadziwa kuimba pogwiritsa ntchito chida. Mayi anga ankaimba nawo kwaya pomwe asuweni anga ankadziwa kuimba mwanthetemya komanso ankaimba piyano. Tinali Akatolika ndipo tonse tinkalimbikira. Ineyo ndinali mnyamata wa Sitefano ndipo ndinkafuna kudzakhala mmishonale wa Katolika. Koma ndinkakonda kuonera mafilimu omenyana ndipo zimenezi zinkachititsa kuti ndisamachedwe kupsa mtima.

Kenako ndinasamukira mumzinda wa Puebla komwe ndinayamba sukulu yophunzitsa za chipembedzo. Zimene zinkachitika pa sukuluyi zinali ngati zimene zimachitika pa sukulu ya ansembe. Ndinayamba sukuluyi n’cholinga choti ndidzakhale wansembe wa Katolika. Koma m’chaka changa chomaliza ndinakhumudwa ndi zimene zinkachitika. Sisitere wina wachitsikana anayamba kundikopa kuti ndigone naye. Ndinakanitsitsa koma zimenezi zinandichititsa kuti ndiyambe kuganiza zokwatira. Komanso ndinkaona kuti ansembe ena ankachita zinthu  mwachinyengo. Kenako ndinasiya kuganiza zoti ndidzakhale wansembe.

Pamene ndinali mnyamata wa Sitefano, ndinkafuna kudzakhala mmishonale wa Katolika koma ndinkakonda kuonera mafilimu achiwawa zomwe zinkachititsa kuti ndisamachedwe kupsa mtima

Ndinayamba kuphunzira nyimbo pasukulu ina ku Mexico City. Nditamaliza maphunziro anga ndinakwatira ndipo patangotha zaka zochepa tinakhala ndi ana anayi. Ndinkaimba nyimbo pa mwambo wa Misa kuti ndizipeza ndalama.

Nditangokwatira, m’banja mwathu munali mavuto osaneneka. Poyamba tinkangolalatirana koma kenako tinayamba kumenyana chifukwa cha nsanje. Zimenezi zinachitika kwa zaka 13, kenako banja linatha.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Ndinakumana ndi a Mboni za Yehova ndisanasiyane ndi mkazi wanga. Iwo anabwera kunyumba kwathu n’kutipempha kuti tikambirane zokhudza Baibulo. Chifukwa chakuti ndinkadziona ngati ndimadziwa zambiri za chipembedzo ndinkawafunsa mafunso kuti ndiwakhaulitse. Ndinkawafunsa mafunso ovuta, amene ineyo ndinkaona ngati alibe mayankho. Koma ndinadabwa kuti anandiyankha funso lililonse kuchokera m’Baibulo. Ndinazindikira kuti ndinkadziwa zochepa kwambiri. Koma sitinapitirize kukambirana chifukwa mkazi wanga ankadana kwambiri ndi Mboni za Yehova komanso chifukwa chakuti ineyo ndinkatanganidwa kwambiri.

Patadutsa zaka zisanu, ndinakumananso ndi Mboni za Yehova. Pa nthawi imeneyi ndinali nditapeza mkazi wina, Elvira, ndipo tinkakhala limodzi. Elvira sankadana ndi Mboni za Yehova ndiye ndinapitiriza kuphunzira Baibulo. Ngakhale ndinkaphunzira, zinanditengera zaka zambiri kuti ndisinthe khalidwe langa loipa.

Ndikupitiriza kuphunzira, ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kutumikira Yehova ndi mtima wanga wonse ndinafunika kusintha. Choyamba, ndinafunika kusiya ntchito yoimba pa mwambo wa Misa, zimene zinkatanthauza kuti ndiyambe kufufuza ntchito ina. (Chivumbulutso 18:4) Ndinkafunikanso kulembetsa ukwati wathu ku boma.

Koma chinthu chimodzi chimene chinandivuta kwambiri chinali kusiya khalidwe langa lokwiya msanga. Malemba awiri anandithandiza kwambiri kuti ndisinthe. Lemba la Salimo 11:5, lomwe limasonyeza kuti Yehova amadana ndi chiwawa, komanso lemba la 1 Petulo 3:7. Lembali limasonyeza kuti ngati ndikufuna kuti Yehova azimva mapemphero anga, ndiyenera kulemekeza mkazi wanga. Ndinkaganizira kwambiri zimene malemba amenewa amanena komanso kupemphera kwa Yehova, ndipo kenako ndinasiya kukwiya msanga.

Baibulo landithandiza kudziwa kuti ndiyenera kulemekeza mkazi wanga ngati ndikufuna kuti Yehova azimva mapemphero anga

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Panopa banja langa ndi losangalala kwambiri. Ndikuyesetsa kuthandiza banja langa kuti likhale lokhulupirika kwa Yehova komanso ndikuyesetsa kuti ndiyambirenso kugwirizana ndi ana anga aamuna amene ndinabereka ndi mkazi wanga woyamba.

Ndili mwana ndinkafuna kudzakhala wansembe kuti ndizidzathandiza anthu. Koma panopa ndi pamene ndimaona kuti ndine wosangalala kwambiri. Ndimaphunzitsa anthu kuyimba nyimbo kuti ndizipeza ndalama zosamalira banja langa. Komanso ndimathokoza kuti Yehova anandilezera mtima kuti ndisinthe n’kukhala munthu wabwino.