Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA

N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Ofotokozedwa M’Baibulo Sanatchulidwe Mayina Awo?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Ofotokozedwa M’Baibulo Sanatchulidwe Mayina Awo?

Buku la Rute limanena za munthu wina amene anakana kugula munda wa Elimeleki. Zimene anachita munthuyo zinali zosemphana ndi chilamulo cha Mose. Munthuyo anangotchulidwa kuti Uje. (Rute 4:1-12) Kodi zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene mayina awo sanatchulidwe m’Baibulo anali anthu oipa kapena osafunika?

Ayi. Kuti timvetse, tiyeni tione chitsanzo china. Pokonzekera Pasika womaliza, Yesu anauza ophunzira ake kuti “pitani mumzinda kwa Munthu wakutiwakuti.” Iye ankafuna kuti akachite mwambo umenewu ndi ophunzira ake m’nyumba mwa munthuyo. (Mateyu 26:18) Kodi tinganene kuti munthu amene anangotchulidwa kuti “wakutiwakuti” pa lembali anali woipa kapena wosafunika? Ayi, n’kutheka kuti munthuyu anali wophunzira wa Yesu. Dzina la munthuyu silinatchulidwe chifukwa silinali lofunika kwambiri mu nkhaniyi.

Ndipotu m’Baibulo muli anthu oipa omwe mayina awo anatchulidwa koma anthu ena abwino sanatchulidwe mayina awo. Mwachitsanzo, Baibulo linatchula dzina la mkazi woyambirira kuti anali Hava. Koma chifukwa chodzikonda komanso kusamvera, anachititsa kuti Adamu achimwe, zomwe zinabweretsa mavuto aakulu kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Koma mosiyana ndi zimene Hava anachita, mkazi wa Nowa anachita zinthu mosadzikonda komanso anali womvera ndipo anathandiza mwamuna wake kugwira ntchito yofunika kwambiri. Koma Baibulo silinatchule dzina lake. Zimenezi sizikusonyeza kuti mkazi wa Nowa anali woipa kapena wosafunika.

Palinso anthu ena, omwe Baibulo silinatchule mayina awo, koma anachita zinthu zofunika kwambiri pokwaniritsa chifuniro cha Yehova. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za mtsikana wa ku Isiraeli yemwe anali kapolo wa Namani mkulu wa asilikali a Siriya. Mtsikanayu anauza molimba mtima mkazi wa Namani za mneneri wa Yehova yemwe anali ku Isiraeli. Zimenezi zinathandiza kuti Namani achiritsidwe. (2 Mafumu 5:1-14) Winanso ndi mwana wamkazi wa Yefita, yemwe anasonyeza chitsanzo chabwino chokhala ndi chikhulupiriro. Analolera kukhala wosakwatira komanso kukhala wopanda ana n’cholinga choti akwaniritse lonjezo limene bambo ake anapanga kwa Yehova. (Oweruza 11:30-40) Palinso anthu ena oposa 40, omwe analemba masalimo, amene mayina awo sanatchulidwe m’Baibulo. Enanso ndi aneneri amene anachita mokhulupirika zimene Mulungu anawatuma.—1 Mafumu 20:37-43.

Chitsanzo chinanso ndi cha angelo okhulupirika. Pali angelo mamiliyoni ambirimbiri koma Baibulo limatchula mayina a angelo awiri okha, Gabirieli ndi Mikayeli. (Danieli 7:10; Luka 1:19; Yuda 9) Angelo ena onse sanatchulidwe mayina awo. Mwachitsanzo, Manowa, yemwe anali bambo ake a Samisoni, anafunsa mngelo wina kuti: “Dzina lanu ndani? Tikufuna tidzakulemekezeni mawu anu akadzakwaniritsidwa.” Koma modzichepetsa mngeloyo anakana kulandira ulemu umene uyenera kupita kwa Mulungu.—Oweruza 13:17, 18.

Baibulo silimatchula chifukwa chimene anthu ena anatchulidwa mayina pomwe ena sanatchulidwe. Komabe tingaphunzire zambiri kwa anthu okhulupirika omwe anatumikira Mulungu ndi mtima wosafuna kutchuka.