Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Kodi mabanja angatani kuti azikhala osangalala?
Malangizo a m’Baibulo okhudza banja amathandiza kuti banja likhale losangalala chifukwa malangizowo amachokera kwa Yehova Mulungu, yemwe anayambitsa ukwati. Baibulo limatiphunzitsa kuti tizikhala ndi makhalidwe abwino amene angapangitse kuti banja likhale losangalala. Komanso limatichenjeza kuti tizipewa makhalidwe oipa amene angasokoneze banja lathu. Baibulo limatiphunzitsanso zimene tingachite kuti tizilankhulana bwino m’banja zomwe zimathandizanso kuti banja likhale losangalala.—Werengani Akolose 3:8-10, 12-14.
Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kulemekezana. Aliyense akamakwaniritsa udindo umene Mulungu anam’patsa, banja lawo limakhala losangalala.—Werengani Akolose 3:18, 19.
N’chiyani chingathandize kuti banja likhale lolimba?
Banja likhoza kukhala lolimba ngati mkazi ndi mwamuna amakondana. Mulungu komanso Yesu ndi chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Iwo amadzipereka kwambiri posonyeza chikondi.—Werengani 1 Yohane 4:7, 8, 19.
Banja likhoza kukhala lolimba ngati mwamuna ndi mkazi amaona kuti Mulungu ndi amene anayambitsa banja. Mulungu safuna kuti banja lizitha n’cholinga choti anthu a m’banjamo azikhala otetezeka. Mulungu anapanga amuna ndi akazi m’njira yoti azigwirizana pochita zinthu. Anawapanganso m’chifaniziro chake kuti azimutsanzira posonyezana chikondi.—Werengani Genesis 1:27; 2:18, 24.