Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

“Yehova Anakukhululukirani ndi Mtima Wonse”

“Yehova Anakukhululukirani ndi Mtima Wonse”

“Munthu amene sakhululukira anzake amakhala akuphwasula mlatho woti adutsepo yekha.” Mawu amenewa, ananenedwa ndi katswiri wina wa ku Britain wa mbiri yakale yemwe anakhalapo m’zaka za m’ma 1600. Katswiriyu dzina lake ndi Edward Herbert ndipo mawu amene ananenawa amasonyeza chifukwa chake tiyenera kukhululukira ena. Tiyenera kukhululuka chifukwa nafenso tsiku lina tidzafuna kuti ena atikhululukire. (Mateyu 7:12) Koma pali chifukwa china chachikulu chimene tiyenera kukhululukira ena. Taonani mawu amene mtumwi Paulo ananena omwe ali pa Akolose 3:13.—Werengani.

Chifukwa chakuti tonse ndife ochimwa, timalakwira ena kapena timachita zinthu zowakhumudwitsa ndipo nawonso akhoza kutilakwira. (Aroma 3:23) Ndiye kodi tingatani kuti tizikhalabe pa mtendere ndi anthu ena? Mulungu anauzira Paulo kulemba kuti tizikhala ololerana komanso kuti tizikhululukirana. Malangizo amenewa ndi othandizanso kwa ife, ngakhale kuti analembedwa zaka 2,000 zapitazo. Tiyeni tione zimene Paulo ankatanthauza.

“Pitirizani kulolerana.” Buku lina linanena kuti Akhristu amasonyeza kulolerana “akamayesetsa kunyalanyaza makhalidwe osasangalatsa a anthu ena kapena kunyalanyaza zimene anthu ena awalakwira.” Mawu akuti “kulolerana” amasonyeza kuti aliyense ayenera kusonyeza khalidwe limeneli kwa mnzake. Zimenezi zikutanthauza kuti, tikakumbukira kuti nafenso tili ndi makhalidwe enaake amene anthu ena samasangalala nawo, sitingakhumudwe ndi makhalidwe awo. Zimenezi zimathandiza kuti tikhale pa mtendere ndi anthu ena. Koma kodi tingatani ngati munthu wina watilakwira?

“Pitirizani . . . kukhululukirana ndi mtima wonse.” Wolemba mabuku wina ananena kuti mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “kukhululukirana ndi mtima wonse” “samangotanthauza kukhululuka basi . . . koma ndi mawu amphamvu kwambiri osonyeza kukhululuka ngakhale munthu wina atakulakwira kwambiri komanso mobwerezabwereza.” Buku lina linanenanso kuti mawu amenewa akhoza kutanthauzanso “kuchitira munthuyo zinthu zabwino komanso zomuthandiza.” Timasonyeza kuti ndife anthu achifundo ngati timakhululukira anzathu kuchokera pansi pa mtima ngakhale titakhala kuti tili ndi ‘chifukwa chowadandaulira.’ Koma n’chifukwa chiyani tiyenera kukhululukirana ndi mtima wonse? Chifukwa chimodzi n’chakuti nafenso tsiku lina tidzafuna kuti ena atikhululukire.

“Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” Chifukwa chachikulu chimene tiyenera kukhululukira ena n’chakuti Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse. (Mika 7:18) Tangoganiza zimene Yehova amachita ndi anthu amene alapa kuchokera pansi pa mtima. Yehova ndi wosiyana ndi anthufe chifukwa iye samachimwa ndipo sangafunikire kuti anthu amukhululukire. Komabe ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu amene alapa moona mtima. Choncho, Yehova ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yokhululukira anthu amene alapa.

Yehova ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yokhululukira anthu amene alapa

Chifundo chimene Yehova amatisonyeza chimatipangitsa kuti tizimuyandikira komanso kuti tizitengera chitsanzo chake. (Aefeso 4:32–5:1) Ndiye tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Popeza Yehova amandikhululukira ndi mtima wonse ndikamulakwira, kodi inenso ndimakhululuka anthu amene andilakwira akapepesa?’—Luka 17:3, 4.