Akufa Adzaukitsidwa
Kodi mumakhulupirira zimene Baibulo limanena zoti akufa adzauka? * Chiyembekezo choti tidzaonananso ndi abale athu amene anamwalira, ndi chosangalatsa kwambiri. Koma kodi zimenezi zidzachitikadi? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambirane chitsanzo cha atumwi a Yesu Khristu.
Atumwi ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti akufa adzauka. Panali zifukwa ziwiri zimene zinkawapangitsa kukhulupirira zimenezi. Choyamba, iwo ankadziwa zoti Yesu anaukitsidwa. Pa nthawi ina, atumwiwo komanso “abale oposa 500” anamuona Yesu ataukitsidwa. (1 Akorinto 15:6) Komanso nkhani yoti Yesu anaukitsidwa inali ponseponse moti anthu onse 4 amene analemba Mauthenga Abwino analemba za nkhaniyi.—Mateyu 27:62–28:20; Maliko 16:1-8; Luka 24:1-53; Yohane 20:1–21:25.
Chachiwiri, atumwi ankadziwa kuti Yesu anaukitsapo anthu atatu. Munthu woyamba anali wa ku Naini, wina wa ku Kaperenao ndipo wina wa ku Betaniya. (Luka 7:11-17; 8:49-56; Yohane 11:1-44) Munthu wachitatuyu nkhani yake ndi imene yafotokozedwa koyambirira kwa magaziniyi ndipo anali mnzake wa Yesu. Tiyeni tikambiranenso bwinobwino zimene zinachitika.
“INE NDINE KUUKA”
“Mlongo wako adzauka.” Yesu anauza Marita mawu amenewa patatha masiku 4 kuchokera pamene mlongo wake, Lazaro, anamwalira. Poyamba Marita sanadziwe bwinobwino zimene Yesu ankatanthauza. Iye ankaganiza kuti Yesu akutanthauza kuti Lazaro adzaukitsidwa m’tsogolo. Choncho anayankha kuti: “Ndikudziwa kuti adzauka.” Koma Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” Ndiye taganizirani mmene Marita anasangalalira ataona kuti Yesu waukitsa mlongo wakeyo.—Yohane 11:23-25.
Kodi Lazaro anali ali kuti pa masiku 4 amene anali atafa? Lazaro ataukitsidwa, sananene kuti anali ndi moyo kwinakwake pa masiku 4 amenewo. Choncho Lazaro analibe mzimu wosafa umene unapita kumwamba. Pamene Yesu anaukitsa Lazaro sikuti anamuchotsa kumwamba komwe ankasangalala ndi Mulungu. Ndiye kodi Lazaro anali kuti pamene anamwalira? Iye anali atagona m’manda.—Mlaliki 9:5, 10.
Kumbukirani kuti Yesu anayerekezera imfa ndi tulo, ndipo kuti munthu akhalenso ndi moyo amafunika kuukitsidwa. Nkhaniyi imati: “‘Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.’ Pamenepo ophunzirawo anati: ‘Ambuye, ngati iye akupumula, apeza bwino.’ Apa Yesu anali kunena za imfa yake. Koma iwo anaganiza kuti anali kunena za kugona tulo teniteni. Choncho, Yesu tsopano anawauza momveka bwino kuti: ‘Lazaro wamwalira.’” (Yohane 11:11-14) Pamene Yesu anaukitsa Lazaro, anachititsa kuti Lazaroyo akhalenso ndi moyo n’kuyambanso kukhala ndi abale ake. Banjali liyenera kuti linasangalala kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi.
Zimene Yesu anachita, poukitsa anthu zikusonyeza zimene adzachite m’tsogolo monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. * Yesu akadzayamba kulamulira dziko lapansili, adzaukitsa anthu amene anamwalira, omwe tingati akugona m’manda. N’chifukwa chake iye anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” Taganizirani mmene mudzasangalalire anthu onse amene munkawakonda akadzaukitsidwa. Komanso taganizirani mmene anthu oukitsidwawo adzasangalalire.—Luka 8:56.
Taganizirani mmene mudzasangalalire onse omwe munkawakonda akadzaukitsidwa
ANTHU ACHIKHULUPIRIRO ADZAKHALA NDI MOYO WOSATHA
Yesu anauza Marita kuti: “Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali moyo ndi kukhulupirira mwa ine sadzafa ayi.” (Yohane 11:25, 26) Anthu amene Yesu adzawaukitse mu Ufumu wake wa zaka 1,000, adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha ngati adzakhulupirire Yesu.
“Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo.”—Yohane 11:25.
Yesu atalankhula mawu osangalatsa amenewa, okhudza kuukitsa anthu, anafunsa Marita kuti: “‘Kodi ukukhulupirira zimenezi?’ Iye anayankha kuti: ‘Inde, Ambuye. Ndimakhulupirira kuti ndinu Khristu Mwana wa Mulungu.’” (Yohane 11:26, 27) Kodi inunso mukufuna kukhala ndi chikhulupiriro choti akufa adzauka ngati chimene Marita anali nacho? Chinthu choyamba chimene mungachite ndi kuphunzira za cholinga cha Mulungu chokhudza anthu. (Yohane 17:3; 1 Timoteyo 2:4) Ndipo zimenezi zingachititse kuti mukhale ndi chikhulupiriro. Funsani a Mboni za Yehova kuti akusonyezeni zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi. Iwo adzasangalala kukambirana nanu za chiyembekezo chosangalatsa chakuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo.
^ ndime 2 Onani nkhani yakuti “Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo” patsamba 6.
^ ndime 9 Kuti mudziwe zambiri zimene Baibulo limalonjeza zokhudza anthu amene anamwalira, werengani mutu 7 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.