NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI ZINTHU ZITI ZIMENE MULUNGU WAKUCHITIRANI?
Mwambo Womwe Simuyenera Kuuphonya
Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu analamula ophunzira ake kuti azichita mwambo wokumbukira imfa yake. Yesu anagwiritsa ntchito mkate wopanda chofufumitsa komanso vinyo wofiira, ndipo anayambitsa mwambo umene umatchedwa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Iye analamula ophunzira ake kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”—Luka 22:19.
Chaka chilichonse, pa tsiku limene Yesu anayambitsa mwambowu, Mboni za Yehova padziko lonse zimasonkhana kuti zikumbukire imfa ya Yesu. Chaka chino, mwambowu udzachitika Lolemba pa April 14, dzuwa litalowa.
Tikukuitanani kuti mudzapezeke pa mwambo umenewu. Padzakambidwa nkhani imene idzafotokoze kufunika kwa nsembe ya Yesu. Simudzalipira chilichonse pa mwambowu, ndipo sipadzayendetsedwa mbale ya zopereka. Mungafunse munthu amene wakupatsani magaziniyi kuti mudziwe nthawi komanso malo amene mwambowu udzachitikire m’dera lanu, kapena mungapite pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. Tikukupemphani kuti mulembe deti limene mwambo umenewu udzachitike kuti musadzalephere kupezekapo.