Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Yesu?

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Yesu?

Nkhani ili m’munsiyi ikusonyeza mmene a Mboni za Yehova amachitira akamakambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti abambo ena a Mboni, dzina lawo a Ben, afika pakhomo pa a Tim.

KUKHULUPIRIRA YESU N’KOFUNIKA

A Ben: Muli bwanji a Tim? Ndasangalala kuti ndakupezaninso muli pakhomo lero.

A Tim: Inenso ndasangalala kwambiri kukuonani.

A Ben: Ndakubweretserani magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndikukhulupirira musangalala nawo.

A Tim: Zikomo kwambiri. Ndipotu ndasangalala kwambiri kuti mwabwera chifukwa ndili ndi funso.

A Ben: Owoo, funso lake ndi lotani?

A Tim: Tsiku lina ndikucheza ndi mnzanga wa kuntchito ndinamuuza za magazini amene munandipatsa aja, ndipo ndinamufotokozera kuti muli nkhani zosangalatsa kwambiri. Koma anandiuza kuti ndisamawerenge magazini anu chifukwa choti a Mboni za Yehova simukhulupirira Yesu. Zimenezi zinandidabwitsa kwambiri moti ndinamuuza kuti tikadzakumananso ndidzakufunsani ngati zili zoona. Eti n’zoonadi kuti simukhulupirira Yesu?

A Ben: Ndasangalala kuti mwandifunsa funso limeneli. Chimene chandisangalatsa kwambiri n’choti mwafunsa wa Mboni. Zimachita bwino kufunsa mwiniwake kusiyana ndi kufunsa munthu wina.

A Tim: Inenso ndimaona choncho.

A Ben: Koma zoona n’zakuti a Mboni za Yehova timakhulupirira kwambiri Yesu. Ndipotu timaona kuti kukhulupirira Yesu n’kofunika kwambiri kuti tidzapulumuke.

A Tim: Inenso ndimaona kuti muyenera kuti mumakhulupirira Yesu. Koma ndinadabwa mnzanga wa kuntchito akundiuza kuti simukhulupirira Yesu. Ndimafuna kudziwa ngati zimenezi zilidi zoona. Ndikukhulupirira kuti nkhaniyi sitinakambiranepo.

A Ben: Bwanji ndikusonyezeni malemba m’Baibulo amene amanena za kufunika kwa kukhulupirira Yesu. Malemba amenewa ndi amene a Mboni za Yehova amakonda kuwerenga akamaphunzitsa anthu Baibulo.

A Tim: Zingakhale bwinodi kuwawerenga.

A Ben: Tingachite bwino kuyamba ndikuwerenga zimene Yesu ananena palemba la Yohane 14:6. Mawuwa Yesu ankauza mtumwi wake wina. Iye anati: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” Malinga ndi lembali, kodi ndi njira yokha iti imene tingafikire kwa Atate?

A Tim: Tiyenera kudzera mwa Yesu.

A Ben: Mwalondola. Ndipo izi n’zimene a Mboni za Yehova timakhulupirira. Koma n’takufunsani, mogwirizana ndi zimene mumadziwa, kodi Mulungu amafuna kuti tikamapemphera, tizipemphera kudzera mwa ndani?

A Tim: Kudzera mwa Yesu.

A Ben: N’zoonadi. N’chifukwa chake sindilephera kutchula kuti m’dzina la Yesu ndikamapemphera. Izi n’zimene wa Mboni aliyense amachita popemphera.

A Tim: N’zochititsa chidwi kudziwa zimenezi.

A Ben: Lemba lina limene tingawerenge ndi la Yohane 3:16. Vesi limeneli ndi lofunika kwambiri chifukwa Uthenga Wabwino wonse uli m’vesili. Ngati titatenga zonse zimene zinalembedwa zokhudza moyo wa Yesu ali padziko lapansi n’kuziika m’lemba limodzi, tikhoza kunena kuti lemba lake ndi limeneli. Mwina mungakonde kuwerenga lembali.

A Tim: Chabwino. Likunena kuti: “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

 A Ben: Zikomo kwambiri. Kodi mukulidziwa bwino lembali?

A Tim: Inde, ndikulidziwa chifukwa ndakhala ndikumva anthu ambiri akunena mawu a palembali ndiponso ndimaliona litalembedwa pamalo osiyanasiyana monga pazikwangwani ndiponso pamagalimoto.

A Ben: Ndi lembadi lodziwika kwa anthu ambiri. Komatu mukaliganizira bwinobwino likusonyeza kuti, chikondi cha Mulungu n’chimene chinapangitsa kuti anthufe tikhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Koma kodi lembali likusonyeza kuti tingadzapeze moyo wosatha umenewu pokhapokha titachita chiyani?

A Tim: Pokhapokha titakhala ndi chikhulupiriro.

A Ben: N’zoona. Makamaka titakhulupirira Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu wobadwa yekha. Ndipotu mfundo imeneyi, yoti kukhulupirira Yesu n’kumene kungatithandize kudzapeza moyo wosatha, yafotokozedwa bwino patsamba 2 la magazini a Nsanja ya Olonda amene ndakubweretseraniwa. Ponena za Nsanja ya Olonda, patsambali pamati cholinga cha magaziniwa ‘n’kulimbikitsa anthu kukhulupirira Yesu Khristu amene anatifera kuti tipeze moyo wosatha ndipo panopo akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.’

A Tim: Aaa, sindimadziwa kuti m’magazini anu omwewa muli umboni wosonyeza kuti a Mboninu mumakhulupirira Yesu.

A Ben: Mwaonatu.

A Tim: Nanga n’chifukwa chiyani anthu amanena kuti inu simukhulupirira Yesu?

A Ben: Pangakhale zifukwa zosiyanasiyana zimene anthu amanenera zimenezi. Anthu ena amanena zimenezi chifukwa chongomva kwa anthu ena. Pomwe ena amakhala kuti anachita kuuzidwa ndi abusa a kutchalitchi kwawo.

A Tim: Komadi n’zoona. Koma ndikuonanso kuti anthu ena amaganiza kuti simukhulupirira Yesu chifukwa choti mumati ndinu Mboni za Yehova, osati Mboni za Yesu.

A Ben: Chimenechonso chingakhaledi chifukwa china.

A Tim: Nanga n’chifukwa chiyani mumalankhula kwambiri za Yehova?

“INE NDACHITITSA KUTI IWO ADZIWE DZINA LANU”

A Ben: Chifukwa china n’choti timakhulupirira kuti n’kofunika kugwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu, ngati mmene Mwana wake, Yesu anachitira. Taonani mawu amene Yesu ananena popemphera kwa Atate wake. Mawuwa ali pa Yohane 17:26. Kodi mungawerenge lembali?

A Tim: Ee, ndikhoza kuwerenga: Likuti: “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”

A Ben: Zikomo kwambiri. Lembali likuti Yesu anachititsa kuti anthu adziwe dzina la Mulungu. Kodi mukuganiza kuti anachita bwanji zimenezi?

A Tim: Hmm. Sindikudziwa.

Kukhulupirira Yesu n’kofunika kwambiri kuti tidzapulumuke

A Ben: Chabwino, mwina tiwerenge lemba lina lomwe lingatithandize kudziwa mmene anachitira zimenezi. Ndikuganiza kuti lemba limene lingatithandize ndi la Machitidwe 2:21. Lembali limati: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” Ndikukhulupirira kuti ngati inunso mukuona kuti kuitana pa dzina la Yehova n’kofunika kuti munthu apulumuke, ndiye kuti Yesu ankaidziwanso bwino mfundo imeneyi.

A Tim: N’zoona.

A Ben: Choncho chifukwa choti chipulumutso chagona pamenepa, n’chifukwa chake Yesu anaona kuti n’kofunika kuti otsatira ake adziwe dzina la Yehova komanso azilitchula. N’chifukwa chaketu timakonda kulankhula za Yehova. Timaona kuti n’kofunika kudziwitsa anthu dzina la Mulungu, ndipo timakhulupirira kuti zimenezi zingathandize kuti ayambe kuitanira pa dzinalo.

A Tim: Koma ndikuona kuti ngakhale zitakhala kuti anthu sadziwa dzina la Mulungu ndipo samalitchula, amakhalabe akupemphera kwa Mulungu yemweyo.

A Ben: Zimenezi zikhoza kukhala zoona. Komabe potiuza dzina lake, Mulungu anasonyeza kuti akufuna tikhale naye pa ubwenzi.

 A Tim: Mukutanthauza chiyani pamenepa?

A Ben: Taganizirani chitsanzo ichi: Mwina munthu angaganize kuti panalibe chifukwa chotchulira dzina la Mose m’Baibulo. Bwenzi tikungomutchula kuti, munthu amene anagawanitsa Nyanja Yofiira kapena amene anapatsidwa Malamulo Khumi. N’chimodzimodzinso ndi Nowa. Munthu angaganize kuti sizofunika kudziwa dzina lake. Tikhoza kumangoti, munthu amene anamanga chingalawa n’kuthandiza kuti nyama komanso anthu a m’banja lake apulumuke. Ndiye kuti Yesu Khristu nayenso bwenzi akungodziwika kuti, munthu amene anachokera kumwamba n’kudzatifera chifukwa cha machimo athu. Si choncho?

A Tim: Zoona, inenso ndikuganiza choncho.

A Ben: Komatu Mulungu anaonetsetsa kuti tidziwe mayina a anthu amenewa. Kudziwa dzina lenileni la munthu amene anachita zinazake, kumatithandiza kutsimikiza kuti nkhaniyo ndi yoona. Ngakhale kuti sitinaone Mose, Nowa komanso Yesu, kudziwa mayina awo kumatithandiza kudziwa kuti anali anthu enieni.

A Tim: Ndinali ndisanaganizirepo zimenezi. Koma ndikuona kuti n’zoona.

A Ben: Chimenechi n’chifukwa chinanso chimene a Mboni za Yehova amakondera kutchula dzina la Mulungu. Timafuna kuthandiza anthu kuti azikhulupirira kuti Yehova ndi weniweni ndipo angathe kukhala naye pa ubwenzi. Koma timathandizanso anthu kuti adziwe kuti Yesu ndi wofunika kwambiri kuti tidzapulumuke. Mwina tiwerengenso lemba limodzi limene lingakuthandizeni kumvetsa mfundo imeneyi.

A Tim: Chabwino.

A Ben: Poyamba paja tinawerenga Yohane 14:6, pamene Yesu ananena kuti: “Ndine njira, choonadi ndi moyo.” Koma panopa tiyeni tiwerenge chaputala 14 chomwe chija, koma tiwerenge pavesi 1 kuti tione zimene ananena. Kodi mungakonde kuwerenga mbali yomaliza ya vesili?

A Tim: Ndikhoza kuwerenga. Mbali yomalizira ya lembali ikuti: “Khulupirirani Mulungu, khulupiriraninso ine.”

A Ben: Zikomo kwambiri. Kodi mungati vesili likusonyeza kuti ndi nkhani yoti tisankhe amene tiyenera kum’khulupirira pakati pa Yesu ndi Yehova?

A Tim: Ayi. Yesu anati tiyenera kukhulupirira onse, Yehova komanso iyeyo.

A Ben: Mwayankha bwino. Koma ndikukhulupirira kuti inunso mukudziwa kuti kungonena kokha kuti timakhulupirira Mulungu ndi Yesu sikokwanira. Tiyenera kuchita zinthu zogwirizana ndi zimene timakhulupirirazo.

A Tim: Zimenezi n’zoonadi.

A Ben: Komano kodi munthu angasonyeze bwanji kuti amakhulupiriradi Mulungu ndi Yesu? Bwanji ndidzabwerenso kuti tidzakambirane yankho la funso limeneli? *

A Tim: Ndingasangalale kudzakambiranadi funso limeneli.

Kodi pali nkhani inayake ya m’Baibulo imene simumaimvetsa? Kapena mumafuna mutadziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira? Ngati ndi choncho, funsani a Mboni za Yehova ndipo adzasangalala kwambiri kukambirana nanu.

^ ndime 60 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 12 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.