Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera?
Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye momasuka komanso nthawi zonse, n’kumuuza mavuto athu. (Luka 18:1-7) Tikamapemphera amamvetsera chifukwa amatidera nkhawa. Ndiye popeza Atate wathu wakumwamba amatilimbikitsa kuti tizimuuza mavuto athu, tiyeneradi kumapemphera kwa iye.—Werengani Afilipi 4:6.
Sikuti tiyenera kupemphera pa nthawi yokha imene tikufuna kuti Mulungu atithandize zinazake. Tizidziwanso kuti pemphero limatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu. (Salimo 8:3, 4) Tikamauza Yehova zakukhosi kwathu nthawi zonse, timayamba kumuona kuti ndi mnzathu wapamtima.—Werengani Yakobo 4:8.
Kodi tizipemphera bwanji?
Mulungu safuna kuti tikamapemphera tizinena mawu odzionetsera kapena kunena mapemphero oloweza. Safunanso kuti tizichita kukhala mwa njira inayake tikamapemphera. Chofunika kwambiri kwa iye n’choti tizipemphera kuchokera pansi pa mtima. (Mateyu 6:7) Mwachitsanzo, Hana yemwe ankakhala ku Isiraeli wakale, pa nthawi ina anapemphera zokhudza mavuto a m’banja lake. Yehova atayankha pemphero lake, iye anasangalala kwambiri ndipo anapempheranso kwa Mulungu n’kumuthokoza kuchokera pansi pa mtima.—Werengani 1 Samueli 1:10, 12, 13, 26, 27; 2:1.
Tilitu ndi mwayi waukulu woti tingathe kupemphera kwa Mlengi wathu n’kumuuza zimene zikutidetsa nkhawa. Tingathenso kumutamanda ndi kumuthokoza pa zabwino zimene amachita. Choncho tiyenera kupemphera nthawi zonse posonyeza kuti timayamikira mwayi umenewu.—Werengani Salimo 145:14-16.