Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi anthu akale ankatani kuti sitima zawo zisamalowe madzi?

Katswiri wina wodziwa za sitima zapamadzi, dzina lake Lionel Casson, ananena zimene Aroma ankachita akamaliza kupanga sitima. Iye ananena kuti anthu ambiri ankakonda “kupaka phula malo onse amene matabwa alumikizana. Enanso ankapaka phulalo mkati monse ndi kunja komwe.” Kale kwambiri Aroma asanayambe kuchita zimenezi, anthu a ku Siriya ndi a ku Babulo ankapakanso sitima zawo phula.

Phula laphalaphala ngati ili linkapezeka lambirimbiri m’madera otchulidwa m’Baibulo

Malemba Achiheberi amatchulanso za phula pa Genesis 6:14. Phulali linkapezeka lambiri chifukwa linkatuluka lokha m’nthaka.

Phula lina linkakhala lolimba ndipo lina linkakhala laphalaphala. Anthu opanga sitima ankakonda kugwiritsa ntchito phula laphalaphalali chifukwa silinkafunikanso kulisungunula. Phulali likauma linkalimba zedi ndipo zimenezi ndi zimene zinkathandiza kuti madzi asamalowe.

Phula linkapezeka lambiri m’madera otchulidwa m’Baibulo. Mwachitsanzo chigwa cha Sidimu, chomwe chinali pafupi ndi nyanja yakufa, “chinali ndi maenje aphula ambirimbiri.”—Genesis 14:10.

Kodi kale anthu ankatani akafuna kusunga nsomba kuti zisawonongeke?

Kuyambira kale kwambiri, anthu akhala akuona kuti nsomba ndi chakudya chofunika. Atumwi ena a Yesu, poyamba anali asodzi pa nyanja ya Galileya. (Mateyu 4:18-22) Nsomba zina zimene anthuwa ankapha, ankakazikonza pamalo ena chapafupi kuti zikhale nthawi yaitali zisanawonongeke.

Thabwa losonyeza asodzi a ku Iguputo

Njira imene anthu a ku Galileya ankagwiritsa ntchito kuti nsomba zawo zisawonongeke imagwiritsidwabe ntchito masiku ano m’madera ena. Asodzi akapha nsomba, choyamba ankazichotsa matumbo kenako n’kuzitsuka. Bukuli limanena kuti “akatero ankaziika mchere m’malakhwi, mkamwa ndi m’mamba. Kenako ankaziyanika padzuwa kuti ziume. Pakadutsa masiku 5, ankazitembenuza n’kuzisiyabe padzuwa pompo kwa masiku enanso 5. Pakutha pa masiku amenewa, mchere uja unkakhala utalowerera ndipo nsombazi zinkakhala zitauma gwa.”—Studies in Ancient Technology.

Sizikudziwika kuti nsombazi akazichita zimenezi zinkakhala nthawi yaitali bwanji zisanawonongeke. Komabe, popeza anthu akale a ku Iguputo ankatumiza nsomba zoterezi ku Siriya, ndiye kuti nsombazi zinkakhala nthawi yaitali ndithu.