Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi zipembedzo zonse zimakondweretsa Mulungu?

N’kutheka kuti munamvapo nkhani zosonyeza zinthu zoipa zimene zimachitika m’dzina la chipembedzo. Mwina munamva nkhani zimenezi pa wailesi kapena munawerenga m’nyuzipepala. Zimenezi zikusonyeza kuti si zipembedzo zonse zimene zimakondweretsa Mulungu. (Mateyu 7:15) Izitu ndi umboni wakuti anthu ambiri asocheretsedwa.—Werengani 1 Yohane 5:19.

Komabe, Mulungu amachita chidwi ndi anthu amene amafunitsitsa kuchita zabwino komanso kumulambira m’njira imene iye amafuna. (Yohane 4:23) Mulungu akuthandiza anthu amenewa kuti aphunzire zolondola kudzera m’Mawu ake, Baibulo.—Werengani 1 Timoteyo 2:3-5.

Kodi mungadziwe bwanji chipembedzo choona?

Yehova Mulungu akuphunzitsa choonadi anthu omwe poyamba anali m’zipembedzo zosiyanasiyana ndipo akuthandiza anthuwa kuti akhale ogwirizana komanso okondana. (Mika 4:2, 3) Choncho, chizindikiro china cha chipembedzo choona ndi choti anthu ake amakondana.—Werengani Yohane 13:35.

Yehova Mulungu akuphunzitsa choonadi anthu osiyanasiyana ndipo akuthandiza anthuwa kuti akhale ogwirizana.—Salimo 133:1

Zinthu zimene anthu a m’chipembedzo choona amakhulupirira zimachokera m’Baibulo. Anthuwa amayesetsa kutsatira zimene amaphunzira m’Baibulo pa moyo wawo. (2 Timoteyo 3:16) Iwo amauza anthu dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Ndipo amathandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto padzikoli. (Danieli 2:44) Iwo amatengera chitsanzo cha Yesu ndipo ‘amaonetsa kuwala’ pochitira zabwino anthu. (Mateyu 5:16) Akhristu oona amadziwikanso chifukwa amapita kunyumba za anthu n’kumakawauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Werengani Mateyu 24:14; Machitidwe 5:42; 20:20.